Ekisodo 6:1-30
6 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Tsopano uona zimene ndichite kwa Farao.+ Chifukwa cha dzanja lamphamvu, iye awalola kuchoka, ndipo chifukwa cha dzanja lamphamvu awatulutsa m’dziko lake.”+
2 Mulungu ananenanso kwa Mose kuti: “Ine ndine Yehova.+
3 Ndinali kuonekera kwa Abulahamu,+ Isaki+ ndi Yakobo+ monga Mulungu Wamphamvuyonse.+ Koma za dzina langa lakuti Yehova,+ ine sindinadzidziwikitse+ kwa iwo.
4 Ndinakhazikitsa pangano langa ndi iwo kuti ndidzawapatsa dziko la Kanani, dziko limene anali kukhalamo monga alendo.+
5 Motero ineyo ndamva kubuula kwa ana a Isiraeli,+ amene Aiguputo akuwagwiritsa ntchito yaukapolo, ndipo ndikukumbukira pangano langa.+
6 “Choncho uwauze ana a Isiraeli kuti, ‘Ine ndine Yehova. Ndithu, ndidzakutulutsani mu Iguputo ndi kukuchotserani goli lawo, ndipo ndidzakulanditsani ku ukapolo wawo.+ Ndidzakuwombolani ndi dzanja langa lotambasula komanso ndi ziweruzo zamphamvu.+
7 Chotero ndidzakutengani kukhala anthu anga,+ ndi kukusonyezani kuti ndine Mulungu.+ Inuyo mudzadziwadi kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndidzakutulutsani mu Iguputo, ndi kukuchotserani goli lawo.+
8 Ine ndidzakulowetsani m’dziko limene ndinalumbirira+ Abulahamu, Isaki ndi Yakobo, nditakweza dzanja langa. Ndidzakupatsani dzikolo kukhala lanu.+ Ine ndine Yehova.’”+
9 Kenako Mose analankhula mawu amenewa kwa ana a Isiraeli, koma iwo sanamvere Mose chifukwa chokhumudwa ndiponso chifukwa cha ntchito yowawa ya ukapolo.+
10 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti:
11 “Pita kwa Farao, mfumu ya Iguputo,+ ukamuuze kuti alole ana a Isiraeli kutuluka m’dziko lake.”+
12 Koma Mose anayankha Yehova kuti: “Komatu ana a Isiraeli sanandimvere,+ nanga Farao akandimvera bwanji?+ Pakuti ndimalankhula movutikira.”*+
13 Koma Yehova anapitirizabe kuuza Mose ndi Aroni, kuti apereke lamulo kwa ana a Isiraeli ndi kwa Farao, mfumu ya Iguputo, kuti atulutse ana a Isiraeli m’dziko la Iguputo.+
14 Tsopano awa ndiwo atsogoleri a nyumba ya makolo a Aisiraeli. Ana aamuna a Rubeni, yemwe anali mwana woyamba kubadwa wa Isiraeli,+ anali Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karami.+ Amenewa ndiwo mabanja a fuko la Rubeni.+
15 Ndipo ana aamuna a Simiyoni anali Yemueli, Yamini, Ohadi, Yakini, Zohari ndi Shauli, mwana amene anabereka ndi mkazi wachikanani.+ Amenewa ndiwo mabanja a fuko la Simiyoni.+
16 Awa ndi mayina a ana aamuna a Levi,+ malinga ndi mzere wobadwira wa makolo awo:+ Gerisoni, Kohati ndi Merari.+ Ndipo Levi anakhala ndi moyo zaka 137.
17 Ana a Gerisoni anali Libini ndi Simeyi,+ malinga ndi mzere wobadwira wa makolo awo.+
18 Ndipo ana a Kohati anali Amuramu, Izara, Heburoni ndi Uziyeli.+ Kohati anakhala ndi moyo zaka 133.
19 Ndipo ana aamuna a Merari anali Mali ndi Musi.+
Amenewa ndiwo anali mabanja a Alevi malinga ndi mzere wobadwira wa makolo awo.+
20 Tsopano Amuramu anatenga Yokebedi, mlongo wa bambo ake, kukhala mkazi wake.+ Ndipo Yokebedi anam’berekera Amuramu, Aroni ndi Mose.+ Amuramu anakhala ndi moyo zaka 137.
21 Ndipo ana aamuna a Izara anali Kora,+ Nefegi ndi Zikiri.
22 Ndipo ana aamuna a Uziyeli anali Misayeli, Elizafana ndi Sitiri.+
23 Aroni anatenga Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wake wa Naasoni,+ kukhala mkazi wake. Ndipo Eliseba anam’berekera Nadabu, Abihu, Eleazara ndi Itamara.+
24 Ndipo ana aamuna a Kora anali Asiri, Elikana ndi Abiasafu.+ Amenewa ndiwo anali mabanja a Kora.+
25 Ndipo Eleazara mwana wa Aroni,+ anatenga mwana wamkazi wa Putieli kukhala mkazi wake. Ndipo iye anam’berekera Pinihasi.+
Amenewa ndiwo atsogoleri a mabanja a m’fuko la Levi, malinga ndi mzere wobadwira wa makolo awo.+
26 Umenewu ndiwo mzere wa Aroni ndi Mose, amene Yehova anawauza kuti:+ “Tulutsani ana a Isiraeli m’dziko la Iguputo malinga ndi makamu awo.”+
27 Mose ndi Aroni amenewa ndi amene analankhula kwa Farao mfumu ya Iguputo, kuti atulutse ana a Isiraeli mu Iguputo.+
28 Choncho pa tsiku limene Yehova analankhula ndi Mose m’dziko la Iguputo,+
29 Yehova anamuuza kuti: “Ine ndine Yehova.+ Zonse zimene ndikukuuza, ukauze Farao mfumu ya Iguputo.”
30 Pamenepo Mose anauza Yehova kuti: “Komatu ndimalankhula movutikira, ndiye Farao akandimvera bwanji?”+
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “Ndine wosadulidwa milomo,” ngati kuti milomo yake inali ndi khungu lolendewera, moti inali yaitali kwambiri ndi yochindikala, yomulepheretsa kulankhula bwinobwino.