Salimo 31:1-24
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.
31 Ndathawira kwa inu Yehova.+Musalole kuti ndichite manyazi.+Ndipulumutseni chifukwa cha chilungamo chanu.+
2 Tcherani khutu lanu kwa ine.+Ndilanditseni mofulumira.+Mukhale thanthwe lolimba kwa ine,+Mukhale nyumba ya mpanda wolimba kuti mundipulumutse.+
3 Pakuti inu ndinu thanthwe langa ndi malo anga achitetezo.+Chifukwa cha dzina lanu+ mudzanditsogolera ndi kundilozera njira.+
4 Mudzandiwonjola mu ukonde umene anditchera,+Pakuti inu ndinu malo anga achitetezo.+
5 Ndikuikiza mzimu* wanga m’manja mwanu.+Mwandiwombola,+ inu Yehova, Mulungu wachoonadi.+
6 Ndimadana ndi olambira mafano opanda pake ndi achabechabe.+Koma ine ndimadalira Yehova.+
7 Ndidzakondwera ndi kusangalala chifukwa cha kukoma mtima kwanu kosatha,+Pakuti mwaona kusautsika kwanga.+Mwadziwa zowawa zimene zandigwera,+
8 Simunandipereke m’manja mwa adani.+Mwapondetsa phazi langa pamalo otakasuka.+
9 Ndikomereni mtima inu Yehova, pakuti ndasautsika kwambiri.+Diso langa lafooka chifukwa cha chisoni,+ chimodzimodzinso moyo wanga ndi m’mimba mwanga.+
10 Chifukwa cha chisoni, moyo wanga watha,+Ndipo chifukwa cha kuusa moyo kwanga, zaka zanga zafika kumapeto.+Chifukwa cha zolakwa zanga, mphamvu zanga zafooka,+Ndipo mafupa anga afooka.+
11 Ndakhala chitonzo+ pamaso pa onse odana nane,+Ndipo kwa anthu oyandikana nawo ndakhala chitonzo chachikulu,+Kwa anthu ondidziwa ndakhala woopsa.+Akandiona ndili panja amandithawa.+
12 Ndaiwalidwa ngati munthu wakufa amene anthu sakumukumbukiranso.+Ndakhala ngati chiwiya chosweka.+
13 Ndamva zinthu zoipa zimene anthu ambiri akunena,+Ndamva zochititsa mantha kuchokera kumbali zonse.+Akasonkhana pamodzi kundichitira upo,+Amakonza chiwembu kuti achotse moyo wanga.+
14 Koma ine chikhulupiriro changa chili mwa inu Yehova.+Ndipo ndikunena kuti: “Inu ndinu Mulungu wanga.”+
15 Moyo wanga uli m’manja mwanu.+Ndilanditseni m’manja mwa adani anga ndi kwa anthu ondisakasaka.+
16 Ndikomereni mtima ine mtumiki wanu.+Ndipulumutseni mwa kukoma mtima kwanu kosatha.+
17 Inu Yehova, musalole kuti ndichite manyazi, pakuti ndaitana pa dzina lanu.+Anthu oipa achite manyazi.+Akhale chete m’Manda.+
18 Milomo yachinyengo isowe chonena,+Milomo imene ikulankhula motsutsana ndi wolungama,+ yosadziletsa pa kudzikweza ndi kunyoza ena.+
19 Ubwino wanu,+ umene mwasungira anthu okuopani ndi wochuluka kwambiri!+Ubwino umenewu mwapereka kwa anthu othawira kwa inu.Mwaupereka kwa iwo, ana a anthu akuona.+
20 Mudzawabisa m’malo otetezeka pafupi ndi inu,+Kuwachotsa pamaso pa anthu amene asonkhana pamodzi kuti awachitire chiwembu.+Mudzawabisa mumsasa wanu kwa anthu ofuna kukangana nawo.+
21 Yehova adalitsike,+Pakuti wandisonyeza modabwitsa kukoma mtima kosatha+ mumzinda wozingidwa ndi adani.+
22 Koma ine nditapanikizika ndinati:+“Ndidzafafanizidwa kuchoka pamaso panu.”+Ndithudi mwamva kuchonderera kwanga pamene ndinali kufuulira kwa inu kupempha thandizo.+
23 Kondani Yehova, inu nonse okhulupirika ake.+Yehova amateteza okhulupirika,+Koma aliyense wodzikuza adzamulanga mowirikiza.+
24 Limbani mtima ndipo muchite zinthu mwamphamvu,+Inu nonse amene mukuyembekezera Yehova.+
Mawu a M'munsi
^ Onani Zakumapeto 4.