Salimo 56:1-13
Kwa wotsogolera nyimbo pa “Nkhunda Yosanena Kanthu” pakati pa okhala kutali. Salimo la Davide. Mikitamu.* Pa nthawi imene Afilisiti anamugwira ku Gati.+
56 Ndikomereni mtima inu Mulungu wanga, chifukwa munthu wopanda pake akufuna kundiwakha ndi pakamwa pake.+Akulimbana nane tsiku lonse ndi kundipondereza.+
2 Tsiku lonse adani anga akufuna kundiwakha ndi pakamwa pawo,+Pakuti anthu ambiri akumenyana nane modzikuza.+
3 Ine ndidzadalira inu, tsiku lililonse limene ndingachite mantha.+
4 Popeza kuti ndine wogwirizana ndi Mulungu, ndidzatamanda mawu ake.+Ine ndimadalira Mulungu, sindidzaopa.+Kodi munthu angandichite chiyani?+
5 Tsiku lonse amasokoneza zolinga zanga.Nthawi zonse amaganiza zondichitira zoipa.+
6 Amandiukira ndi kundibisalira,+Iwo nthawi zonse amaonetsetsa mmene ndikuyendera,+Pamene akundidikirira kuti awononge moyo wanga.+
7 Atayeni chifukwa cha zochita zawo zoipa.+Inu Mulungu, gwetsani mitundu ya anthu mu mkwiyo wanu.+
8 Inu mwalemba za kuthawathawa kwanga.+Sungani misozi yanga m’thumba lanu lachikopa.+Kodi misozi yanga sili m’buku lanu?+
9 Pa nthawi imeneyo adani anga adzabwerera pa tsiku limene ndidzaitana inu.+Ndikudziwa bwino kuti Mulungu ali kumbali yanga.+
10 Popeza kuti ndine wogwirizana ndi Mulungu,+ ndidzatamanda mawu ake.Popeza kuti ndine wogwirizana ndi Yehova, ndidzatamanda mawu ake.+
11 Ine ndimadalira Mulungu. Sindidzaopa.+Kodi munthu wochokera kufumbi angandichite chiyani?+
12 Inu Mulungu, ine ndikuyenera kukwaniritsa malonjezo anga kwa inu.+Ndidzapereka kwa inu nsembe zoyamikira.+
13 Pakuti inu mwalanditsa moyo wanga ku imfa.+Inu mwateteza phazi langa kuti lisapunthwe,+Kuti ndiyendeyende pamaso pa Mulungu m’kuwala kumene kumaunikira anthu amoyo.+