Salimo 129:1-8
Nyimbo Yokwerera Kumzinda.
129 “Andisonyeza chidani mokwanira kuyambira ndili mnyamata,”+Isiraeli anene kuti,+
2 “Andisonyeza chidani mokwanira kuyambira ndili mnyamata,+Koma sanandigonjetse.+
3 Olima ndi ng’ombe andilima pamsana.*+Iwo alima mizere italiitali.”
4 Yehova ndi wolungama.+Iye waduladula zingwe za oipa.+
5 Onse odana ndi Ziyoni,+Adzachita manyazi ndipo adzatembenuka ndi kubwerera okha.+
6 Adzakhala ngati udzu wanthete womera padenga,+Umene umauma asanauzule,+
7 Umene wokolola sanadzaze nawo manja ake,+Ngakhalenso aliyense amene akunyamula mitolo ya zokolola sanadzaze nawo thumba lake la pachifuwa.
8 Anthu odutsa nawonso sananene kuti:“Madalitso a Yehova akhale nanu anthu inu.+Takudalitsani m’dzina la Yehova.”+
Mawu a M'munsi
^ Zikuoneka kuti apa akunena za nkhanza zimene mitundu ina yodana nawo inawachitira.