Miyambo 26:1-28
26 Monga chipale chofewa m’chilimwe ndiponso mvula pa nthawi yokolola,+ momwemonso ulemerero suyenerera munthu wopusa.+
2 Mbalame imakhala ndi chifukwa chothawira, ndiponso namzeze* amakhala ndi chifukwa choulukira. Momwemonso temberero silibwera popanda chifukwa chenicheni.+
3 Chikwapu n’cha hatchi,+ zingwe n’za pakamwa pa bulu,+ ndipo ndodo ndi yokwapulira msana wa anthu opusa.+
4 Usayankhe aliyense wopusa mogwirizana ndi uchitsiru wake, kuti iweyo usafanane naye.+
5 Uzimuyankha wopusa mogwirizana ndi uchitsiru wake, kuti asadzione ngati wanzeru m’maso mwake.+
6 Munthu amene amakankhira nkhani m’manja mwa wopusa ali ngati munthu wopundula mapazi ake, ndiponso ngati munthu amene amamwa chiwawa.+
7 Mwambi wa m’kamwa mwa anthu opusa uli ngati munthu wa miyendo yolumala amene wasenza madzi.+
8 Munthu amene amapereka ulemerero kwa munthu wopusa ali ngati munthu wobisa mwala pamulu wa miyala.+
9 Mwambi wa m’kamwa mwa anthu opusa uli ngati chitsamba chaminga m’manja mwa munthu woledzera.+
10 Wolemba ntchito munthu wopusa kapena munthu wongodutsa m’njira, ali ngati woponya muvi ndi uta amene amangolasa chilichonse.+
11 Monga galu amene wabwerera ku masanzi ake, wopusa amabwereza uchitsiru wake.+
12 Kodi waona munthu wodziona ngati wanzeru m’maso mwake?+ Munthu wopusa ali ndi chiyembekezo chachikulu+ kuposa iyeyo.
13 Waulesi amati: “Panjira pali mkango wamphamvu. M’mabwalo a mzinda mukuyendayenda mkango.”+
14 Chitseko chimazungulira pomwe anachimangirira, ndipo waulesi amangotembenukatembenuka pabedi pake.+
15 Munthu waulesi amapisa dzanja lake m’mbale yodyera, koma amalephera kulibweretsa pakamwa pake chifukwa amaona kuti n’zotopetsa kwambiri.+
16 Waulesi amadziona kuti ndi wanzeru kwambiri m’maso mwake+ kuposa anthu 7 oyankha zanzeru.
17 Munthu wongodutsa amene amalowerera mkangano womwe si wake n’kukwiya nawo, ali ngati munthu wogwira makutu a galu.+
18 Monga munthu wamisala amene akuponya zida ndiponso mivi yamoto+ yakupha,
19 ndi mmenenso alili munthu amene amapusitsa mnzake, n’kunena kuti: “Inetu ndimangochita zocheza.”+
20 Popanda nkhuni moto umazima, ndipo popanda munthu wonenera anzake zoipa mikangano imazilala.+
21 Monga mmene amakhalira makala pamoto wonyeka ndiponso nkhuni pamoto woyaka, ndi mmenenso amakhalira munthu wokonda kuyambana ndi anthu pokolezera mikangano.+
22 Mawu a munthu wonenera ena zoipa ali ngati zinthu zofunika kuzimeza msangamsanga, zimene zimatsikira mkatikati mwa mimba.+
23 Milomo yonena zabwino mwachiphamaso koma mumtima muli zoipa, ili ngati siliva wokutira phale.+
24 Munthu wodana nawe amadzibisa ndi milomo yake, koma mkati mwake mumakhala chinyengo.+
25 Ngakhale azilankhula mawu okoma,+ usam’khulupirire+ chifukwa mumtima mwake muli zinthu 7 zonyansa.+
26 Chidani chimaphimbidwa ndi chinyengo. Zoipa zake zidzaululika mumpingo.+
27 Amene akukumba dzenje adzagweramo yekha,+ ndipo amene akugubuduza mwala udzabwerera kwa iye.+
28 Lilime lonama limadana ndi amene lam’pweteka,+ ndipo pakamwa polankhula zabwino mokokomeza pamabweretsa chiwonongeko.+
Mawu a M'munsi
^ Mbalame imeneyi ena amati “kaluweluwe” kapena “kamembe.”