Miyambo 21:1-31
21 Mtima wa mfumu uli ngati mitsinje yamadzi m’dzanja la Yehova.+ Amautembenuzira kulikonse kumene iye akufuna.+
2 Njira iliyonse ya munthu imaoneka yowongoka m’maganizo mwake,+ koma Yehova amafufuza mitima.+
3 Kuchita zinthu zoyenera ndi zachilungamo kumamusangalatsa kwambiri Yehova, kuposa kupereka nsembe.+
4 Maso odzikweza ndi mtima wodzikuza+ ndizo nyale ya anthu oipa, ndipo zimenezi ndi tchimo.+
5 Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira,+ koma aliyense wopupuluma, ndithu adzasauka.+
6 Kupeza chuma pogwiritsa ntchito lilime lonama kuli ngati nkhungu imene imachoka mofulumira.+ Anthu ochita zinthu mwa njira imeneyi akufunafuna imfa.+
7 Kulanda zinthu za ena kumene anthu oipa amachita n’kumene kudzawawononge,+ chifukwa akana kuchita chilungamo.+
8 Njira ya mlendo imakhala yokhota,+ koma munthu woyera amachita zowongoka.+
9 Kuli bwino kukhala pakona ya denga la nyumba,+ kusiyana ndi kukhala m’nyumba limodzi ndi mkazi wolongolola.+
10 Moyo wa munthu woipa umalakalaka zoipa,+ ndipo iye akaona mnzake samumvera chisoni.+
11 Mwa kulipiritsa munthu wonyoza, wosadziwa zinthu amakhala wanzeru.+ Munthu wanzeru akapatsidwa malangizo, amadziwa zinthu.+
12 Mulungu wolungama amayang’ana nyumba ya munthu woipa,+ ndipo anthu oipa amawagwetsa kuti akumane ndi tsoka.+
13 Aliyense wotseka khutu lake kuti asamve kudandaula kwa munthu wonyozeka,+ nayenso adzaitana koma sadzayankhidwa.+
14 Mphatso yoperekedwa mobisa imathetsa mkwiyo,+ ndipo chiphuphu chopereka mobisa chimathetsa+ ukali waukulu.
15 Wolungama amasangalala akamachita chilungamo,+ koma anthu ochita zopweteka ena adzakumana ndi zoipa.+
16 Munthu wochoka pa njira yochita zinthu mozindikira,+ adzapumula mumpingo wa anthu akufa.+
17 Wokonda zosangalatsa adzakhala munthu wosauka.+ Wokonda vinyo ndi mafuta sadzapeza chuma.+
18 Munthu woipa ndiye dipo la wolungama,+ ndipo munthu wochita zachinyengo amalowa m’malo mwa anthu owongoka mtima.+
19 Kuli bwino kukhala m’chipululu kusiyana ndi kukhala mokhumudwa ndi mkazi wolongolola.+
20 Chuma chosiririka ndiponso mafuta zimakhala pamalo a munthu wanzeru,+ koma wopusa amazimeza.+
21 Amene akufunafuna chilungamo+ ndiponso kukoma mtima kosatha adzapeza moyo, chilungamo ndi ulemerero.+
22 Wanzeru amakwera mzinda wa anthu amphamvu, kuti athetse mphamvu imene mzindawo umadalira.+
23 Wosunga pakamwa pake ndiponso lilime lake akuteteza moyo wake ku masautso.+
24 Munthu amene amadzikuza akapsa mtima, amatchedwa wodzikuza, wonyada ndi wodzitama.+
25 Zolakalaka za munthu waulesi zidzamupha, chifukwa manja ake amakana kugwira ntchito.+
26 Tsiku lonse amaoneka kuti akulakalaka kwambiri chinachake, koma wolungama amapatsa ndipo saumira chilichonse.+
27 Nsembe ya anthu oipa ndi yonyansa.+ Ndiye kuli bwanji munthu akaiperekera limodzi ndi makhalidwe otayirira?+
28 Mboni yonama idzawonongedwa,+ koma munthu amene amamvetsera adzalankhula kwamuyaya.+
29 Munthu woipa amakhala ndi nkhope yamwano,+ koma wowongoka mtima ndi amene njira zake zidzakhazikike.+
30 Palibe nzeru kapena kuzindikira kulikonse, kapena malangizo alionse otsutsana ndi Yehova.+
31 Hatchi* anaikonzera tsiku la nkhondo,+ koma Yehova ndiye amapulumutsa.+
Mawu a M'munsi
^ Ena amati “hosi” kapena “kavalo.”