Luka 4:1-44
4 Tsopano Yesu anachoka ku Yorodano atadzazidwa ndi mzimu woyera. Ndipo mzimuwo unamutenga ndi kumuyendetsa uku ndi uku m’chipululu+
2 kwa masiku 40,+ kumene anali kuyesedwa+ ndi Mdyerekezi. Komanso m’masiku amenewo sanali kudya chilichonse, choncho masikuwo atatha, anamva njala.
3 Mdyerekezi ataona zimenezi anamuuza kuti: “Ngati ndinudi mwana wa Mulungu, uzani mwala uwu kuti usanduke mkate.”
4 Koma Yesu anamuyankha kuti: “Malemba amati, ‘Munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha.’”+
5 Choncho anakwera naye pamwamba ndipo anamuonetsa maufumu onse a padziko lapansi m’kanthawi kochepa.
6 Ndiyeno Mdyerekezi anamuuza kuti: “Ndikupatsani ulamuliro+ pa maufumu onsewa ndi ulemerero wawo wonse, chifukwa unaperekedwa kwa ine. Ndikhoza kuupereka kwa aliyense amene ndakonda kum’patsa.+
7 Chotero ngati inuyo mungandiweramireko+ kamodzi kokha, ulamuliro wonsewu udzakhala wanu.”
8 Poyankha Yesu anamuuza kuti: “Malemba amati, ‘Yehova* Mulungu wako+ ndi amene uyenera kumulambira, ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.’”+
9 Kenako anamutengera ku Yerusalemu, ndipo anamukweza pamwamba pa khoma+ la mpanda wa kachisi n’kumuuza kuti: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, mudziponye pansi kuchokera pano.+
10 Pajatu Malemba amati, ‘Iye adzalamula angelo ake za inu, kuti akutetezeni.’+
11 Choncho, ‘Adzakunyamulani m’manja mwawo, kuti phazi lanu lisawombe mwala uliwonse.’”+
12 Poyankha Yesu anamuuza kuti: “Pajatu Malemba amati, ‘Usamuyese, Yehova Mulungu wako.’”+
13 Choncho Mdyerekeziyo atamaliza mayesero onsewo, anamusiya kufikira nthawi ina yabwino.+
14 Tsopano Yesu anabwerera ku Galileya+ atadzazidwa ndi mphamvu ya mzimu. Ndipo mbiri yake yabwino inamveka ponseponse m’madera onse ozungulira.+
15 Komanso, anayamba kuphunzitsa m’masunagoge awo, ndipo anthu onse anali kumulemekeza.+
16 Kenako anabwera ku Nazareti,+ kumene analeredwa. Malinga ndi chizolowezi chake pa tsiku la sabata, analowa m’sunagoge,+ ndi kuimirira kuti awerenge Malemba.
17 Pamenepo anamupatsa mpukutu wa mneneri Yesaya. Iye anafunyulula mpukutuwo ndi kupeza pamene panalembedwa mawu akuti:
18 “Mzimu wa Yehova+ uli pa ine, chifukwa iye anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa osauka. Anandituma kudzalalikira za kumasulidwa kwa ogwidwa ukapolo, ndi zoti akhungu ayambe kuona. Anandituma kudzamasula oponderezedwa kuti akhale mfulu,+
19 ndi kudzalalikira chaka chovomerezeka kwa Yehova.”+
20 Atatero anapinda mpukutuwo, n’kuubwezera kwa wotumikira mmenemo ndi kukhala pansi. Maso onse m’sunagogemo anali pa iye kumuyang’anitsitsa.
21 Ndiyeno anayamba kuwauza kuti: “Lero lemba ili, limene mwangolimva kumeneli lakwaniritsidwa.”+
22 Pamenepo onse anayamba kumutamanda ndi kudabwa ndi mawu ogwira mtima+ otuluka pakamwa pake, mwakuti anali kunena kuti: “Kodi iyeyu si mwana wa Yosefe?”+
23 Zitatero iye anawauza kuti: “Mosakayikira mawu akuti, ‘Wochiritsa+ iwe, dzichiritse wekha,’ mudzawagwiritsa ntchito pa ine. Mudzanena kuti: ‘Tinamva kuti unachita zinthu zambiri ku Kaperenao.+ Zinthu zimenezo+ uzichitenso kwanu kuno.’”+
24 Iye ananenanso kuti: “Ndithu ndikukuuzani, palibe mneneri amene amalandiridwa kwawo.
25 Mwachitsanzo, ndikukuuzani ndithu kuti, Munali akazi ambiri amasiye mu Isiraeli m’masiku a Eliya, pamene kumwamba kunatsekedwa zaka zitatu ndi miyezi 6, mwakuti m’dziko lonse munagwa njala yaikulu.+
26 Koma Eliya sanatumizidwe kwa aliyense wa akazi amenewo. M’malomwake anatumizidwa kwa mkazi wamasiye ku Zarefati+ m’dziko la Sidoni.
27 Ndiponso, munali akhate ambiri mu Isiraeli m’nthawi ya mneneri Elisa. Komabe palibe aliyense wa iwo amene anayeretsedwa, koma Namani, mwamuna wa ku Siriya.”+
28 Tsopano onse amene anali kumvetsera mawu amenewa m’sunagogemo anakwiya kwambiri.+
29 Iwo ananyamuka ndipo mwamsangamsanga anamutulutsira kunja kwa mzinda. Kenako anapita naye pamwamba pa phiri limene anamangapo mzinda wawo, kuti akam’ponye kuphedi.+
30 Koma iye anangodutsa pakati pawo n’kumapita.+
31 Choncho anapita ku Kaperenao,+ mzinda wa ku Galileya. Ndipo anali kuwaphunzitsa pa sabata.
32 Kumeneko anthu anadabwa kwambiri ndi kaphunzitsidwe kake,+ chifukwa anali kulankhula ndi mphamvu za ulamuliro.+
33 Tsopano m’sunagogemo munali munthu wogwidwa ndi mzimu,+ chiwanda chonyansa, ndipo anafuula ndi mawu amphamvu kuti:
34 “Tili nanu chiyani,+ Yesu Mnazareti?+ Kodi mwabwera kudzatiwononga? Inetu ndikukudziwani+ bwino kwambiri, ndinu Woyera wa Mulungu.”+
35 Koma Yesu anadzudzula mzimuwo kuti: “Khala chete, ndipo tuluka mwa iye.” Choncho chiwandacho chinagwetsa munthuyo pansi pakati pawo, kenako chinatuluka mwa iye osamuvulaza.+
36 Ataona zimenezi, onse anadabwa kwambiri, ndipo anayamba kukambirana kuti: “Kulankhula kumeneku ndi kwa mtundu wanji anthuni? Taonani! Akutha kudzudzula mizimu yonyansa mwa ulamuliro ndi mphamvu, ndipo mizimuyo ikutulukadi.”+
37 Choncho mbiri yake inapitiriza kufalikira ponseponse m’midzi yonse yozungulira.+
38 Atatuluka m’sunagogemo, anakalowa m’nyumba ya Simoni. Kumeneko apongozi aakazi a Simoni anali kudwala malungo* aakulu, choncho anam’pempha kuti apite kumeneko chifukwa cha mayiwo.+
39 Chotero anaima pamene mayiwo anagona ndi kuwachiritsa,+ ndipo malungowo anatheratu. Nthawi yomweyo mayiwo anadzuka n’kuyamba kuwatumikira.+
40 Koma pamene dzuwa linali kulowa, onse amene anali ndi anthu odwala matenda osiyanasiyana anawabweretsa kwa iye. Ndipo iye anawachiritsa mwa kuika manja ake pa aliyense.+
41 Ziwanda nazonso zinatuluka mwa anthu ambiri.+ Zinali kufuula kuti: “Inu ndinu Mwana+ wa Mulungu.” Koma iye anali kudzudzula ziwandazo, ndipo sanali kuzilola kuti zilankhule,+ chifukwa zinali kudziwa kuti iye+ ndi Khristu.+
42 Kutacha, anatuluka ndi kupita kumalo kopanda anthu.+ Koma khamu la anthu linayamba kumufunafuna mpaka linafika kumene iye anali, ndipo anthuwo anayesa kumuletsa kuti asawasiye.
43 Koma iye anawauza kuti: “Ndiyenera kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu kumizinda inanso, chifukwa ndi zimene anandituma kudzachita.”+
44 Choncho anapita n’kumalalikira m’masunagoge a mu Yudeya.+