Mateyu 19:1-30
19 Tsopano Yesu atatsiriza mawu amenewa, anachoka ku Galileya ndi kubwera kumadera a kumalire kwa Yudeya kutsidya la Yorodano.+
2 Khamu lalikulu la anthu linam’tsatira, ndipo iye anawachiritsa kumeneko.+
3 Afarisi anabwera kwa iye, ndipo pofuna kumuyesa anamufunsa kuti: “Kodi n’kololeka kuti mwamuna asiye mkazi wake pa chifukwa chilichonse?”+
4 Yesu anayankha kuti: “Kodi simunawerenge kuti amene analenga anthu pa chiyambi pomwe anawalenga mwamuna ndi mkazi+
5 n’kunena kuti, ‘Pa chifukwa chimenechi mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake+ n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi’?+
6 Chotero salinso awiri, koma thupi limodzi. Choncho chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.”+
7 Iwo anamufunsa kuti: “Nanga n’chifukwa chiyani Mose analamula kuti mwamuna azipereka kalata yothetsa ukwati kwa mkazi ndi kum’siya?”+
8 Iye anayankha kuti: “Chifukwa cha kuuma mtima kwanu,+ Mose anakulolezani kuti muzithetsa ukwati, koma kuyambira pa chiyambi sizinali choncho ayi.+
9 Ine ndikukuuzani kuti aliyense wosiya mkazi wake n’kukwatira wina wachita chigololo, kupatulapo ngati wamusiya chifukwa cha dama.”*+
10 Kenako ophunzira ake anati: “Ngati zili choncho kwa munthu ndi mkazi wake, ndiyetu ndi bwino kusakwatira.”+
11 Iye anawauza kuti: “Si onse amene angathe kuchita zimenezi, koma okhawo amene ali ndi mphatso.+
12 Pakuti ena sakwatira chifukwa chakuti anabadwa choncho kuchokera m’mimba mwa mayi awo,+ ndipo ena chifukwa chakuti anafulidwa ndi anthu. Koma pali ena amene safuna kukwatira chifukwa cha ufumu wakumwamba. Amene angathe kuchita zimenezi achite.”+
13 Kenako anthu anam’bweretsera ana aang’ono kuti awaike manja ndi kuwapempherera, koma ophunzirawo anawakalipira.+
14 Koma Yesu anawauza kuti: “Alekeni anawo, ndipo musawaletse kubwera kwa ine, pakuti ufumu wakumwamba ndi wa anthu amene ali ngati ana amenewa.”+
15 Pamenepo anaika manja ake pa anawo, kenako anachoka kumeneko.+
16 Tsopano munthu wina anafika kwa iye ndi kumufunsa kuti: “Mphunzitsi, n’chiyani chabwino chimene ndiyenera kuchita kuti ndikapeze moyo wosatha?”+
17 Iye anamuyankha kuti: “N’chifukwa chiyani ukundifunsa chimene chili chabwino? Pali Mmodzi yekha amene ali wabwino.+ Chotero ngati ukufuna kukapeza moyo, uzisunga malamulo nthawi zonse.”+
18 Koma iye anafunsa Yesu kuti: “Malamulo ati?”+ Yesu anati: “Akuti, Usaphe+ munthu,* Usachite chigololo,+ Usabe,+ Usapereke umboni wonamizira mnzako.+
19 Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako,+ komanso lakuti, Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.”+
20 Mnyamatayo anayankha Yesu kuti: “Ndakhala ndikutsatira zonsezi, n’chiyaninso chimene ndikupereweza?”
21 Yesu anamuuza kuti: “Ngati ukufuna kukhala wangwiro, pita kagulitse katundu wako ndipo ndalama zake upatse osauka. Ukatero udzakhala ndi chuma kumwamba,+ ndiyeno ubwere udzakhale wotsatira wanga.”+
22 Mnyamata uja atamva mawu amenewa, anachoka ali wachisoni, chifukwa anali ndi katundu wambiri.+
23 Koma Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ndithu ndikukuuzani, zidzakhalatu zovuta kuti munthu wolemera adzalowe mu ufumu wakumwamba.+
24 Ndiponso ndikukuuzani kuti, N’chapafupi kuti ngamila ilowe padiso la singano kusiyana n’kuti munthu wolemera alowe mu ufumu wa Mulungu.”+
25 Ophunzirawo atamva zimenezi, anadabwa kwambiri ndipo anati: “Ndiye angapulumuke ndani?”+
26 Yesu anawayang’anitsitsa n’kunena kuti: “Kwa anthu zimenezi n’zosathekadi, koma zinthu zonse n’zotheka kwa Mulungu.”+
27 Pamenepo Petulo ananena kuti: “Taonani! Ife tasiya zinthu zonse ndi kukutsatirani, kodi tidzapeza chiyani?”+
28 Yesu anawayankha kuti: “Ndithu ndikukuuzani, Pa nthawi ya kulenganso zinthu, pamene Mwana wa munthu adzakhala pampando wachifumu waulemerero, inu amene mwatsatira ine mudzakhalanso m’mipando yachifumu 12, kuweruza mafuko 12 a Isiraeli.+
29 Aliyense amene wasiya nyumba, abale, alongo, abambo, amayi, ana kapena minda chifukwa cha dzina langa adzalandira zochuluka kwambiri kuposa zimenezi, ndipo adzapeza moyo wosatha.+
30 “Koma ambiri amene ali oyamba adzakhala omaliza, ndipo omaliza adzakhala oyamba.+