Luka 16:1-31

16  Kenako anauzanso ophunzira ake kuti: “Munthu wina anali wolemera ndipo anali ndi mtumiki woyang’anira nyumba+ yake. Mtumiki ameneyu ena anamuneneza kwa bwana wakeyo kuti anali kumusakazira chuma.+  Choncho anamuitana ndi kumuuza kuti, ‘Ndamva zoipa zimene ukuchita. Pita ukalembe lipoti la mmene wagwirira ntchito yoyang’anira nyumba ino udzandipatse,+ pakuti supitiriza kuyendetsa ntchito za panyumba pano.’  Pamenepo mtumikiyo mumtima mwake anati, ‘Nditani ine, pakuti bwana wanga+ andichotsa ntchito? Sindingathe kulima chifukwa ndilibe mphamvu, ndipo ndikuchita manyazi kukhala wopemphapempha.  Eya! Ndadziwa chochita kuti akandichotsa ntchito, anthu akandilandire bwino m’nyumba zawo.’+  Ndiyeno anaitana amene anali ndi ngongole kwa bwana wake mmodzi ndi mmodzi, ndipo anafunsa woyamba kuti, ‘Uli ndi ngongole yochuluka bwanji kwa bwana wanga?’  Iye anayankha kuti, ‘Mitsuko 100 ya mafuta a maolivi.’ Iye anamuuza kuti, ‘Nayi kalata yako ya ngongole, khala pansi ulembe mitsuko 50 mwamsanga.’  Kenako anafunsa wina kuti, ‘Nanga iwe, ngongole yako ndi yaikulu bwanji?’ Iye anayankha kuti, ‘Madengu 100 a tirigu.’ Iye anamuuza kuti, ‘Nayi kalata yako ya ngongole ulembepo madengu 80.’  Bwana wake uja anamuyamikira mtumiki ameneyu, ngakhale kuti anali wosalungama, chifukwa anachita mwanzeru.+ Pakuti ana a m’dziko lino amachita mwanzeru pochita zinthu ndi anthu a m’badwo wawo kuposa ana a kuwala.+  “Nanunso ndikukuuzani kuti, Dzipezereni mabwenzi+ ndi chuma chosalungama,+ kuti chumacho chikatha, akakulandireni m’malo okhala amuyaya.+ 10  Munthu wokhulupirika pa chinthu chaching’ono alinso wokhulupirika pa chinthu chachikulu, ndipo munthu wosalungama pa chinthu chaching’ono alinso wosalungama pa chinthu chachikulu.+ 11  Choncho, ngati simunakhale wokhulupirika pa chuma chosalungama, ndani adzakupatseni ntchito yoyang’anira chuma chenicheni?+ 12  Komanso ngati simunakhale wokhulupirika pa zinthu za ena,+ ndani adzakupatseni mphoto imene anakusungirani? 13  Wantchito wa panyumba sangatumikire ambuye awiri, chifukwa adzadana ndi mmodzi ndi kukonda wina, kapena adzakhulupirika kwa mmodzi ndi kunyoza winayo. Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.”+ 14  Tsopano Afarisi, amene anali okonda kwambiri ndalama, anali kumvetsera zonsezi, ndipo anayamba kumunyogodola.+ 15  Pamenepo iye anawauza kuti: “Inu mumadzitcha olungama pamaso pa anthu,+ koma Mulungu akudziwa mitima yanu.+ Chifukwa chimene chili chapamwamba kwa anthu n’chonyansa m’maso mwa Mulungu.+ 16  “Anthu anali kulalikira Chilamulo ndi Zolemba za aneneri kudzafika m’nthawi ya Yohane.+ Kuchokera nthawi imeneyo, uthenga wabwino umene ukulengezedwa ndi wokhudza ufumu wa Mulungu, ndipo anthu osiyanasiyana akuyesetsa mwakhama kuti akalowemo.+ 17  Ndithudi, n’chapafupi kuti kumwamba ndi dziko lapansi zichoke+ kusiyana n’kuti ngakhale mbali chabe ya chilembo chimodzi+ cha m’Chilamulo isakwaniritsidwe.+ 18  “Aliyense wosiya mkazi wake ndi kukwatira wina, wachita chigololo, ndipo wokwatira mkazi wosiyidwayo wachita chigololo.+ 19  “Munthu winawake+ anali wolemera, ndipo nthawi zonse anali kuvala zovala zofiirira zapamwamba ndi nsalu zabwino kwambiri. Iye anali kusangalala ndi kudyerera tsiku ndi tsiku.+ 20  Koma munthu wina wopemphapempha dzina lake Lazaro, anali kumukhazika pachipata cha wachumayo, ali ndi zilonda thupi lonse. 21  Iyeyo ankalakalaka kudya nyenyeswa zakugwa patebulo la wachuma uja. Agalu nawonso anali kubwera kudzanyambita zilonda zakezo. 22  Patapita nthawi wopemphapempha uja anamwalira+ ndipo angelo anamutenga kukamuika pachifuwa+ cha Abulahamu.+ “Munthu wachuma ujanso anamwalira+ ndipo anaikidwa m’manda. 23  Ali m’Mandamo anakweza maso ake, ali mkati mozunzika,+ ndipo anaona Abulahamu kutali, ndipo Lazaro anali pachifuwa chake. 24  Choncho anaitana kuti, ‘Atate Abulahamu,+ ndichitireni chifundo. Mutume Lazaro kuti aviike nsonga ya chala chake m’madzi kuti aziziritse lilime langa,+ chifukwa ndikuzunzika m’moto wolilimawu.’+ 25  Koma Abulahamu anati, ‘Mwanawe, kumbukira kuti unalandiriratu zabwino zako zonse pamene unali moyo, ndipo Lazaro analandiriratu zinthu zoipa. Koma tsopano akusangalala kuno ndipo iwe ukuzunzika.+ 26  Komanso, paikidwa phompho lalikulu kwambiri+ pakati pa ife ndi anthu inu,+ moti ofuna kuolokera kumeneko kuchokera kuno sangathe. Komanso anthu sangaoloke kuchokera kumeneko kubwera kuno.’+ 27  Ndiyeno munthu wachuma uja anati, ‘Popeza zili choncho, ndikukupemphani atate kuti, mum’tumize kunyumba ya bambo anga. 28  Chifukwa ndili ndi abale anga asanu kumeneko, choncho apite akawapatse umboni wokwanira, kuti nawonso asabwere kumalo ozunzikira kuno.’ 29  Koma Abulahamu ananena kuti, ‘Kumeneko ali ndi Zolemba za Mose+ ndi Zolemba za aneneri,+ amvere zimenezo.’+ 30  Pamenepo iye anati, ‘Ayi chonde atate Abulahamu, pakuti ngati wina wochokera kwa akufa angapite kumeneko, iwo adzalapa ndithu.’ 31  Koma iye anamuuza kuti, ‘Ngati sakumvera Zolemba za Mose+ ndi Zolemba za aneneri, sangathekebe ngakhale wina atauka kwa akufa.’”

Mawu a M'munsi