Salimo 132:1-18
Nyimbo Yokwerera Kumzinda.
132 Inu Yehova, kumbukirani Davide,+Kumbukirani masautso ake onse.+
2 Kumbukirani kuti analumbira kwa inu Yehova,+Analonjeza kwa Wamphamvu+ wa Yakobo kuti:+
3 “Sindilowa m’nyumba yanga.+Sindigona pabedi langa.+
4 Maso anga saona tulo,+Ndipo sindilola maso anga owala kuwodzera,+
5 Kufikira Yehova nditamupezera nyumba,+Kufikira nditapeza chihema chachikulu cha Wamphamvu wa Yakobo.”+
6 Taonani! Tamva za Likasa* ku Efurata,+Talipeza kunkhalango.+
7 Tiyeni tilowe m’chihema chake chachikulu.+Tiyeni tiwerame pachopondapo mapazi ake.+
8 Nyamukani, inu Yehova, kuti mulowe kumalo anu okhalamo,+Inu pamodzi ndi Likasa+ limene mumasonyezera mphamvu zanu.+
9 Ansembe anu avale chilungamo,+Ndipo okhulupirika anu afuule mosangalala.+
10 Chifukwa cha zimene munalonjeza Davide mtumiki wanu,+Musakane kuona nkhope ya wodzozedwa wanu.+
11 Yehova walumbira kwa Davide,+Ndithudi sadzabweza mawu ake akuti:+“Ndidzaika pampando wako wachifumu+Chipatso cha mimba yako.+
12 Ana ako akadzasunga pangano langa+Ndi zikumbutso zanga zimene ndidzawapatsa,+Ngakhalenso ana awo+Adzakhala pampando wako wachifumu kwamuyaya.”+
13 Yehova wasankha Ziyoni,+Ndipo amafunitsitsa kuti akhale malo ake okhalamo. Iye amati:+
14 “Awa ndi malo anga okhalamo mpaka muyaya.+Ndidzakhala mmenemu, pakuti ndimafunitsitsa kukhala m’malo amenewa.+
15 Ndithu ndidzadalitsa chakudya chake.+Anthu ake osauka ndidzawapatsa chakudya chokwanira.+
16 Ansembe ake ndidzawaveka chipulumutso,+Ndipo anthu ake okhulupirika adzafuula ndithu mokondwera.
17 Ku Ziyoniko ndidzakulitsa nyanga* ya Davide.+Wodzozedwa wanga ndamukonzera nyale.+
18 Adani ake ndidzawaveka manyazi,+Koma ufumu*+ wake udzapita patsogolo.”+