Miyambo 30:1-33
30 Nawa mawu a Aguri mwana wa Yake, mwamuna wamphamvu. Mawuwa anali uthenga wamphamvu+ womwe iye analankhula ndi Itiyeli, ndi Itiyeli ndiponso Ukali, kuti:
2 Ine ndine wopanda nzeru kuposa munthu wina aliyense,+ ndipo sindimvetsa zinthu monga mmene anthu onse amamvetsetsera.+
3 Inetu ndilibe nzeru,+ ndipo sindidziwa nzeru zimene zili ndi Woyera Koposa.+
4 Ndani amene anakwerapo kumwamba n’kubwerako?+ Ndani anasonkhanitsapo mphepo m’manja mwake?+ Ndani anamangapo madzi munsalu?+ Ndani anaika malekezero onse a dziko lapansi?+ Dzina lake ndani?+ Nanga mwana wake dzina lake ndani? Ndiuzeni ngati mukudziwa.+
5 Mawu alionse a Mulungu ndi oyera.+ Iye ndi chishango kwa onse othawira kwa iye.+
6 Usawonjezere kanthu pa mawu ake+ kuti angakudzudzule ndiponso kuti ungakhale wabodza.+
7 Ndikukupemphani zinthu ziwiri.+ Musandikanize ndisanafe.+
8 Zachinyengo ndi mawu onama muwaike kutali ndi ine.+ Musandipatse umphawi kapena chuma.+ Ndidye chakudya chimene ndikufunika kudya,+
9 kuti ndisakhute kwambiri n’kukukanani+ kuti: “Kodi Yehova ndani?”+ ndiponso kuti ndisasauke n’kukaba ndi kunyozetsa dzina la Mulungu wanga.+
10 Usanenere wantchito zoipa kwa mbuye wake,+ kuti angakutemberere ndiponso kuti ungakhale ndi mlandu.+
11 Pali m’badwo umene umatemberera ngakhale abambo awo ndiponso umene sudalitsa ngakhale amayi awo.+
12 Pali m’badwo umene umadziona kuti ndi woyera,+ koma sunasambe kuti uchotse ndowe zake.+
13 Pali m’badwo umene maso ake ali pamwamba kwambiri, ndiponso umene maso ake owala ali odzikweza.+
14 Pali m’badwo umene mano ake ali ngati malupanga ndiponso umene nsagwada zake zili ngati mipeni yophera nyama,+ kuti m’badwowo udye osautsidwa onse a padziko lapansi ndiponso anthu osauka pakati pa anthu.+
15 Misundu* ili ndi ana aakazi awiri amene amafuula kuti: “Tipatseni! Tipatseni!” Pali zinthu zitatu zimene sizikhuta ndiponso zinthu zinayi zimene sizinena kuti: “Ndakhuta!” Zinthuzo ndi izi:
16 Manda,+ mimba yosabereka,+ nthaka imene sikhuta madzi,+ ndiponso moto+ umene sunena kuti: “Ndakhuta!”+
17 Diso limene limanyoza bambo ake ndiponso limene silimvera mayi ake,+ akhwangwala a kuchigwa* adzalikolowola ndipo ana a chiwombankhanga adzalidya.
18 Pali zinthu zitatu zimene n’zodabwitsa kwambiri kwa ine, ndiponso zinthu zinayi zimene sindizimvetsa. Zinthuzo ndi izi:
19 Njira ya chiwombankhanga m’mlengalenga, njira ya njoka pamwala, njira ya ngalawa pakatikati pa nyanja,+ ndiponso njira ya mwamuna ndi mtsikana.+
20 Nayi njira ya mkazi wachigololo: Iye amadya n’kupukuta pakamwa pake ndipo amanena kuti: “Sindinachite cholakwa chilichonse.”+
21 Pali zinthu zitatu zimene zimagwedeza dziko lapansi ndiponso zinthu zinayi zimene dziko lapansi silitha kuzipirira. Zinthuzo ndi izi:
22 Kapolo akamalamulira monga mfumu,+ munthu wopusa akakhuta,+
23 mkazi wodedwa akakwatiwa,+ ndiponso mtsikana wantchito akatenga malo a mbuye wake wamkazi.+
24 Pali zinthu zinayi zomwe ndi zing’onozing’ono kwambiri padziko lapansi koma n’zanzeru mwachibadwa:+
25 Nyerere si zamphamvu,+ koma zimasonkhanitsa chakudya chawo m’chilimwe.+
26 Mbira+ si nyama zamphamvu koma zimamanga nyumba zawo pathanthwe.+
27 Dzombe+ lilibe mfumu koma limauluka lonse litagawikana m’magulumagulu.+
28 Nalimata*+ amagwira zinthu ndi manja ake ndipo amapezeka m’nyumba yaikulu yachifumu.
29 Pali zinthu zitatu zimene zimayenda molemekezeka ndiponso zinthu zinayi zimene zimayenda monyadira. Zinthuzo ndi izi:
30 Mkango, umene ndi wamphamvu kwambiri panyama zonse zakutchire ndiponso umene suopa chilichonse n’kubwerera m’mbuyo,+
31 galu wosaka kapena mbuzi yamphongo, ndiponso mfumu imene ikutsogolera asilikali ake.+
32 Ngati wachita zinthu zopusa n’kudzikweza,+ ndiponso ngati watsimikiza mtima wako kuti uchite zimenezo, gwira pakamwa pako.+
33 Pakuti mkaka ukaukhutchumula umatulutsa mafuta, mphuno ukaifinya imatulutsa magazi, ndipo kutulutsa mkwiyo kumayambitsa mkangano.+
Mawu a M'munsi
^ “Msundu” ndi mtundu wa nyongolotsi zimene zimakhala m’madzi ndipo zimaluma anthu kapena zinyama n’kumayamwa magazi.
^ “Nalimata” ndi kabuluzi kakang’ono komwe kamakonda kukhala m’nyumba, koonekera matumbo.