Mateyu 24:1-51
24 Tsopano Yesu anayamba ulendo kuchoka kukachisiko. Kenako ophunzira ake anabwera pafupi naye kuti amuonetse nyumba za pakachisipo.+
2 Koma iye anawayankha kuti: “Kodi simukuziona zinthu zonsezi? Ndithu ndikukuuzani, Pano sipadzatsala mwala uliwonse pamwamba pa mwala unzake umene sudzagwetsedwa.”+
3 Atakhala pansi m’phiri la Maolivi, ophunzira anafika kwa iye mwamseri ndi kunena kuti: “Tiuzeni, Kodi zinthu zimenezi zidzachitika liti, ndipo chizindikiro cha kukhalapo* kwanu+ ndi cha mapeto a nthawi* ino chidzakhala chiyani?”+
4 Poyankha Yesu ananena kuti: “Samalani kuti munthu asakusocheretseni,+
5 chifukwa ambiri adzabwera m’dzina langa ndi kunena kuti, ‘Khristu uja ndine,’ ndipo adzasocheretsa anthu ambiri.+
6 Mudzamva phokoso la nkhondo ndi mbiri za nkhondo. Izitu zisadzakuchititseni mantha. Pakuti zimenezi ziyenera kuchitika ndithu, koma mapeto adzakhala asanafikebe.+
7 “Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina,+ ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina.+ Kudzakhala njala+ ndi zivomezi+ m’malo osiyanasiyana.
8 Zonsezi ndi chiyambi cha masautso, ngati mmene zimayambira zowawa za pobereka.
9 “Kenako anthu adzakuperekani ku chisautso+ ndipo adzakuphani.+ Mitundu yonse idzadana nanu+ chifukwa cha dzina langa.+
10 Komanso, pa nthawiyo anthu ambiri adzapunthwa+ ndipo adzaperekana ndi kudana.+
11 Kudzafika aneneri ambiri onyenga+ ndipo adzasocheretsa anthu ambiri.+
12 Chifukwa cha kuwonjezeka kwa kusamvera malamulo,+ chikondi cha anthu ambiri chidzazirala.+
13 Koma amene adzapirire+ mpaka pa mapeto, ndiye amene adzapulumuke.+
14 Uthenga wabwino+ uwu wa ufumu+ udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse,+ kenako mapeto+ adzafika.
15 “Choncho, mukadzaona chinthu chonyansa+ chowononga chimene chinanenedwa kudzera mwa mneneri Danieli chitaimirira m’malo oyera,+ (wowerenga adzazindikire,)
16 amene ali mu Yudeya adzayambe kuthawira+ kumapiri.
17 Munthu amene ali padenga la nyumba asadzatsike kukatenga katundu m’nyumba mwake.
18 Munthu amene ali m’munda asadzabwerere kunyumba kukatenga malaya ake akunja.
19 Tsoka kwa akazi apakati ndi oyamwitsa ana m’masiku amenewo!+
20 Pitirizani kupemphera kuti musadzathawe m’nyengo ya chisanu kapena pa tsiku la sabata.
21 Pakuti pa nthawiyo kudzakhala chisautso chachikulu+ chimene sichinachitikepo kuchokera pa chiyambi cha dziko mpaka tsopano,+ ndipo sichidzachitikanso.
22 Kunena zoona, masikuwo akanapanda kufupikitsidwa, palibe amene akanapulumuka. Koma chifukwa cha osankhidwawo,+ masikuwo adzafupikitsidwa.+
23 “Chotero munthu akadzakuuzani kuti, ‘Onani! Khristu uja ali kuno,’+ kapena, ‘Ali uko!’ musadzakhulupirire zimenezo.+
24 Pakuti kudzafika onamizira kukhala Khristu+ ndi aneneri onyenga,+ ndipo adzachita zizindikiro zamphamvu+ ndiponso zodabwitsa, kuti ngati n’kotheka, adzasocheretse ngakhale osankhidwawo.+
25 Onani! Ine ndakuchenjezeranitu.+
26 Chotero anthu akadzakuuzani kuti, ‘Taonani! Ali m’chipululu,’ musadzapiteko. Akadzati, ‘Taonani! Ali m’zipinda zamkati,’ musadzakhulupirire zimenezo.+
27 Pakuti mmene mphezi+ imang’animira kuchokera kum’mawa, ndi kuwala mpaka kumadzulo, zidzakhalanso choncho ndi kukhalapo kwa Mwana wa munthu.+
28 Kulikonseko kumene kuli thupi lakufa, ziwombankhanga+ zimasonkhana komweko.+
29 “Chisautso cha masiku amenewo chikadzangotha, dzuwa lidzachita mdima+ ndipo mwezi+ sudzapereka kuwala kwake. Nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndipo mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka.+
30 Pamenepo chizindikiro cha Mwana wa munthu+ chidzaonekera kumwamba. Ndiyeno mafuko onse a padziko lapansi adzadziguguda pachifuwa chifukwa cha chisoni,+ ndipo adzaona Mwana wa munthu akubwera pamitambo ya kumwamba ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.+
31 Iye adzatumiza angelo ake ndi kulira kwamphamvu kwa lipenga,+ ndipo adzasonkhanitsa osankhidwa ake+ kuchokera kumphepo zinayi,+ kuchokera kumalekezero a m’mlengalenga mpaka kumalekezero ena.
32 “Tsopano phunzirani mfundo imeneyi pa fanizo ili la mkuyu: Nthambi yake yanthete ikaphuka ndi kuchita masamba, mumadziwa kuti dzinja lili pafupi.+
33 Inunso chimodzimodzi, mukadzaona zinthu zonsezi, mudzadziwe kuti iye ali pafupi, ali pakhomo penipeni.+
34 Ndithu ndikukuuzani kuti m’badwo uwu+ sudzatha wonse kuchoka kufikira zinthu zonsezi zitachitika.
35 Kumwamba ndi dziko lapansi zidzachoka,+ koma mawu anga sadzachoka ayi.+
36 “Kunena za tsikulo ndi ola lake,+ palibe amene akudziwa, ngakhale angelo akumwamba kapenanso Mwana, koma Atate yekha.+
37 Pakuti monga mmene analili masiku a Nowa,+ ndi mmenenso kukhalapo kwa Mwana wa munthu kudzakhalire.+
38 M’masiku amenewo chigumula chisanafike, anthu anali kudya ndi kumwa. Amuna anali kukwatira ndipo akazi anali kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa+ analowa m’chingalawa.+
39 Anthu ananyalanyaza zimene zinali kuchitika mpaka chigumula chinafika n’kuwaseseratu onsewo.+ Zidzateronso ndi kukhalapo kwa Mwana wa munthu.
40 Pa nthawiyo, amuna awiri adzakhala ali m’munda, wina adzatengedwa ndipo winayo adzasiyidwa.
41 Akazi awiri adzakhala akupera pamphero+ wina adzatengedwa ndipo winayo adzasiyidwa.+
42 Chotero khalanibe maso chifukwa simukudziwa tsiku limene Ambuye wanu adzabwere.+
43 “Koma dziwani ichi: Ngati mwininyumba angadziwe nthawi yobwera mbala,+ angakhale maso ndipo sangalole kuti mbala zithyole ndi kulowa m’nyumba mwake.
44 Pa chifukwa chimenechi, nanunso khalani okonzeka,+ chifukwa pa ola limene simukuliganizira, Mwana wa munthu adzabwera.
45 “Ndani kwenikweni amene ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru+ amene mbuye wake anamuika kuti aziyang’anira antchito ake apakhomo, ndi kuwapatsa chakudya pa nthawi yoyenera?+
46 Kapolo ameneyu adzakhala wodala+ ngati mbuye wake pobwera adzam’peza akuchita zimenezo!
47 Ndithu ndikukuuzani, Adzamuika kuti aziyang’anira zinthu zake zonse.+
48 “Koma ngati kapolo woipayo anganene mumtima mwake+ kuti, ‘Mbuye wanga akuchedwa,’+
49 n’kuyamba kumenya akapolo anzake ndi kudya komanso kumwa limodzi ndi zidakwa zenizeni,
50 mbuye wa kapoloyo adzabwera pa tsiku limene iye sakuyembekezera ndi pa ola+ limene sakulidziwa.
51 Pamenepo adzam’patsa chilango choopsa+ ndipo adzam’ponya kumene kuli anthu onyenga. Kumeneko ndiye kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.+