Genesis 37:1-36
37 Yakobo anakhalabe m’dziko la Kanani,+ kumene bambo ake anakhalako ngati mlendo.+
2 Nayi mbiri ya Yakobo.
Pamene Yosefe+ anali ndi zaka 17, tsiku lina anapita kokadyetsa nkhosa limodzi ndi abale ake.+ Pokhala wamng’ono, anali limodzi ndi ana a Biliha+ ndi ana a Zilipa,+ omwe anali akazi a bambo ake. Tsopano Yosefe anakauza bambo ake zoipa zimene abale ake anali kuchita.+
3 Isiraeli anali kum’konda kwambiri Yosefe kuposa ana ake ena onse,+ chifukwa anali mwana amene anam’bereka atakalamba. Chotero anam’soketsera mkanjo wamizeremizere wamanja aatali.+
4 Abale ake ataona kuti bambo awo anali kum’konda kwambiri Yosefe kuposa iwo onse, anayamba kudana naye,+ moti sankatha kulankhula naye mwamtendere.+
5 Pambuyo pake, Yosefe analota maloto ndi kuuza abale ake.+ Kwa iwo chinakhala chifukwa china chomudera.
6 Iye anawauza kuti: “Tamverani maloto amene ine ndinalota.+
7 Ndinalota tikumanga mitolo ya tirigu pakati pa munda. Mtolo wanga unadzuka n’kuima chilili. Mitolo yanunso inadzuka, ndipo inazungulira mtolo wanga n’kuyamba kuuweramira.”+
8 Pamenepo abale akewo anamufunsa kuti: “Kodi iweyo ndithu ukuganiza kuti ungadzakhale mfumu yathu?+ Moti ukuona kuti ungadzatilamulire ife?”+ Kwa iwo, maloto amenewa ndi mawu akewa anakhala chifukwa chinanso chomudera.
9 Tsiku linanso analota maloto ena, ndipo anakauza abale akewo kuti: “Leronso ndinalota maloto ena. Ndinalota dzuwa ndi mwezi ndiponso nyenyezi zokwanira 11 zikundigwadira.”+
10 Kenako anafotokozeranso malotowo bambo ake ndi abale akewo. Koma bambo ake anam’dzudzula kuti:+ “Kodi maloto walotawa akutanthauza chiyani? Kodi ineyo ndithu ndi mayi akowa, komanso abale akowa tidzagwada pansi pamaso pa iwe?”
11 Abale akewo anachita naye kaduka,+ koma bambo ake anasunga mawuwo.+
12 Tsopano abale ake aja anapita kokadyetsa nkhosa za bambo awo kufupi ndi ku Sekemu.+
13 Pambuyo pake, Isiraeli anauza Yosefe kuti: “Kodi abale ako sakudyetsa nkhosa cha ku Sekemu? Tabwera ndikutume kwa iwo.” Iye anati: “Chabwino bambo.”+
14 Ndiye Isiraeli anati: “Pita ukaone ngati abale ako ali bwino limodzi ndi nkhosa. Kenako ubwere udzandiuze.”+ Chotero, anamuuza kuti anyamuke kuchigwa cha Heburoni+ ndipo iye analowera ku Sekemu.
15 Ali pa ulendowo, munthu wina anakumana ndi Yosefe akungoyenda uku ndi uku kutchireko. Ndiyeno munthuyo anamufunsa kuti: “Kodi ukufunafuna chiyani?”
16 Iye anayankha kuti: “Ndikufunafuna abale anga. Tandiuzani chonde, Kodi iwo akudyetsera kuti nkhosa?”
17 Munthuyo anati: “Amenewo achoka. Ndinawamva akunena kuti, ‘Tiyeni tipite ku Dotana.’” Pamenepo Yosefe anawalondolabe abale akewo mpaka anakawapeza ku Dotanako.
18 Iwo anamuonera patali akubwera, ndipo asanafike pafupi anayamba kupangana chiwembu choti amuphe.+
19 Chotero anauzana kuti: “Tamuonani wolota uja.+ Uyo akubwera apoyo!
20 Tiyeni timuphe, timuponye m’chitsime chopanda madzi,+ ndipo tikanene kuti chilombo cholusa chamudya.+ Tidzaone kuti chidzachitike n’chiyani ndi maloto ake aja.”
21 Rubeni atamva zimenezo anayesa kum’landitsa kwa iwo.+ Iye anati: “Ayi, tisachite kuwononga moyo wake.”+
22 Ndipo anapitiriza kuwauza kuti: “Musakhetse magazi ayi.+ Muponyeni m’chitsime chopanda madzichi kutchire kuno, musamuvulaze.”+ Cholinga chake chinali chakuti amupulumutse kwa iwo ndi kum’bwezera kwa bambo ake.
23 Choncho Yosefe atangofika kwa abale akewo, anamuvula mkanjo wake wamizeremizere uja, womwe anavala.+
24 Atatero, anamutenga n’kukamuponya m’chitsimecho.+ Pa nthawiyo chitsimecho chinali chopanda madzi.
25 Ndiyeno anakhala pansi kuti adye chakudya.+ Koma pamene anakweza maso, anaona gulu la apaulendo la Aisimaeli.+ Anali kuchokera ku Giliyadi, ndipo ngamila zawo zinali zitanyamula mafuta onunkhira a labidanamu ndi a basamu, komanso makungwa a utomoni wonunkhira.+ Apaulendowo anali kupita ku Iguputo.
26 Yuda atawaona, anauza abale ake kuti: “Tipindulapo chiyani tikapha m’bale wathu ndi kubisa imfa yake?+
27 Tiyeni timugulitse kwa Aisimaeliwa,+ tisam’pweteke ayi.+ Ndipotu ndi m’bale wathu ameneyu, magazi* athu enieni.” Atamva mawuwa, iwo anamvera m’bale wawoyo.+
28 Tsopano amuna amalonda achimidiyani+ aja anali kudutsa mumsewu. Pamenepo abale a Yosefe anamutulutsa m’chitsimemo+ n’kumugulitsa kwa Aisimaeliwo. Anamugulitsa ndalama zasiliva 20,+ ndipo iwo anapita naye ku Iguputo.
29 Pambuyo pake, Rubeni anabwerera kuchitsime kuja, koma anakapeza kuti Yosefe mulibe m’chitsimemo. Ataona choncho, anang’amba zovala zake.+
30 Atabwerera kwa abale ake aja, anafuula kuti: “Mwana ujatu kulibe! Kalanga ine, ndilowera kuti ine?”+
31 Tsopano iwo anatenga mkanjo wa Yosefe uja, n’kupha mbuzi yamphongo, n’kuviika mkanjowo mobwerezabwereza m’magazi a mbuziyo.+
32 Kenako, iwo anatumiza mkanjo wamizeremizere uja kwa bambo awo. Atafika nawo anati: “Tapeza mkanjo uwu. Chonde, uonetsetseni+ kuti muone ngati uli mkanjo wa mwana wanu kapena ayi.”+
33 Bambo awo anauyang’anitsitsa mkanjowo. Ndiyeno anafuula kuti: “Kalanga ine! Mkanjowu ndi wa mwana wanga! Chilombo cholusa chamudya basi mwana wanga.+ Wakhadzulidwa+ ndithu mwana wanga Yosefe!”
34 Pamenepo Yakobo anang’amba zovala zake, n’kuvala chiguduli* m’chiuno mwake, ndipo anamulira mwana wake masiku ambiri.+
35 Ana ake onse aamuna ndi aakazi anali kupita kukam’tonthoza,+ koma iye anali kukana kutonthozedwa. Anali kunena kuti:+ “Ayi! Ndidzalira mpaka kutsikira ku Manda* kumene kuli mwana wanga.” Ndipo bambo akewo anapitiriza kumulira.
36 Amidiyani aja anakagulitsa Yosefe ku Iguputo kwa Potifara. Potifara anali nduna ya panyumba ya Farao,+ ndiponso anali mkulu wa asilikali olondera mfumu.+