Ekisodo 13:1-22
13 Yehova analankhulanso ndi Mose kuti:
2 “Ndipatulireni mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa,* wa munthu ndi wa chiweto, pakati pa ana a Isiraeli. Ameneyu ndi wanga.”+
3 Chotero Mose anauza anthuwo kuti: “Muzikumbukira tsiku lino limene munatuluka mu Iguputo,+ m’nyumba ya ukapolo, chifukwa Yehova anakutulutsani mmenemo ndi mphamvu ya dzanja lake.+ Choncho musadye chilichonse chokhala ndi chofufumitsa.+
4 Mukutuluka lero m’mwezi wa Abibu.*+
5 Ndipo Yehova akadzakulowetsani m’dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, Ahivi ndi Ayebusi,+ dziko loyenda mkaka ndi uchi,+ limene analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani,+ pamenepo muzidzachita mwambo uwu m’mwezi uno.
6 Muzidzadya mikate yosafufumitsa masiku 7,+ ndipo pa tsiku la 7 limenelo muzidzachita chikondwerero kwa Yehova.+
7 Muzidzadya mikate yopanda chofufumitsa kwa masiku 7.+ Musamadzapezeke ndi chilichonse chokhala ndi chofufumitsa.+ Mtanda wa ufa wokanda wokhala ndi chofufumitsa usamadzapezeke pena paliponse m’dziko lanu.+
8 Ndiyeno pa tsiku limenelo udzauze mwana wako kuti, ‘Ndikuchita izi chifukwa cha zimene Yehova anandichitira potuluka mu Iguputo.’+
9 Chotero mwambo umenewu uzikukumbutsani zimene zinachitikazi ngati chizindikiro cholembedwa padzanja lanu ndi pamphumi panu,+ kuti chilamulo cha Yehova chikhale pakamwa panu.+ Zizikhala choncho chifukwa Yehova anakutulutsani mu Iguputo ndi mphamvu ya dzanja lake.+
10 Ndipo muzisunga lamulo ili pa nthawi yake yoikidwiratu chaka ndi chaka.+
11 “Yehova akadzakulowetsani m’dziko la Akanani,+ monga momwe analumbirira kwa inu ndi kwa makolo anu,+ akadzakupatsani dzikolo,
12 pamenepo muzidzapereka kwa Yehova mwana aliyense woyamba kubadwa,+ ndi mwana aliyense wa ziweto zanu woyamba kubadwa.+ Chachimuna chilichonse n’cha Yehova.+
13 Mwana aliyense woyamba kubadwa wa bulu muzimuwombola ndi nkhosa, koma ngati simungamuwombole, muzimupha mwa kum’thyola khosi.+ Ndipo aliyense woyamba kubadwa mwa ana anu aamuna muzimuwombola.+
14 “Ndiyeno m’tsogolo, mwana wanu akadzakufunsani+ kuti, ‘Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?’ Mudzamuyankhe kuti, ‘Yehova anatitulutsa ndi mphamvu ya dzanja lake mu Iguputo,+ m’nyumba ya ukapolo.+
15 Koma Farao anaumitsa mtima wake posalola kuti ife tichoke,+ motero Yehova anapha mwana woyamba kubadwa aliyense m’dziko la Iguputo,+ kuyambira mwana woyamba kubadwa wa munthu mpaka mwana woyamba kubadwa wa nyama.+ N’chifukwa chake tikupereka nsembe kwa Yehova ana onse a nyama oyamba kubadwa,+ ndipo tikuwombola mwana woyamba kubadwa aliyense mwa ana athu.’+
16 Mwambo umenewu ukhale ngati chizindikiro cholembedwa padzanja lanu ndi chomanga pamphumi panu,*+ chifukwa Yehova anatitulutsa mu Iguputo ndi mphamvu ya dzanja lake.”+
17 Farao atalola kuti ana a Isiraeli apite, Mulungu sanawadutsitse m’dziko la Afilisiti ngakhale kuti kunali kufupi, pakuti Mulungu anati: “Anthu angataye mtima atakumana ndi nkhondo ndipo angabwerere ku Iguputo.”+
18 Chotero Mulungu anachititsa ana a Isiraeli kuyenda njira yaitali yodutsa m’chipululu chapafupi ndi Nyanja Yofiira.+ Koma iwo potuluka m’dziko la Iguputo, anayenda mwa dongosolo lomenyera nkhondo.+
19 Choncho Mose anatenga mafupa a Yosefe chifukwa Yosefe analumbiritsa ana a Isiraeli, kuti: “Ndithudi, Mulungu adzakukumbukirani,+ ndipo pochoka kuno mudzatenge mafupa anga.”+
20 Motero ananyamuka ku Sukoti n’kukamanga msasa ku Etamu m’malire a chipululu.+
21 Yehova anali kuyenda patsogolo pawo mumtambo woima njo ngati chipilala powatsogolera usana,+ ndipo usiku anali kuwatsogolera m’moto woima njo ngati chipilala kuti uziwaunikira, kuti apitirizebe ulendo usana ndi usiku.+
22 Choncho mtambowo sunachoke patsogolo pa anthuwo usana, ngakhalenso motowo sunachoke usiku.+
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “Mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa, wotsegula mimba ya mayi aliyense.”
^ Onani Zakumapeto 13.
^ Mawu ake enieni, “pakati pa maso anu.”