Nyimbo ya Solomo 7:1-13

7  “Mapazi ako akukongola kwambiri munsapato zako,+ iwe mwana wamkazi+ wodzipereka. Ntchafu zako n’zoumbidwa bwino ngati zinthu zokongoletsera,+ ngati ntchito ya manja a munthu waluso.  Mchombo wako uli ngati mbale yozungulira. Vinyo wosakaniza+ asasowepo. Mimba yako ili ngati mulu wa tirigu, wotchingidwa ndi maluwa.+  Mabere ako awiri ali ngati ana awiri aang’ono, ngati ana amapasa a insa yaikazi.+  Khosi lako+ lili ngati nsanja ya mnyanga wa njovu. Maso ako+ ali ngati maiwe a ku Hesiboni,+ amene ali pafupi ndi chipata cha Bati-rabimu. Mphuno yako ili ngati nsanja ya Lebanoni, imene inayang’ana cha ku Damasiko.  Mutu wako ndi wokwezeka ngati Karimeli.+ Tsitsi+ la m’mutu mwako lili ngati ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira,+ ndipo mfumu yatengeka nalo tsitsi lako lalitalilo.+  Iwe mtsikana wokondedwa, ndiwe wokongola, ndipo ndiwe wosangalatsa kuposa zinthu zina zonse zosangalatsa mtima.+  Msinkhu wako uli ngati mtengo wa kanjedza,*+ ndipo mabere ako+ ali ngati zipatso zake.  Ine ndinati, ‘Ndikwera mtengo wa kanjedza kuti ndikathyole nthambi zake zokhala ndi zipatso.’+ Mabere ako akhale ngati zipatso za mpesa, ndipo mpweya wa m’kamwa mwako ununkhire ngati maapozi.  M’kamwa mwako mukhale ngati vinyo wabwino kwambiri+ amene amatsetserekera kukhosi kwa wokondedwa wanga mwamyaa,+ amene amayenderera pang’onopang’ono pamilomo ya anthu amene akugona.” 10  “Wachikondi wangayo, ine ndine wake,+ ndipo iye akulakalaka ineyo.+ 11  Bwera wachikondi wanga. Tiye tipite kumunda.+ Tiye tikakhale pakati pa mitengo ya maluwa ofiirira.+ 12  Tiye tilawirire m’mawa tipite kuminda ya mpesa. Tikaone ngati mitengo ya mpesa yaphukira,+ ngati yatuluka maluwa,+ ndiponso ngati mitengo ya makangaza yachita maluwa.+ Kumeneko ndikakusonyeza chikondi changa.+ 13  Zipatso za mandereki*+ zikununkhira, ndipo pafupi ndi makomo olowera kunyumba zathu pali zipatso zosiyanasiyana zokoma kwambiri.+ Ndakusungira zipatso zatsopano ndi zakale zomwe, iwe wachikondi wanga.

Mawu a M'munsi

Umenewu ndi mtundu wa kanjedza amene amamera ku Palesitina.
“Mandereki” ndi chitsamba cha m’gulu la mbatata, chimene chimabereka zipatso.