Machitidwe 14:1-28

14  Tsopano Paulo ndi Baranaba ali ku Ikoniyo,+ analowa m’sunagoge+ wa Ayuda. Mmenemo analankhula bwino kwambiri moti khamu lalikulu la Ayuda limodzi ndi Agiriki+ anakhala okhulupirira.  Koma Ayuda amene sanakhulupirire, anauza zoipa+ anthu a mitundu ina ndi kupotoza maganizo awo kuti atsutsane ndi abalewo.+  Chotero kwa nthawi yaitali, anakhala akulankhula molimba mtima chifukwa cha mphamvu ya Yehova. Iye anatsimikizira mawu a kukoma mtima kwake kwakukulu, mwa kulola kuti zizindikiro ndi zodabwitsa zichitike kudzera mwa ophunzirawo.+  Koma khamu la mumzindawo linagawanika. Ena anakhala kumbali ya Ayuda, ena kumbali ya atumwi.  Ndiyeno anthu a mitundu ina komanso Ayuda pamodzi ndi olamulira awo, anakonza chiwembu kuti achitire chipongwe atumwiwo ndi kuwaponya miyala.+  Koma iwo atadziwitsidwa zimenezi, anathawira+ m’mizinda ya Lukaoniya, Lusitara, Debe, ndi m’madera ozungulira.  Kumeneko anapitiriza kulengeza uthenga wabwino.+  Tsopano ku Lusitara, mwamuna wina wolumala miyendo anali atakhala pansi. Iyeyu anabadwa wolumala ndipo anali asanayendepo chibadwire.+  Mwamuna ameneyu anali kumvetsera pamene Paulo anali kulankhula. Ndiyeno Paulo atamuyang’anitsitsa anaona kuti ali ndi chikhulupiriro+ ndipo angathe kuchiritsidwa. 10  Choncho Paulo analankhula mokweza mawu kuti: “Imirira ndi miyendo yako!” Pamenepo iye anadumpha n’kuyamba kuyenda.+ 11  Pamene khamu la anthu linaona zimene Paulo anachitazo, linafuula ndi kunena m’chinenero cha Chilukaoniya kuti: “Milungu+ yakhala ngati anthu, ndipo yatsikira kwa ife!” 12  Chotero Baranaba anayamba kumutchula kuti Zeu, koma Paulo anamutchula kuti Heme, chifukwa ndi amene anali kutsogolera polankhula. 13  Ndiyeno wansembe wa Zeu, amene kachisi wake anali pafupi kunja kwa mzindawo, anabweretsa ng’ombe zamphongo ndi nkhata zamaluwa kuzipata. Iye pamodzi ndi khamu la anthulo anali kufuna kupereka nsembe.+ 14  Koma atumwiwo, Baranaba ndi Paulo, atamva zimenezi anang’amba malaya awo akunja ndi kuthamanga kukalowa m’khamu la anthu lija akufuula 15  kuti: “Anthu inu, mukuchitiranji zimenezi? Ifenso ndife anthu+ okhala ndi zofooka+ ngati inu nomwe, ndipo tikulengeza uthenga wabwino kwa inu. Tikuchita izi kuti musiye zachabechabe zimenezi+ ndi kutembenukira kwa Mulungu wamoyo,+ amene anapanga kumwamba,+ dziko lapansi, nyanja ndi zonse zokhala mmenemo. 16  M’mibadwo ya m’mbuyomu iye analola anthu a mitundu yonse kuyenda m’njira zawo.+ 17  Komabe iye sanangokhala wopanda umboni wakuti anachita zabwino.+ Anakupatsani mvula+ kuchokera kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zanu zimakhala zambiri. Anadzaza mitima yanu ndi chakudya komanso chimwemwe.”+ 18  Ngakhale kuti atumwiwo ananena mawu amenewa, anavutikabe kuti aletse khamu la anthulo kupereka nsembe kwa iwo. 19  Ndiyeno Ayuda anafika kuchokera ku Antiokeya ndi ku Ikoniyo ndipo anakopa anthuwo.+ Choncho anaponya Paulo miyala ndi kumukokera kunja kwa mzindawo, poganiza kuti wafa.+ 20  Koma pamene ophunzira anamuzungulira, anadzuka ndi kukalowa mumzinda. Tsiku lotsatira iye pamodzi ndi Baranaba anachoka ndi kupita ku Debe.+ 21  Atalengeza uthenga wabwino mumzinda umenewo ndi kuphunzitsa anthu angapo kuti akhale ophunzira,+ anabwerera ku Lusitara, ku Ikoniyo ndi ku Antiokeya. 22  M’malo onsewa anali kulimbitsa mitima ya ophunzira+ ndi kuwalimbikitsa kuti akhalebe m’chikhulupiriro. Anali kuwauza kuti: “Tiyenera kukumana ndi masautso ambiri kuti tikalowe mu ufumu wa Mulungu.”+ 23  Komanso, anawaikira akulu+ mumpingo uliwonse, ndipo atapemphera ndi kusala kudya,+ anawapereka kwa Yehova+ yemwe anamukhulupirira. 24  Kenako anadutsa ku Pisidiya ndi kukalowa ku Pamfuliya.+ 25  Atalengeza mawu opatulika ku Pega, anapita ku Ataliya. 26  Pochoka kumeneko anayenda ulendo wa pamadzi wobwerera ku Antiokeya.+ Kumeneku n’kumene m’mbuyomo abale anawaika m’manja mwa Mulungu kuti awasonyeze kukoma mtima kwakukulu n’cholinga choti agwire ntchito imene tsopano anali ataikwaniritsa.+ 27  Atafika kumeneko ndi kusonkhanitsa pamodzi mpingo, anafotokoza+ zinthu zambiri zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwo. Anafotokozanso kuti Mulungu anatsegulira anthu a mitundu ina khomo lolowera m’chikhulupiriro chimenechi.+ 28  Choncho anakhala ndi ophunzirawo kwa kanthawi ndithu.

Mawu a M'munsi