Salimo 90:1-17
Pemphero la Mose, munthu wa Mulungu woona.+
90 Inu Yehova, ndinudi malo athu okhalamo+Ku mibadwomibadwo.+
2 Mapiri asanabadwe,+Kapena musanakhazikitse dziko lapansi+ ndi malo okhalapo anthu,*+Inu ndinu Mulungu kuyambira kalekale mpaka kalekale.+
3 Mumabwezera munthu kufumbi,+Ndipo mumanena kuti: “Bwererani kufumbi, inu ana a anthu.”+
4 Pakuti kwa inu zaka 1,000 zili ngati dzulo lapitali,+Ndiponso zili ngati ulonda umodzi wa usiku.*+
5 Mwawawonongeratu,+ ndipo amangozimiririka ngati maloto.+M’mawa amakhala ngati msipu wobiriwira umene watsitsimuka.+
6 Msipuwo umaphuka ndi kutsitsimuka m’mawa.+Madzulo umafota kenako umauma.+
7 Pakuti ife tatha chifukwa cha mkwiyo wanu,+Ndipo tasokonezeka chifukwa cha kupsa mtima kwanu.+
8 Zolakwa zathu mwaziika patsogolo panu,+Ndipo machimo athu obisika* ali patsogolo pa nkhope yanu yowala.+
9 Pakuti masiku athu onse atha chifukwa cha mkwiyo wanu.+Zaka zathu zafika kumapeto ngati mpweya wotuluka m’mphuno pousa moyo.+
10 Masiku a moyo wathu amangokwana zaka 70,+Ndipo ngati tili ndi mphamvu yapadera amakwana zaka 80.+Koma ngakhale zili choncho, amangodzaza ndi mavuto ndi zopweteka.+Pakuti masiku amene timakhala ndi moyo amatha mwamsanga ndipo timachoka mofulumira.+
11 Ndani angadziwe kukula kwa ukali wanu,+Ndi kukula kwa mkwiyo wanu kumene kumafanana ndi ulemu umene muyenera kulandira?+
12 Tisonyezeni mmene tingawerengere masiku athu+Kuti tikhale ndi mtima wanzeru.+
13 Bwererani kwa ife, inu Yehova!+ Kodi mudzatenga nthawi yaitali bwanji musanabwerere kwa ife?+Timvereni chisoni ife atumiki anu.+
14 M’mawa mutikhutiritse ndi kukoma mtima kwanu kosatha,+Kuti tifuule mokondwera ndi kuti tikhale osangalala masiku onse a moyo wathu.+
15 Tichititseni kusangalala kwa masiku ofanana ndi masiku amene mwatisautsa,+Kwa masiku ofanana ndi zaka zimene taona masoka.+
16 Ntchito zanu zionekere kwa atumiki anu,+Ndipo ulemerero wanu uonekere pa ana awo.+
17 Ubwino wa Yehova Mulungu wathu ukhale pa ife,+Ndipo mukhazikitse ntchito ya manja athu.+Muidalitse ntchito ya manja athu.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti “musanamve zowawa ngati za pobereka pokhazikitsa dziko lapansi.”
^ Zikuoneka kuti usiku anali kuugawa zigawo zitatu za ulonda, kuyambira pamene dzuwa lalowa mpaka kutuluka. Ulonda uliwonse unali pafupifupi maola anayi malinga ndi nyengo ya pachaka.
^ Kapena kuti “machimo amene tinachita mosadziwa.”