Chivumbulutso 2:1-29

2  “Kwa mngelo+ wa mpingo wa ku Efeso,+ lemba kuti: Izi ndi zimene akunena wonyamula nyenyezi 7+ m’dzanja lake lamanja, woyenda pakati pa zoikapo nyale 7 zagolide.+  ‘Ndikudziwa ntchito zako,+ khama lako, ndi kupirira kwako, ndiponso kuti sungalekelere anthu oipa. Iwe unayesanso+ anthu amene amadzitcha atumwi+ pamene sanali atumwi, ndipo unapeza kuti ndi onama.  Umaonetsanso kupirira,+ ndipo walimbana ndi mavuto osiyanasiyana chifukwa cha dzina langa,+ koma sunafooke.+  Komabe, ndakupeza ndi mlandu wakuti wasiya chikondi chimene unali nacho poyamba.+  “‘Choncho, kumbukira malo amene unali usanagwe, lapa+ ndi kuchita ntchito za poyamba. Ngati sutero, ndikubwera kwa iwe,+ ndipo ndidzachotsa choikapo nyale chako+ pamalo ake ngati sulapa.  Komabe, pali chinthu chimodzi chimene ukuchita bwino: Umadana+ ndi ntchito za mpatuko wa Nikolao,+ zimenenso ine ndimadana nazo.  Ali ndi makutu amve zimene mzimu+ ukunena ku mipingo kuti: Wopambana pa nkhondo,+ ndidzamulola kudya za mumtengo wa moyo,+ umene uli m’paradaiso wa Mulungu.’  “Kwa mngelo+ wa mpingo wa ku Simuna lemba kuti: Izi ndi zimene akunena ‘Woyamba ndi Wotsiriza,’+ amene anafa n’kukhalanso ndi moyo.+  ‘Ndikudziwa masautso ako ndi umphawi wako, koma ndiwe wolemera.+ Ndikudziwanso za kutonza kwa odzitcha Ayudawo,+ pamene si Ayuda, koma ndiwo sunagoge wa Satana.+ 10  Usachite mantha ndi mavuto amene ukumane nawo.+ Taona! Mdyerekezi+ adzapitiriza kuponya m’ndende ena a inu, kuti muyesedwe mpaka pamapeto,+ ndipo mudzakhala m’masautso+ masiku 10. Sonyeza kukhulupirika kwako mpaka imfa,+ ndipo ndidzakupatsa mphoto* ya moyo.+ 11  Ali ndi makutu amve+ zimene mzimu+ ukunena ku mipingo kuti: Wopambana pa nkhondo,+ sadzakhudzidwa ndi imfa yachiwiri.’+ 12  “Kwa mngelo wa mpingo wa ku Pegamo lemba kuti: Izi ndi zimene akunena amene ali ndi lupanga lalitali, lakuthwa konsekonse.+ 13  ‘Ndikudziwa kumene ukukhala. Ukukhala kumene kuli mpando wachifumu wa Satana. Koma ukugwirabe mwamphamvu dzina langa,+ ndipo sunakane kuti umakhulupirira ine.+ Sunakane ngakhale m’masiku a Antipa mboni yanga,+ wokhulupirika wanga uja, amene anaphedwa+ pambali panu, kumene Satana akukhala. 14  “‘Koma ngakhale zili choncho, ndakupeza ndi milandu ingapo. Iwe kumeneko uli ndi anthu olimbikira chiphunzitso cha Balamu,+ amene anaphunzitsa Balaki+ kuikira ana a Isiraeli chopunthwitsa kuti adye zoperekedwa nsembe kwa mafano ndi kuchita dama.+ 15  Ndiponso uli ndi olimbikira chiphunzitso cha mpatuko wa Nikolao.+ 16  Choncho ulape.+ Ngati sulapa, ndikubwera kwa iwe msanga, ndipo ndidzamenyana+ nawo ndi lupanga lalitali la m’kamwa mwanga.+ 17  “‘Ali ndi makutu amve zimene mzimu ukunena ku mipingo kuti:+ Wopambana pa nkhondo+ ndidzamupatsa ena mwa mana+ obisika. Ndidzamupatsanso mwala woyera wolembedwa dzina latsopano+ limene wina aliyense sakulidziwa kupatulapo wolandira yekhayo.’+ 18  “Kwa mngelo wa mpingo wa ku Tiyatira+ lemba kuti: Izi ndi zimene Mwana+ wa Mulungu akunena, iye amene maso ake ali ngati lawi la moto,+ ndipo mapazi ake ali ngati mkuwa woyengedwa bwino.+ 19  ‘Ndikudziwa ntchito zako, chikondi chako,+ chikhulupiriro chako, utumiki wako, ndi kupirira kwako. Ndikudziwanso kuti ntchito zako+ zapanopa n’zambiri kuposa zoyamba zija.+ 20  “‘Komabe, ndakupeza ndi mlandu uwu. Walekerera mayi uja Yezebeli,+ amene amadzitcha mneneri. Iye amaphunzitsa+ ndi kusocheretsa akapolo anga+ kuti azichita dama+ ndi kudya zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano.+ 21  Ndamupatsa nthawi kuti alape,+ koma sakufuna kulapa dama* lake.+ 22  Taona! Ndatsala pang’ono kumudwalitsa kwambiri, ndipo ochita naye chigololo ndiwaponya m’masautso aakulu, kupatulapo ngati atalapa ntchito zawo zofanana ndi za mayiyo. 23  Ana ake ndidzawapha ndi mliri wakupha, moti mipingo yonse idzadziwa kuti ineyo ndiye amene ndimafufuza impso ndi mitima, ndipo ndidzabwezera mmodzi ndi mmodzi wa inu malinga ndi ntchito zake.+ 24  “‘Komabe, kwa ena nonse amene muli ku Tiyatira, nonsenu amene mulibe chiphunzitso chimenechi, amene simudziwa chilichonse chokhudza zinthu zimene amazitcha “zinthu zozama za Satana,”+ ndikuti: Sindikusenzetsani katundu wina wolemera.+ 25  Gwirani mwamphamvu zomwe zija, zimene muli nazo,+ mpaka nditabwera. 26  Ndipo amene wapambana pa nkhondo ndi kutsatira zochita zanga kufikira mapeto,+ ndidzamupatsa ulamuliro pa mitundu ya anthu.+ 27  Iyeyo adzakusa anthu ndi ndodo yachitsulo,+ ngati imenenso ine ndailandira kwa Atate wanga. Anthuwo adzaphwanyidwaphwanyidwa ngati mbiya zadothi.+ 28  Ndidzamupatsanso nthanda.*+ 29  Amene ali ndi makutu amve zimene mzimu+ ukunena ku mipingo.’+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “chisoti chachitsulo chooneka ngati nkhata.”
Onani Zakumapeto 7.
“Nthanda” ndi nyenyezi yomalizira kutuluka imene imaonekera dzuwa likangotsala pang’ono kutuluka.