Luka 19:1-48

19  Ndiyeno Yesu analowa mu Yeriko,+ koma anali kungodutsamo.  Kumeneko kunali munthu wina dzina lake Zakeyu. Iyeyu anali mkulu wa okhometsa msonkho, ndipo anali wolemera.  Zakeyu anali kufunitsitsa kuona+ Yesu kuti ndi wotani, koma sanathe kutero chifukwa cha khamu la anthu, pakuti anali wamfupi.  Choncho anathamangira kutsogolo n’kukwera mumtengo wamkuyu kuti athe kumuona, chifukwa anali kudzera njira imeneyo.  Yesu atafika pamalopo, anayang’ana m’mwambamo n’kumuuza kuti: “Zakeyu, fulumira tsika, chifukwa lero ndiyenera kukakhala m’nyumba mwako.”  Atamva zimenezo anatsika mofulumira, ndipo mosangalala anamulandira m’nyumba mwake monga mlendo wake.  Koma anthu ataona Yesu akulowa m’nyumbamo, onse anayamba kung’ung’udza,+ kuti: “Akupita kukakhala ndi munthu wochimwa.”  Koma Zakeyu anaimirira ndi kuuza Ambuye kuti: “Ambuye, ine ndipereka ndithu hafu ya chuma changa kwa osauka. Ndipo chilichonse chimene ndinalanda munthu aliyense pomunamizira mlandu+ ndibweza kuwirikiza kanayi.”+  Pamenepo Yesu anamuuza kuti: “Lero chipulumutso chafika panyumba ino, chifukwa nayenso ndi mwana wa Abulahamu.+ 10  Pakuti Mwana wa munthu anabwera kudzafunafuna ndi kupulumutsa anthu osochera.”+ 11  Pamene iwo anali kumvetsera zimenezi, iye anawonjezapo fanizo, chifukwa anali pafupi ndi Yerusalemu ndipo anthu anali kuganiza kuti ufumu wa Mulungu uonekera nthawi yomweyo.+ 12  Choncho iye ananena kuti: “Munthu wina wa m’banja lachifumu anapita kudziko lakutali kuti akalandire ufumu ndi kubwerako.+ 13  Ndiyeno anaitana akapolo ake 10 ndi kuwapatsa ndalama 10 za mina n’kuwauza kuti, ‘Muchite malonda mpaka nditabwera.’+ 14  Koma nzika zinzake zinadana naye+ ndipo m’mbuyo muno zinatumiza akazembe kuti apite akanene kuti, ‘Ife sitikufuna kuti munthu uyu akhale mfumu yathu.’+ 15  “Atabwerera kwawo pambuyo polandira ufumuwo, analamula kuti akapolo ake aja amene anawapatsa ndalama zasiliva abwere kwa iye, kuti awerengerane ndi kuona mmene apindulira pa malonda awo.+ 16  Woyamba anafika ndipo ananena kuti, ‘Mbuyanga, ndalama yanu ya mina ija inapindula ndalama zina 10 za mina.’+ 17  Iye anamuuza kuti, ‘Unagwira ntchito, ndiwe kapolo wabwino! Chifukwa wasonyeza kukhulupirika pa chinthu chaching’ono, ndakupatsa ulamuliro woyang’anira mizinda 10.’+ 18  Kenako wachiwiri anafika, ndipo anati, ‘Ambuye ndalama yanu ija ya mina yapindula zinanso zisanu.’+ 19  Iye anauzanso ameneyu kuti, ‘Nawenso ukhala woyang’anira mizinda isanu.’+ 20  Tsopano panafika wina ndipo ananena kuti, ‘Ambuye, ndalama yanu ya mina ija nayi. Ndinaimanga pansalu ndi kuisunga. 21  Ndinachita zimenezi chifukwa ndinali kukuopani. Inutu ndinu munthu wouma mtima. Mumatenga zimene simunasungitse ndi kukolola zimene simunafese.’+ 22  Iye anamuuza kuti, ‘Ndikuweruza mwa zotuluka pakamwa pako,+ kapolo woipa iwe. Ukuti unadziwa kuti ine ndine munthu wouma mtima, wotenga zimene sindinasungitse ndi kukolola zimene sindinafese?+ 23  Nangano n’chifukwa chiyani sunasungitse ndalama yanga yasilivayo kwa osunga ndalama? Ukanatero, ine pobwera ndikanaitenga limodzi ndi chiwongoladzanja chake.’+ 24  “Atatero anauza anthu amene anaima chapafupi kuti, ‘Mulandeni ndalama ya mina imeneyo ndi kuipereka kwa winayo amene ali ndi ndalama 10.’+ 25  Koma iwo anamuuza kuti, ‘Ambuye, iyetu ali nazo ndalama za mina 10!’ . . . 26  ‘Ndithu ndikukuuzani, Aliyense amene ali nazo, adzamuwonjezera zochuluka, koma amene alibe adzalandidwa ngakhalenso zimene ali nazo.+ 27  Komanso adani angawa, amene sanafune kuti ine ndikhale mfumu yawo, bwerani nawo kuno muwaphe ine ndikuona.’”+ 28  Choncho atatsiriza kunena zimenezi, anapitiriza ulendo wake wopita ku Yerusalemu.+ 29  Tsopano atayandikira ku Betefage ndi Betaniya paphiri lotchedwa phiri la Maolivi,+ anatumiza ophunzira ake awiri.+ 30  Iye anawauza kuti: “Pitani m’mudzi umene mukuuonawo, ndipo mukalowa mmenemo mukapeza bulu wamng’ono wamphongo atamumangirira, amene munthu sanakwerepo chiyambire. Mukamumasule n’kubwera naye kuno.+ 31  Koma aliyense akakakufunsani kuti, ‘N’chifukwa chiyani mukumasula buluyu?’ Mukanene kuti, ‘Ambuye akumufuna.’”+ 32  Choncho otumidwawo ananyamuka ndipo anakam’pezadi mmene iye anawauzira.+ 33  Koma mmene anali kumasula buluyo, eniake anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukumasula buluyu?”+ 34  Iwo anayankha kuti: “Ambuye akumufuna.”+ 35  Pamenepo iwo anamutenga ndi kupita naye kwa Yesu. Kenako iwo anaponya malaya awo akunja pabuluyo ndi kukwezapo Yesu.+ 36  Pamene anali kuyenda,+ anthu anali kuyala malaya awo akunja mumsewu.+ 37  Atangofika pafupi ndi msewu wochokera m’phiri la Maolivi khamu lonse la ophunzirawo linayamba kukondwera ndi kutamanda Mulungu mokweza mawu chifukwa cha ntchito zamphamvu zimene anaona.+ 38  Iwo anali kunena kuti: “Wodalitsidwa Iye wobwera monga Mfumu m’dzina la Yehova!+ Mtendere kumwamba, ndi ulemerero kumwambamwambako!”+ 39  Koma Afarisi ena m’khamulo anauza Yesu kuti: “Mphunzitsi, adzudzuleni ophunzira anuwa.”+ 40  Poyankha iye anati: “Ndithu ndikukuuzani, ngati awa atakhala chete, miyala+ ingathe kufuula.” 41  Tsopano atayandikira mzinda wa Yerusalemu, anaona mzindawo n’kuyamba kuulirira.+ 42  Iye anati: “Iwe ukanazindikira+ lero zinthu zamtendere . . . koma tsopano zabisika kuti usathe kuziona.+ 43  Chifukwa masiku adzakufikira pamene adani ako adzamanga mpanda+ wazisonga+ kukuzungulira.+ Adaniwo adzakutsekereza ndi kukusautsa+ kuchokera kumbali zonse. 44  Iwo adzakuwononga+ limodzi ndi ana ako amene ali mwa iwe. Ndipo sadzasiya mwala pamwala unzake+ mwa iwe, chifukwa sunazindikire kuti nthawi yokuyendera inali itakwana.”+ 45  Ndiyeno analowa m’kachisi n’kuyamba kuthamangitsa anthu amene anali kugulitsamo zinthu,+ 46  ndi kuwauza kuti: “Malemba amati, ‘Nyumba yanga idzakhala nyumba yopemphereramo,’+ koma inu mwaisandutsa phanga la achifwamba.”+ 47  Ndipo anali kuphunzitsa m’kachisimo tsiku ndi tsiku. Koma ansembe aakulu, alembi ndi akuluakulu a anthu anafunitsitsa kumupha.+ 48  Komabe anasowa chochita chifukwa anthu ambiri anali kungomuunjirira kuti amumvetsere ndipo sanali kusiyana naye.+

Mawu a M'munsi