Salimo 116:1-19
116 Mtima wanga ndi wodzaza ndi chikondi, chifukwa Yehova amamva+Mawu anga ndi madandaulo anga.+
2 Pakuti watchera khutu lake kwa ine,+Ndipo ndidzaitanira pa iye masiku onse a moyo wanga.+
3 Zingwe za imfa zinandizungulira+Ndipo ndinasautsika ngati kuti ndili m’Manda.+Ndinapitiriza kusautsika ndi kukhala wachisoni,+
4 Koma ndinaitana pa dzina la Yehova kuti:+“Inu Yehova, pulumutsani moyo wanga!”+
5 Yehova ndi wachisomo ndi wolungama.+Mulungu wathu amasonyeza chifundo.+
6 Yehova amateteza anthu osadziwa zambiri.+Ndinali wosautsika koma iye anandipulumutsa.+
7 Iwe moyo wanga, bwerera kumalo ako ampumulo,+Pakuti Yehova wakuchitira zinthu zabwino.+
8 Pakuti inu mwapulumutsa moyo wanga ku imfa,+Mwateteza maso anga kuti asakhetse misozi ndiponso phazi langa kuti lisapunthwe.+
9 Ndidzayenda+ pamaso pa Yehova m’dziko la anthu amoyo.+
10 Ndinali ndi chikhulupiriro,+ n’chifukwa chake ndinalankhula.+Ndinali kusautsika kwambiri.
11 Pamene ndinapanikizika ndinati:+“Munthu aliyense ndi wabodza.”+
12 Yehova ndidzamubwezera chiyani+Pa zabwino zonse zimene wandichitira?+
13 Ndidzamwa za m’kapu yachipulumutso chachikulu,+Ndipo ndidzaitana pa dzina la Yehova.+
14 Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova,+Pamaso pa anthu ake onse.
15 M’maso mwa YehovaImfa ya anthu ake okhulupirika ndi nkhani yaikulu.+
16 Inu Yehova,+Inetu ndine mtumiki wanu.+Ndine mtumiki wanu, mwana wa kapolo wanu wamkazi.+Mwamasula zingwe zimene anandimanga nazo.+
17 Ndidzapereka nsembe zoyamikira kwa inu,+Ndipo ndidzaitana pa dzina la Yehova.+
18 Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova,+Ndidzawakwaniritsa pamaso pa anthu ake onse,+
19 M’mabwalo a nyumba ya Yehova,+Pakati pa iwe Yerusalemu.+Tamandani Ya, anthu inu!+