Luka 12:1-59

12  Pa nthawiyi, chikhamu cha anthu masauzandemasauzande chinali chitasonkhana, moti anali kupondanapondana. Pamenepo Yesu anayamba kulankhula ndi ophunzira ake choyamba kuti: “Samalani ndi chofufumitsa+ cha Afarisi, chimene chili chinyengo.+  Komatu palibe chobisika chimene sichidzaululika, ndi chinsinsi chimene sichidzadziwika.+  Choncho zimene mumanena mumdima zidzamveka poyera, zimene mumanong’ona kwanokha m’zipinda zanu zidzalalikidwa pamadenga.+  Komanso ndikukuuzani ndithu, mabwenzi anga,+ Musamaope amene amapha thupi lokha, amene sangathe kuchita zoposa pamenepa.+  Koma ndikuuzani woti muzimuopa: Muziopa iye+ amene amati akapha, amakhalanso ndi mphamvu zoponya munthu m’Gehena.*+ Ndithu ndikukuuzani, muziopa+ Ameneyu.  Mpheta zisanu amazigulitsa makobidi awiri ochepa mphamvu, si choncho kodi? Komatu palibe ngakhale imodzi mwa izo imene imaiwalika kwa Mulungu.+  Ndipo ngakhale tsitsi+ lonse la m’mutu mwanu analiwerenga. Musachite mantha. Ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zambiri.+  “Chotero ndikukuuzani kuti, Aliyense wovomereza+ pamaso pa anthu kuti ali kumbali yanga, Mwana wa munthunso adzavomereza pamaso pa angelo a Mulungu kuti ali kumbali yake.+  Koma aliyense wondikana+ ine pamaso pa anthu, adzakanidwa pamaso pa angelo a Mulungu.+ 10  Ndipo aliyense wonena mawu onyoza Mwana wa munthu, adzakhululukidwa. Koma wonyoza mzimu woyera sadzakhululukidwa.+ 11  Akapita nanu kumabwalo amilandu, ndi kwa akuluakulu aboma, komanso kwa olamulira, musade nkhawa kuti mukadziteteza bwanji kapena mukanena chiyani.+ 12  Pakuti mzimu woyera+ udzakuphunzitsani mu ola lomwelo zoyenera kunena.”+ 13  Kenako wina mukhamulo anauza Yesu kuti: “Mphunzitsi, mundiuzireko m’bale wanga kuti andigawireko cholowa.” 14  Iye anamuuza kuti: “Munthu iwe, ndani anandiika ine kukhala woweruza+ kapena wogawa chuma chanu?” 15  Kenako anauza anthuwo kuti: “Khalani maso ndipo chenjerani ndi kusirira kwa nsanje kwamtundu uliwonse,+ chifukwa ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.”+ 16  Atatero anawauza fanizo, kuti: “Munda wa munthu wina wachuma unabereka bwino. 17  Choncho anayamba kudzifunsa kuti, ‘Ndichite chiyani tsopano, popeza ndilibe mosungira zokolola zangazi?’ 18  Ndiyeno anati, ‘Ndichita izi:+ Ndipasula nkhokwe zanga ndi kumanga zikuluzikulu, ndipo tirigu wanga yense ndi zinthu zanga zonse zabwino ndidzazitutira mmenemo.+ 19  Ndipo ndidzauza+ moyo wanga kuti: “Moyo wangawe, uli ndi zinthu zambiri zabwino mwakuti zisungika kwa zaka zambiri. Ungoti phee tsopano, ndipo udye, umwe ndi kusangalala.”’+ 20  Koma Mulungu anamuuza kuti, ‘Wopanda nzeru iwe, usiku womwe uno moyo wako adzaufuna.+ Nanga chuma chimene waunjikachi chidzakhala cha ndani?’+ 21  Umu ndi mmene zimakhalira kwa munthu amene wadziunjikira yekha chuma, koma amene sali wolemera kwa Mulungu.”+ 22  Kenako anauza ophunzira ake kuti: “Pa chifukwa chimenechi ndikukuuzani kuti, Lekani kudera nkhawa moyo wanu kuti mudzadya chiyani kapena kudera nkhawa matupi anu kuti mudzavala chiyani.+ 23  Pakuti moyo ndi wofunika kwambiri kuposa chakudya, ndipo thupi ndi lofunika kwambiri kuposa chovala. 24  Onetsetsani makwangwala,+ iwo safesa mbewu kapena kukolola. Alibe nyumba yosungiramo zinthu kapena nkhokwe, komatu Mulungu amawadyetsa. Kodi inu si ofunika kwambiri kuposa mbalame?+ 25  Ndani wa inu amene angatalikitse moyo wake pang’ono pokha* mwa kuda nkhawa?+ 26  Choncho ngati inu simungachite kanthu kochepaka, n’kuderanji nkhawa+ ndi zinthu zinazo? 27  Onetsetsani mmene maluwa amakulira.+ Iwo sagwira ntchito kapena kuwomba nsalu. Koma ndikukuuzani, Ngakhale Solomo mu ulemerero wake wonse sanavalepo zokongola ngati duwa lililonse mwa maluwa amenewa.+ 28  Tsopano ngati Mulungu amaveka chotero zomera zakutchire, zimene zimangokhalapo lero lokha, mawa n’kuzisonkhezera pamoto, kuli bwanji inu, achikhulupiriro chochepa inu! Ndithudi, iye adzakuvekani kuposa pamenepo.+ 29  Choncho lekani kudera nkhawa za chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa, ndipo siyani kuvutika mumtima.+ 30  Pakuti zonsezi ndi zinthu zimene anthu a mitundu ina a m’dzikoli amazifunafuna mwakhama, koma Atate wanu amadziwa kuti zinthu zonsezi n’zofunika kwa inu.+ 31  Koma inu, pitirizani kufunafuna ufumu wake, ndipo zinthu zimenezi zidzawonjezedwa kwa inu.+ 32  “Musaope,+ kagulu ka nkhosa+ inu, chifukwa Atate wanu wavomereza kukupatsani ufumu.+ 33  Gulitsani+ zinthu zanu ndi kupereka mphatso zachifundo.+ Dzipangireni zikwama za ndalama zomwe sizingathe, kutanthauza chuma chosatha kumwamba,+ kumene mbala singafikeko, ndipo njenjete* singawononge. 34  Pakuti kumene kuli chuma chanu, mitima yanunso idzakhala komweko.+ 35  “Mangani m’chiuno mwanu+ ndipo nyale+ zanu zikhale chiyakire. 36  Inuyo mukhale ngati anthu amene akuyembekezera kubwera kwa mbuye wawo+ kuchokera ku ukwati,+ kuti akafika ndi kugogoda+ amutsegulire mwamsanga. 37  Odala ndi akapolo amene mbuye wawo pofika adzawapeza akudikira!+ Ndithu ndikukuuzani, Iye adzamanga m’chiuno+ mwake ndi kuwakhazika patebulo kuti adye chakudya ndipo adzawatumikira.+ 38  Iwo ndi odala ndithu ngati atawapeza akudikirabe ngakhale atafika pa ulonda wachiwiri kapenanso wachitatu!*+ 39  Koma dziwani kuti mwininyumba atadziwa nthawi yobwera mbala, angakhale maso ndipo sangalole kuti mbala zithyole ndi kulowa m’nyumba mwake.+ 40  Inunso khalani okonzeka, chifukwa pa ola limene simukuliganizira, Mwana wa munthu adzafika.”+ 41  Kenako Petulo anati: “Ambuye, kodi mukunena fanizoli kwa ife tokha kapenanso kwa ena onse?” 42  Pamenepo Ambuye ananena kuti: “Ndani kwenikweni amene ali mtumiki woyang’anira nyumba wokhulupirika+ ndi wanzeru,+ amene mbuye wake adzamuika kuyang’anira gulu la atumiki ake, kuti aziwapatsa chakudya chokwanira pa nthawi yake?+ 43  Kapolo ameneyo ndi wodala, ngati mbuye wake pobwera adzam’peze akuchita zimenezo!+ 44  Ndithu ndikukuuzani, Adzamuika kukhala woyang’anira zinthu zake zonse.+ 45  Koma ngati kapoloyo anganene mumtima mwake kuti, ‘Mbuye wanga akuchedwa kubwera.’+ Ndiyeno n’kuyamba kumenya antchito anzake aamuna ndi aakazi, kudya, kumwa ndi kuledzera,+ 46  mbuye wa kapoloyo adzabwera pa tsiku limene iye sakuyembekezera, ndi pa ola limene sakulidziwa,+ ndipo adzam’patsa chilango choopsa ndi kum’patsa gawo pamodzi ndi anthu osakhulupirika.+ 47  Pa nthawiyo kapolo amene anadziwa zofuna za mbuye wake koma osakonzekera kubwera kwake, kapena osachita mogwirizana ndi zofuna za mbuye wakeyo, adzakwapulidwa zikoti zambiri.+ 48  Koma amene sanadziwe+ ndipo wachita zinthu zofunika kum’kwapula zikoti, adzam’kwapula zikoti zochepa.+ Inde, aliyense amene anapatsidwa zambiri, zambirinso zidzafunika kwa iye.+ Ndipo aliyense amene anthu anamuika kuyang’anira zinthu zochuluka, anthuwo adzafunanso zochuluka kwa iye.+ 49  “Ndinabwera kudzakoleza moto+ padziko lapansi, ndiye ngati motowo wayaka kale, chinanso n’chiyani chimene ndingafune? 50  Ndithudi pali ubatizo umene ndiyenera kubatizidwa nawo, ndipotu ndikuvutika kwambiri mumtima kufikira utatha!+ 51  Kodi mukuganiza kuti ndinabweretsa mtendere padziko lapansi? Ayi ndithu, koma ndinabwera kudzagawanitsa anthu.+ 52  Pakuti kuyambira tsopano, m’nyumba imodzi mudzakhala anthu asanu osemphana maganizo, atatu kutsutsana ndi awiri, awiri kutsutsana ndi atatu.+ 53  Iwo adzagawanika, bambo kutsutsana ndi mwana wake wamwamuna, ndipo mwana wamwamuna kutsutsana ndi bambo ake. Mayi kutsutsana ndi mwana wake wamkazi, ndipo mwana wamkazi kutsutsana ndi mayi ake. Mpongozi kutsutsana ndi mkazi wa mwana wake, ndipo mkazi wokwatiwa kutsutsana ndi apongozi ake aakazi.”+ 54  Kenako anauzanso khamu la anthulo kuti: “Mukaona mtambo ukukwera chakumadzulo, nthawi yomweyo mumanena kuti, ‘Kukubwera chimvula,’ ndipo chimabweradi.+ 55  Ndipo mukaona mphepo ya kum’mwera ikuwomba, mumanena kuti, ‘Lero kutentha kwambiri,’ ndipo zimachitikadi. 56  Onyenga inu! Mumatha kuzindikira maonekedwe a dziko lapansi ndi kuthambo. Nanga zimakukanikani bwanji kuzindikira tanthauzo la zimene zikuchitika pa nthawi ino?+ 57  N’chifukwa chiyani inuyo panokha simuzindikira chimene chili cholungama?+ 58  Mwachitsanzo, pamene wokusumira mlandu akupita nawe kwa wolamulira, yesetsa kuchitapo kanthu muli m’njira, kuti uthetse mlanduwo. Uchitepo kanthu kuti asakutengere kwa woweruza, ndi kutinso woweruzayo asakupereke kwa msilikali wa pakhoti, ndipo msilikaliyo n’kukuponya m’ndende.+ 59  Ndithu ndikukuuza, Sudzatulukamo kufikira utapereka kakhobidi kotsiriza kochepa mphamvu kwambiri.”+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 6.
Mawu ake enieni, “amene angatalikitse moyo wake ndi mkono umodzi.”
Mawu amene tawamasulira kuti “njenjete” amatanthauza mtundu wa kachilombo kotchedwa kadziwotche kooneka ngati gulugufe, kamene kamadya zovala ngati mmene njenjete imachitira.
Onani mawu a m’munsi pa Mt 14:25.