Salimo 37:1-40
Salimo la Davide.
א [ʼAʹleph]
37 Usapse mtima chifukwa cha anthu ochita zoipa.+Usakhumbe kukhala ngati anthu ochita zosalungama.+
2 Pakuti adzafota mwamsanga ngati udzu,+Adzanyala ngati msipu watsopano wobiriwira.+
ב [Behth]
3 Khulupirira Yehova ndipo chita zabwino.+Khala padziko lapansi, ndipo khala wokhulupirika m’zochita zako zonse.+
4 Komanso sangalala mwa Yehova,+Ndipo adzakupatsa zokhumba za mtima wako.+
ג [Giʹmel]
5 Lola kuti Yehova akutsogolere panjira yako,+Umudalire+ ndipo iye adzachitapo kanthu.+
6 Iye adzaonetsa poyera kulungama kwako kuti kuunike ngati kuwala,+Adzaonetsa poyera chilungamo chako kuti chiwale ngati usana.+
ד [Daʹleth]
7 Khala chete pamaso pa Yehova,+Ndipo umuyembekezere ndi mtima wako wonse.+Usapse mtima ndi aliyense amene zinthu zikumuyendera bwino,+Munthu amene akukwaniritsa zolinga zake zoipa.+
ה [Heʼ]
8 Usapse mtima ndipo pewa kukwiya.+Usapse mtima kuti ungachite choipa.+
9 Pakuti ochita zoipa adzaphedwa.+Koma oyembekezera Yehova ndi amene adzalandire dziko lapansi.+
ו [Waw]
10 Patsala kanthawi kochepa, woipa sadzakhalakonso.+Udzayang’ana pamene anali kukhala, ndipo sadzapezekapo.+
11 Koma anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi,+Ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.+
ז [Zaʹyin]
12 Woipa akukonzera chiwembu munthu wolungama,+Ndipo akumukukutira mano.+
13 Koma Yehova adzamuseka,+Pakuti akuona kuti chimaliziro chake chifika.+
ח [Chehth]
14 Oipa asolola lupanga ndipo akunga uta wawo,+Kuti agwetse osautsika ndi osauka,+Kuti aphe anthu amene njira zawo ndi zowongoka.+
15 Lupanga lawo lidzalowa mumtima mwawo,+Ndipo mauta awo adzathyoka.+
ט [Tehth]
16 Zinthu zochepa za munthu wolungama ndi zabwino+Kusiyana ndi zinthu zochuluka za anthu ambiri oipa.+
17 Pakuti manja a anthu oipa adzathyoledwa,+Koma Yehova adzathandiza anthu olungama.+
י [Yohdh]
18 Yehova amadziwa za moyo wa anthu osalakwa,+Ndipo cholowa chawo chidzakhalapo mpaka kalekale.+
19 Pa nthawi yatsoka sadzachita manyazi,+Ndipo pa nthawi ya njala adzakhuta.+
כ [Kaph]
20 Pakuti anthu oipa adzatheratu onse,+Ndipo adani a Yehova adzafanana ndi busa la msipu wobiriwira mochititsa kaso.Iwo adzatha.+ Adzazimiririka ndi kusanduka utsi.+
ל [Laʹmedh]
21 Munthu woipa amakongola zinthu za ena koma osabweza,+Koma wolungama amakomera mtima ena ndipo amapereka mphatso.+
22 Anthu amene Mulungu akuwadalitsa adzalandira dziko lapansi,+Koma amene wawatemberera adzaphedwa.+
מ [Mem]
23 Yehova walimbitsa mapazi a munthu wamphamvu zake,+Ndipo Mulungu amakondwera ndi njira zake.+
24 Ngakhale atapunthwa, sadzagweratu,+Pakuti Yehova wamugwira dzanja.+
נ [Nun]
25 Ndinali mwana, ndipo tsopano ndakula,+Koma sindinaonepo munthu aliyense wolungama atasiyidwa,+Kapena ana ake akupemphapempha chakudya.+
26 Tsiku lililonse amakomera mtima ena ndi kuwakongoza zinthu,+Ndipo ana ake adzalandira madalitso.+
ס [Saʹmekh]
27 Patuka pa choipa ndipo uchite chabwino,+Ukatero udzakhala padziko lapansi mpaka kalekale.+
28 Pakuti Yehova amakonda chilungamo,+Ndipo sadzasiya anthu ake okhulupirika.+
ע [ʽAʹyin]Adzawateteza mpaka kalekale.+Koma ana a anthu oipa adzaphedwa.+
29 Olungama adzalandira dziko lapansi,+Ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.+
פ [Peʼ]
30 Pakamwa pa munthu wolungama pamalankhula zinthu zanzeru,+Ndipo lilime lake limalankhula zinthu zachilungamo.+
31 Chilamulo cha Mulungu wake chili mumtima mwake.+Poyenda mapazi ake sadzaterereka.+
צ [Tsa·dhehʹ]
32 Woipa amalondalonda munthu wolungama,+Ndipo amafuna kuti amuphe.+
33 Koma Yehova sadzasiya wolungama m’manja mwa woipayo,+Ndipo pamene wolungamayo akuweruzidwa, Mulungu sadzamuona monga wolakwa.+
ק [Qohph]
34 Yembekezera Yehova, ndi kusunga njira zake,+Ndipo adzakukweza kuti ulandire dziko lapansi.+Pamene oipa akuphedwa, iwe udzaona.+
ר [Rehsh]
35 Ine ndaona munthu woipa, wolamulira mwankhanza+Zinthu zikumuyendera bwino ngati mtengo waukulu wa masamba obiriwira bwino panthaka yake.+
36 Koma anafa ndipo sanapezekenso.+Ndinamufunafuna ndipo sindinamupeze.+
ש [Shin]
37 Ona munthu wosalakwa ndipo yang’anitsitsa munthu wolungama,+Pakuti tsogolo la munthu ameneyu ndi lamtendere.+
38 Koma anthu onse ochimwa adzafafanizidwa.+M’tsogolo, anthu oipa adzaphedwa.+
ת [Taw]
39 Chipulumutso cha anthu olungama chimachokera kwa Yehova.+Iye ndi malo awo achitetezo champhamvu pa nthawi ya nsautso.+
40 Yehova adzawathandiza ndi kuwapulumutsa.+Adzawapulumutsa kwa anthu oipa ndi kuwalanditsa,+Chifukwa athawira kwa iye.+