Machitidwe 4:1-37
4 Pamene Petulo ndi Yohane anali kulankhula ndi anthuwo, ansembe aakulu, woyang’anira kachisi+ ndi Asaduki+ anafika kwa iwo.
2 Iwo anali okwiya chifukwa atumwiwo anali kuphunzitsa anthu ndi kulalikira mosapita m’mbali za kuuka kwa akufa pogwiritsa ntchito chitsanzo cha Yesu.+
3 Choncho anawagwira ndi kuwasunga m’ndende mpaka tsiku lotsatira,+ chifukwa anali kale madzulo.
4 Koma anthu ambiri amene anamvetsera mawu awo anakhulupirira,+ ndipo chiwerengero cha amuna chinakwana pafupifupi 5,000.+
5 Tsiku lotsatira, olamulira ndi akulu ndiponso alembi anasonkhana pamodzi mu Yerusalemu.+
6 (Pamenepo panalinso Anasi+ wansembe wamkulu, Kayafa,+ Yohane, Alekizanda, ndi achibale ambiri a wansembe wamkuluyo.)
7 Ndiyeno anaimika atumwiwo pakati pawo n’kuyamba kuwafunsa kuti: “Kodi mwachita zimenezi ndi ulamuliro uti kapena m’dzina la ndani?”+
8 Pamenepo Petulo, atadzazidwa ndi mzimu woyera,+ anawayankha kuti:
“Olamulira anthu ndiponso akulu inu,
9 ngati pa ntchito yabwino imene tachita kwa wodwalayu,+ lero tikufunsidwa kuti tamuchiritsa m’dzina la ndani,
10 dziwani nonsenu ndi Aisiraeli onse, kuti m’dzina la Yesu Khristu Mnazareti+ uja, amene inu munamupachika pamtengo,+ koma amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa,+ kudzera mwa iyeyo, munthu uyu waimirira pamaso panu atachira bwinobwino.
11 Yesu ameneyu ndiye ‘mwala umene inu omanga nyumba munauona ngati wopanda pake, umene tsopano wakhala mwala wofunika kwambiri wapakona.’+
12 Ndiponso chipulumutso sichipezeka mwa munthu wina aliyense, pakuti palibe dzina lina+ pansi pa thambo, limene laperekedwa kwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.”+
13 Tsopano ataona mmene Petulo ndi Yohane anali kulankhulira molimba mtima, komanso atazindikira kuti anali anthu osaphunzira ndiponso anthu wamba,+ anadabwa kwambiri. Ndipo anayamba kuwazindikira kuti anali kuyenda ndi Yesu.+
14 Ndiyeno poona munthu wochiritsidwa uja ataimirira nawo limodzi,+ analibe chonena kuti awatsutse.+
15 Choncho anawalamula kuti atuluke muholo ya Khoti Lalikulu la Ayuda,* ndipo anayamba kufunsana,
16 kuti: “Tichite nawo chiyani amuna amenewa?+ Chifukwa kunena zoona, iwo achitadi chizindikiro chachikulu, chimene chaonekera kwa onse okhala mu Yerusalemu.+ Ndipo ife sitingatsutse zimenezi.
17 Komabe, kuti nkhaniyi isapitirire kufalikira kwa anthu ena, tiyeni tiwaopseze kuti asalankhulenso m’dzina limeneli kwa munthu wina aliyense.”+
18 Atatero anawaitana ndi kuwalamula kuti asalankhulenso kapena kuphunzitsa m’dzina la Yesu kwina kulikonse.
19 Koma poyankha, Petulo ndi Yohane anawauza kuti: “Weruzani nokha, ngati n’koyenera pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu.
20 Koma ife sitingaleke kulankhula zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.”+
21 Choncho atawonjezera kuwaopseza, anawamasula, pakuti sanapeze chifukwa chilichonse chowapatsira chilango. Komanso anaopa anthu,+ pakuti onse anali kutamanda Mulungu chifukwa cha zimene zinachitikazo.
22 Ndipotu chizindikiro cha machiritsochi chinachitika kwa munthu amene anali ndi zaka zopitirira 40.
23 Atawamasula anapita kwa okhulupirira anzawo,+ ndipo anawafotokozera zonse zimene ansembe aakulu, ndi akulu anawauza.
24 Atamva zimenezi, onse pamodzi anafuula kwa Mulungu+ mokweza mawu kuti:
“Ambuye Wamkulu Koposa,+ Inu ndi amene munapanga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zokhala mmenemo.+
25 Ndinu amene mwa mzimu woyera, munanena kudzera pakamwa pa kholo lathu Davide,+ mtumiki wanu kuti, ‘N’chifukwa chiyani anthu a mitundu ina akuchita chipolowe, ndiponso n’chifukwa chiyani mitundu ya anthu ikusinkhasinkha zinthu zopanda pake?+
26 Mafumu a dziko lapansi aima pamalo awo, ndipo olamulira asonkhana pamodzi mogwirizana, kuti alimbane ndi Yehova komanso wodzozedwa wake.’+
27 Zimenezi zinachitikadi pamene Herode,* Pontiyo Pilato,+ pamodzi ndi anthu a mitundu ina komanso anthu a mu Isiraeli, anasonkhana mumzinda uno ndi kuukira Yesu, mtumiki wanu woyera,+ amene inu munamudzoza.+
28 Iwo anasonkhana pamodzi kuti achite zimene inu munaneneratu. Zimenezi zinachitika chifukwa inu muli ndi mphamvu komanso chifukwa chakuti zinali zogwirizana ndi chifuniro chanu.+
29 Koma tsopano Yehova, imvani mmene akutiopsezera,+ ndipo lolani kuti akapolo anu apitirize kulankhula mawu anu molimba mtima.+
30 Pitirizani kutambasula dzanja lanu ndi kupereka machiritso, komanso kuti zizindikiro ndi zodabwitsa+ zipitirize kuchitika m’dzina+ la Yesu, mtumiki wanu woyera.”+
31 Atatha kupembedzera, malo amene anasonkhanawo anagwedezeka.+ Pamenepo aliyense wa iwo anadzazidwa ndi mzimu woyera,+ ndipo anayamba kulankhula mawu a Mulungu molimba mtima.+
32 Ndipo onse amene anakhulupirira anakhala ndi mtima umodzi ndi maganizo amodzi.+ Panalibe ngakhale mmodzi wonena kuti zinthu zimene anali nazo zinali zayekha. Zonse zimene anali nazo zinali za onse.+
33 Komanso, atumwiwo anapitiriza kuchitira umboni mwamphamvu kwambiri za kuuka kwa Ambuye Yesu.+ Ndipo kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu kunali pa onsewo.
34 Ndithudi, panalibe ngakhale mmodzi wosowa kanthu pakati pawo.+ Onse amene anali ndi minda kapena nyumba, anali kuzigulitsa ndi kubweretsa ndalamazo,
35 kudzazipereka kwa atumwi.+ Ndiyeno ndalamazo anali kuzigawa+ kwa aliyense malinga ndi zosowa zake.
36 Choncho Yosefe, amene atumwiwo anamutchanso Baranaba,+ dzina limene polimasulira limatanthauza, Mwana wa Chitonthozo, amene anali Mlevi, komanso mbadwa ya ku Kupuro,
37 anali ndi munda. Iye anagulitsa mundawo ndi kubweretsa ndalamazo kudzazipereka kwa atumwi.+