Machitidwe 7:1-60

7  Koma mkulu wa ansembe anati: “Kodi zimenezi n’zoona?”  Sitefano anati: “Amuna inu, abale anga ndi abambo anga, mvetserani! Mulungu waulemerero+ anaonekera kwa kholo lathu Abulahamu pamene anali ku Mesopotamiya, asanakakhale ku Harana.+  Ndipo anamuuza kuti, ‘Tuluka m’dziko lako ndi pakati pa abale ako. Tiye ukalowe m’dziko limene ine ndidzakusonyeza.’+  Pamenepo anasamuka m’dziko la Akasidi ndi kukakhala ku Harana. Kumeneko, pambuyo pa imfa ya bambo ake,+ Mulungu anamuuza kuti asamukire m’dziko lino limene inu mukukhala tsopano.+  Komatu sanam’patse cholowa chilichonse mmenemu ayi, ngakhale kadera kochepetsetsa.+ Koma anamulonjeza kuti adzamupatsa dzikoli monga cholowa chake,+ ndi cha mbewu yake,+ ngakhale kuti pa nthawiyo n’kuti alibe mwana.+  Ndipo Mulungu ananenanso kuti mbewu yake idzakhala alendo+ m’dziko lachilendo,+ ndipo anthu adzawasandutsa akapolo ndi kuwasautsa kwa zaka 400.+  Mulungu anati, ‘Ndidzaweruza mtundu umene adzautumikire monga akapolo,+ pambuyo pake adzatuluka ndi kudzanditumikira m’malo ano.’+  “Anamupatsanso pangano la mdulidwe.+ Chotero anabereka Isaki+ ndi kuchita mdulidwe wake tsiku la 8.+ Isaki naye anabereka Yakobo, Yakobo anabereka mitu ya mabanja 12 ija.+  Mitu ya mabanja ija inachitira nsanje+ Yosefe ndi kumugulitsa ku Iguputo.+ Koma Mulungu anali naye,+ 10  ndipo anamulanditsa m’masautso ake onse. Anamupatsanso chisomo ndi nzeru pamaso pa Farao mfumu ya Iguputo. Ndipo anamuika kuti ayang’anire Iguputo ndi nyumba yonse ya Farao.+ 11  Tsopano munagwa njala yaikulu mu Iguputo ndi mu Kanani monse, inde chisautso chachikulu. Ndipo makolo athuwo sanali kupeza chakudya.+ 12  Koma Yakobo anamva kuti ku Iguputo kuli chakudya,+ ndipo anatuma makolo athu aja kwa nthawi yoyamba.+ 13  Pa ulendo wachiwiri Yosefe anadziulula kwa abale ake,+ ndipo Farao anadziwa za achibale ake onse a Yosefe ndi makolo ake.+ 14  Chotero Yosefe anatumiza anthu ku Kanani kukatenga bambo ake Yakobo ndi achibale ake.+ Onse pamodzi analipo anthu 75.+ 15  Yakobo anapita ku Iguputo+ kumene iye ndi makolo athu+ aja anamwalirira.+ 16  Kenako mafupa awo anawatengera ku Sekemu,+ kumene anakawaika m’manda.+ Anawaika m’manda amene Abulahamu anagula ndi ndalama zasiliva kwa ana a Hamori mu Sekemu.+ 17  “Nthawi itayandikira, yakuti lonjezo likwaniritsidwe limene Mulungu anapereka kwa Abulahamu, mtundu wa anthu unakula ndi kuwonjezeka mu Iguputo.+ 18  Kenako, mfumu ina imene sinali kudziwa za Yosefe inayamba kulamulira mu Iguputo.+ 19  Mfumu imeneyi inagwiritsa ntchito ulamuliro wake molakwika pofuna kuzunza anthu a fuko lathu,+ ndipo mwankhanza inachititsa makolo athuwo kutaya makanda awo, kuti asakhale ndi moyo.+ 20  Pa nthawi imeneyo Mose anabadwa,+ ndipo anali wokongola kwambiri, ngakhalenso pamaso pa Mulungu.+ Mose analeredwa m’nyumba ya bambo ake kwa miyezi itatu. 21  Koma pamene anamusiya yekha, mwana wamkazi wa Farao anamutola ndi kumulera ngati mwana wake.+ 22  Chotero Mose anaphunzira nzeru+ zonse za Aiguputo. Ndipo anali wamphamvu m’mawu+ ndi m’zochita zake. 23  “Tsopano pamene anakwanitsa zaka 40 zakubadwa, anaganiza zokayendera abale ake, ana a Isiraeli.+ 24  Ataona winawake akuzunzidwa, anamutchinjiriza ndi kupha Mwiguputo wozunzayo pobwezera m’malo mwa wozunzidwa uja.+ 25  Mose anali kuganiza kuti abale akewo azindikira kuti Mulungu akuwapatsa chipulumutso kudzera m’dzanja lake,+ koma iwo sanaizindikire mfundo imeneyi. 26  Tsiku lotsatira anaonekera kwa iwo pamene anali kumenyana, ndipo anayesa kuwayanjanitsa+ mwa kunena kuti, ‘Amuna inu, ndinu pachibale. N’chifukwa chiyani mukuzunzana chonchi?’+ 27  Koma amene anali kuzunza mnzakeyo anamukankha ndi kunena kuti, ‘Iweyo anakuika ndani kuti ukhale wolamulira ndi woweruza wathu?+ 28  Kodi ukufuna kundipha ngati mmene unaphera Mwiguputo uja dzulo?’+ 29  Atamva mawu amenewa, Mose anathawa ndi kukakhala kuchilendo m’dziko la Midiyani.+ Kumeneko anabereka ana aamuna awiri.+ 30  “Patapita zaka 40, mngelo anaonekera kwa iye m’malawi a moto pachitsamba chaminga+ m’chipululu, pafupi ndi phiri la Sinai. 31  Tsopano Mose ataona zimenezi, anadabwa kwambiri.+ Koma pamene anali kuyandikira kuti aonetsetse, panatuluka mawu a Yehova* akuti, 32  ‘Ine ndine Mulungu wa makolo ako. Ndine Mulungu wa Abulahamu, wa Isaki ndi wa Yakobo.’+ Ponjenjemera ndi mantha, Mose sanathenso kupitiriza kuyang’anitsitsa chitsambacho. 33  Yehova anamuuza kuti, ‘Vula nsapato zako, pakuti malo amene waimawo ndi malo oyera.+ 34  Ine ndaona ndithu mmene anthu anga amene ali ku Iguputo akuwazunzira.+ Ndamva kubuula kwawo+ ndipo ndatsika kudzawalanditsa.+ Tsopano tamvera. Ndikufuna ndikutume ku Iguputo.’+ 35  Mose ameneyo, amene iwo anamukana ndi kunena kuti, ‘Iweyo anakuika ndani kuti ukhale wolamulira ndi woweruza wathu?’+ munthu ameneyo ndi amene Mulungu anamutumiza+ monga wolamulira ndi mpulumutsi kudzera mwa mngelo amene anaonekera kwa iye pachitsamba chaminga chija. 36  Munthu ameneyo anawatsogolera ndi kutuluka nawo,+ atachita zodabwitsa ndi zizindikiro mu Iguputo,+ pa Nyanja Yofiira+ ndi m’chipululu kwa zaka 40.+ 37  “Ameneyu ndi Mose amene anauza ana a Isiraeli kuti, ‘Mulungu adzakupatsani mneneri ngati ine, kuchokera pakati pa abale anu.’+ 38  Uyu ndi amene+ anali pakati pa mpingo+ m’chipululu limodzi ndi mngelo+ amene analankhula ndi iyeyu komanso makolo athu paphiri la Sinai. Pamenepo analandira mawu opatulika+ omwe ndi amphamvu kuti awapereke kwa inu. 39  Koma makolo athu akale anakana kumumvera. M’malomwake, anamukankhira kumbali,+ ndipo mumtima mwawo anabwerera ku Iguputo.+ 40  Anauza Aroni kuti, ‘Tipangire milungu ititsogolere. Chifukwa sitikudziwa zimene zachitikira Mose, amene anatitsogolera potuluka m’dziko la Iguputo.’+ 41  Choncho iwo anapanga mwana wa ng’ombe m’masiku amenewo,+ ndi kubweretsa nsembe kwa fano limenelo. Pamenepo anasangalala ndi ntchito za manja awo.+ 42  Chotero Mulungu anawaleka+ kuti atumikire makamu akumwamba monga mmene malemba amanenera m’buku la aneneri.+ Malembawo amati, ‘Anthu inu a nyumba ya Isiraeli, kodi m’chipululu muja munali kupereka kwa ine nyama zansembe ndi zopereka zina kwa zaka 40?+ 43  Inutu munali kunyamula chihema cha Moloki+ ndi nyenyezi+ ya mulungu Refani, mafano amene munapanga kuti muziwalambira. Chotero ndidzakupitikitsirani+ kutali kupitirira Babulo.’ 44  “Makolo athuwo anali ndi chihema cha umboni m’chipululu. Anachipanga potsatira malangizo amene Mulungu anapereka pamene anali kulankhula ndi Mose. Mulungu anauza Mose kuti apange chihemacho molingana ndi chithunzi chimene anachiona.+ 45  Ndipo makolo athu amene anachilandira kwa makolo awo, analowa nacho limodzi ndi Yoswa,+ m’dziko limene linali m’manja mwa anthu a mitundu ina+ amene Mulungu anawapitikitsa pamaso pa makolo athu.+ Chihemacho chinakhala m’dziko limeneli mpaka m’masiku a Davide. 46  Mulungu anakomera mtima+ Davide ndipo iye anapempha mwayi wakuti amange nyumba yokhalamo+ Mulungu wa Yakobo. 47  Koma Solomo ndiye anamangira Mulungu nyumba.+ 48  Ngakhale ndi choncho, Wam’mwambamwamba sakhala m’nyumba zomangidwa ndi manja,+ monga mneneri akunenera kuti, 49  ‘Kumwamba ndiko mpando wanga wachifumu,+ ndipo dziko lapansi ndilo chopondapo mapazi anga.+ Kodi inu mudzandimangira nyumba yotani? akutero Yehova. Kapena malo oti ine ndipumuliremo ali kuti?+ 50  Kodi si dzanja langa limene linapanga zinthu zonsezi?’+ 51  “Anthu okanika inu ndi osachita mdulidwe wa mumtima+ ndi m’makutu. Nthawi zonse mumatsutsana ndi mzimu woyera. Mmene anachitira makolo anu inunso mukuchita chimodzimodzi.+ 52  Ndi mneneri uti amene makolo anuwo sanamuzunze?+ Inde, iwo anapha+ amene analengezeratu za kubwera kwa Wolungamayo,+ amene inuyo munamupereka ndi kumupha,+ 53  inu amene munalandira Chilamulo kudzera mwa angelo,+ koma osachisunga.” 54  Atamva zimenezi, anakwiya koopsa+ ndipo anayamba kumukukutira+ mano. 55  Koma iye, pokhala wodzazidwa ndi mzimu woyera, anayang’anitsitsa kumwamba ndi kuona ulemelero wa Mulungu ndi wa Yesu ataimirira kudzanja lamanja la Mulungu.+ 56  Ndipo ananena kuti: “Taonani! Ndikuona kumwamba kotseguka,+ ndipo Mwana wa munthu+ waimirira kudzanja lamanja la Mulungu.”+ 57  Iwo atamva zimenezi anafuula mokuwa atatseka m’makutu ndi manja awo,+ ndipo onse pamodzi anathamangira kwa iye. 58  Atamutulutsira kunja kwa mzinda,+ anayamba kumuponya miyala.+ Ndipo mboni+ zinaika malaya awo akunja pafupi ndi mnyamata wina dzina lake Saulo.+ 59  Iwo anapitiriza kumuponya miyala Sitefano, pamene iye anali kuchonderera kuti: “Ambuye Yesu, landirani mzimu* wanga.”+ 60  Kenako anagwada pansi ndi kufuula ndi mawu amphamvu kuti: “Yehova, musawaimbe mlandu wa tchimo ili.”+ Atanena zimenezi anagona tulo ta imfa.

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 2.
Onani Zakumapeto 4.