Salimo 9:1-20
Kwa wotsogolera nyimbo pa Mutilabeni.* Nyimbo ya Davide.
א [ʼAʹleph]
9 Ndidzakutamandani inu Yehova ndi mtima wanga wonse.+Ndidzalengeza ntchito zanu zonse zodabwitsa.+
2 Ndidzakondwera ndi kusangalala chifukwa cha inu,+Ndidzaimba nyimbo motsagana ndi zipangizo zoimbira, kutamanda dzina lanu, inu Wam’mwambamwamba.+
ב [Behth]
3 Adani anga akabweranso,+Adzapunthwa ndi kuwonongeka pamaso panu,+
4 Chifukwa mwandiweruzira mlandu wanga ndi dandaulo langa.+Mwakhala pampando wachifumu ndipo mukuweruza mwachilungamo.+
ג [Giʹmel]
5 Mwadzudzula anthu a mitundu ina,+ mwawononga oipa.+Dzina lawo mwalifafaniza mpaka kalekale, mwalifafaniza mpaka muyaya.+
6 Kusakaza kwa mdani kwatheratu tsopano,+Mizinda imene mwaifafaniza, nayonso yatheratu.+Dzina la mdani wanu silidzatchulidwanso.+
ה [Heʼ]
7 Koma Yehova adzakhala pampando wachifumu mpaka kalekale,+Adzakhazikitsa mpando wake wachifumu kuti aweruze.+
8 Iye adzaweruza anthu padziko lapansi mwachilungamo.+Adzazenga mlandu mitundu ya anthu moyenerera.+
ו [Waw]
9 Yehova adzakhala malo okwezeka ndiponso achitetezo kwa aliyense woponderezedwa,+Adzakhala malo okwezeka ndiponso achitetezo m’nthawi za masautso.+
10 Anthu odziwa dzina lanu adzakukhulupirirani,+Pakuti simudzasiya ndithu anthu okufunafunani, inu Yehova.+
ז [Zaʹyin]
11 Anthu inu, imbani nyimbo motsagana ndi zipangizo zoimbira, kutamanda Yehova amene akukhala m’Ziyoni.+Fotokozani ntchito zake kwa mitundu ya anthu.+
12 Pofunafuna okhetsa magazi,+ iye adzakumbukira ndithu anthu osautsidwa.+Sadzaiwala ndithu kulira kwawo.+
ח [Chehth]
13 Ndikomereni mtima inu Yehova. Onani mmene anthu odana nane akundisautsira,+Inu Mulungu amene mukundinyamula kundichotsa pazipata za imfa.+
14 Ndichitireni zimenezi kuti ndilengeze ntchito zanu zonse zotamandika+Pazipata+ za mwana wamkazi wa Ziyoni,+Kuti ndikondwere ndi chipulumutso chanu.+
ט [Tehth]
15 Anthu a mitundu ina agwera m’dzenje limene anakumba okha.+Phazi lawo lakodwa mu ukonde+ umene anatchera okha.+
16 Yehova amadziwika ndi ziweruzo zimene amapereka.+Woipa wakodwa mumsampha wa ntchito ya manja ake.+Higayoni.* [Seʹlah.]
י [Yohdh]
17 Anthu oipa+ adzapita ku Manda,+Ngakhalenso anthu onse a mitundu ina amene aiwala Mulungu.+
18 Pakuti waumphawi sadzaiwalidwa nthawi zonse,+Ndiponso chiyembekezo cha ofatsa sichidzatha konse.+
כ [Kaph]
19 Nyamukani, inu Yehova! Munthu asakuposeni mphamvu.+Anthu a mitundu ina aweruzidwe pamaso panu.+
20 Ikani mantha m’mitima yawo, inu Yehova,+Kuti anthu a mitundu ina adziwe kuti iwo ndi anthu ochokera kufumbi.+ [Seʹlah.]
Mawu a M'munsi
^ “Mutilabeni” ndi mawu achiheberi amene tanthauzo lake lenileni silikudziwika. Koma omasulira ena anamasulira mawuwa kuti, “yonena za imfa ya mwana wamwamuna.”
^ “Higayoni” ndi mawu achiheberi amene anali kuwagwiritsa ntchito polemba nyimbo, koma tanthauzo lake lenileni silikudziwika.