Genesis 26:1-35
26 Tsopano m’dzikomo munagwanso njala, kuwonjezera pa njala yoyamba ija imene inagwa m’masiku a Abulahamu.+ Choncho Isaki anapita kwa Abimeleki, mfumu ya Afilisiti, ku Gerari.+
2 Ndiyeno Yehova anaonekera kwa iye,+ n’kumuuza kuti, “Usatsikire ku Iguputo. Umange mahema ako m’dziko limene ndikusonyeze.+
3 Ukhale ngati mlendo m’dzikoli,+ ndipo ndidzapitiriza kukhala nawe ndi kukudalitsa, chifukwa mayiko onsewa ndidzawapereka kwa iwe ndi kwa mbewu yako.+ Ndidzakwaniritsa lumbiro limene ndinalumbirira Abulahamu bambo ako.+
4 ‘Ndidzachulukitsa mbewu yako ngati nyenyezi zakumwamba, ndipo mayiko onsewa ndidzawapereka kwa mbewu yako.+ Mitundu yonse ya padziko lapansi idzapeza madalitso*+ ndithu kudzera mwa mbewu yako.’
5 Zidzatero chifukwa Abulahamu anamvera mawu anga, ndipo anachita zofuna zanga ndi kusunga malamulo anga onse.”+
6 Chotero Isaki anapita kukakhala ku Gerari.+
7 Anthu a kumeneko anali kufunsa za mkazi wake, ndipo iye anali kuwayankha kuti, “Ndi mlongo wanga.”+ Anali kuopa kunena kuti: “Ndi mkazi wanga,” chifukwa malinga ndi kunena kwake, anati: “Anthu a kuno andipha chifukwa cha Rabeka,” pakuti mkaziyo anali wokongola mochititsa kaso.+
8 Patapita nthawi ali kumeneko, Abimeleki mfumu ya Afilisiti anali kuyang’ana pawindo, ndipo anaona Isaki akucheza mwachikondi ndi mkazi wake Rabeka.+
9 Nthawi yomweyo Abimeleki anaitanitsa Isaki n’kumufunsa kuti: “Ameneyu ndi mkazi wako, eti? Nanga n’chifukwa chiyani unali kunena kuti, ‘Ndi mlongo wanga’?” Ndiyeno Isaki anayankha kuti: “Ndinali kunena choncho poopa kuti angandiphe chifukwa cha iye.”+
10 Koma Abimeleki anapitiriza kuti: “N’chifukwa chiyani watichitira zoterezi?+ Pakanangopita kanthawi munthu wina akanagona naye mkazi wakoyu, ndipo ukanatipalamulitsa.”+
11 Pamenepo Abimeleki analamula anthu ake onse kuti: “Aliyense amene akhudze munthuyu ndiponso mkazi wake, aphedwa.”
12 Zitatero, Isaki anayamba kubzala mbewu m’dzikomo.+ M’chaka chimenechi anakolola zochuluka moti pa mbewu zimene anabzala, anakolola zochuluka kuwirikiza nthawi 100,+ popeza Yehova anali kum’dalitsa.+
13 Patapita nthawi, Isaki anakhala wolemera, ndipo chuma chake chinapitiriza kuchuluka mpaka anakhala wolemera kwambiri.+
14 Iye anakhala ndi nkhosa ndi ng’ombe zankhaninkhani. Anakhalanso ndi antchito ochuluka kwambiri,+ moti Afilisitiwo anayamba kum’chitira kaduka.+
15 Zitsime zonse zimene antchito a Abulahamu bambo ake anakumba m’masiku a bambo akewo,+ Afilisiti anazifotsera ndi dothi.+
16 Pamapeto pake, Abimeleki anauza Isaki kuti: “Utichokere kwathu kuno, chifukwa wakhala munthu wamphamvu kwambiri kuposa ifeyo.”+
17 Choncho Isaki anachoka kumeneko n’kukamanga mahema ake m’chigwa* cha Gerari,+ n’kukhazikika kumeneko.
18 Kumeneko, Isaki anafukulanso zitsime za madzi zimene zinakumbidwa m’masiku a Abulahamu bambo ake. Afilisiti anafotsera zitsimezo Abulahamu atamwalira,+ ndipo iye anazitchanso mayina amene bambo ake anazipatsa.+
19 Antchito a Isaki anayamba kukumba m’chigwacho ndipo anapeza chitsime cha madzi abwino.
20 Koma abusa a ku Gerari anayamba kukangana ndi abusa a Isaki,+ kuti: “Ndi madzi athu amenewa!” Choncho iye anatcha chitsimecho Eseke,* chifukwa iwo anakangana naye.
21 Kenako iwo anakumbanso chitsime china, n’kukangananso za chitsimecho. Chitsimechi iye anachitcha Sitina.
22 Pambuyo pake, anasamukako kumeneko, n’kukakumbanso chitsime kwina.+ Koma pa chitsimechi, sanakanganepo. Chotero iye anachitcha Rehoboti,* n’kunena kuti: “Chifukwa chake n’chakuti, tsopano Yehova watipatsa malo okwanira,+ ndipo watichulukitsa m’dziko lino.”+
23 Kenako iye anachokanso kumeneko, n’kukwezeka mtunda kupita ku Beere-seba.+
24 Usiku umenewo, Yehova anaonekera kwa iye ndipo anamuuza kuti: “Ine ndine Mulungu wa Abulahamu bambo ako.+ Usaope,+ chifukwa ndili nawe. Ndidzakudalitsa ndi kuchulukitsa mbewu yako chifukwa cha Abulahamu mtumiki wanga.”+
25 Kumeneko Isaki anamanga guwa lansembe n’kuitana pa dzina la Yehova.+ Anamanganso mahema ake,+ ndipo antchito ake anakumba chitsime kumeneko.
26 Patapita nthawi, Abimeleki anafika kwa iye kuchokera ku Gerari. Anafika limodzi ndi Ahuzati bwenzi lake lapamtima, komanso Fikolo mkulu wa asilikali ake.+
27 Pamenepo Isaki anawafunsa kuti: “Kodi n’chifukwa chiyani mwabwera kwa ine? Si paja inu munandida ine ndi kundipitikitsa kwanu kuja?”+
28 Koma iwo anayankha kuti: “Ife taona kuti ndithu Yehova ali nawe.+ Choncho tinaganiza zokupempha kuti, ‘Chonde, tiye tilumbirirane,+ iwe ndi ife, ndipo tichite nawe pangano.+
29 Tilumbirirane kuti sudzatichitira choipa chilichonse, pakuti ifenso sitinakukhudze. Tinakuchitira zabwino zokhazokha, mwa kukuchotsa kwathu mwamtendere.+ Tsopano Yehova wakudalitsa.’”+
30 Pamenepo Isaki anawakonzera phwando, ndipo iwo anadya ndi kumwa.+
31 M’mawa mwake, analawirira kudzuka n’kulumbiritsana.+ Kenako Isaki anatsanzikana nawo ndipo iwo anachoka kwa iye mwamtendere.+
32 Pa tsiku limenelo, antchito a Isaki anafika kwa iye n’kumuuza zokhudza chitsime chimene anakumba.+ Anamuuza kuti: “Madzi tawapeza.”
33 Chotero chitsimecho anachitcha Siba.* Ndiye chifukwa chake dzina la mzindawo ndi Beere-seba,+ mpaka lero.
34 Esau atakwanitsa zaka 40, anakwatira Yuditi mwana wa Beeri, Mhiti. Anakwatiranso Basemati mwana wa Eloni, Mhiti.+
35 Akaziwo anabweretsa chisoni kwa Isaki ndi Rabeka.+
Mawu a M'munsi
^ Mawu achiheberi amene tawamasulira kuti “chigwa” angatanthauze chigwa chimene mumadutsa mtsinje, ndipo angatanthauzenso mtsinje weniweniwo. Chigwa choterocho nthawi zambiri chimakhala chouma koma nthawi zina mumadutsa madzi ambiri.
^ Dzina lakuti “Eseke” limatanthauza “Mkangano.”
^ Dzina lakuti “Rehoboti” limatanthauza “Malo Aakulu.”
^ Dzina lakuti “Siba” limatanthauza “Lumbiro” kapena “7.”