Aroma 8:1-39

8  Chotero amene ali ogwirizana ndi Khristu Yesu alibe mlandu.+  Pakuti chilamulo+ cha mzimu+ umene umapatsa moyo+ mwa Khristu Yesu chakumasulani+ ku chilamulo cha uchimo ndi cha imfa.+  Mulungu anatsutsa uchimo mwa kugwiritsa ntchito thupi potumiza Mwana wake+ m’thupi lofanana ndi lauchimo+ kuti athane ndi uchimo.+ Pakuti Chilamulo sichinathe kuchita zimenezi+ pokhala chofooka+ chifukwa cha thupi.  Mulungu anachita izi kuti ife amene tikuyenda motsatira za mzimu,+ osati motsatira zofuna za thupi, tikwaniritse miyezo yolungama ya Chilamulo.+  Chifukwa otsatira zofuna za thupi amaika maganizo awo pa zinthu za thupi,+ koma otsatira za mzimu amaika maganizo awo pa zinthu za mzimu.+  Pakuti kuika maganizo pa zinthu za thupi kumabweretsa imfa,+ koma kuika maganizo pa zinthu za mzimu+ kumabweretsa moyo ndi mtendere,  chifukwa kuika maganizo pa zinthu za thupi ndiko udani+ ndi Mulungu, popeza thupi siligonjera+ chilamulo cha Mulungu, ndipotu kunena zoona, silingachigonjere.  Choncho, otsatira zofuna za thupi+ sangakondweretse Mulungu.  Komabe, inu mukutsatira za mzimu,+ osati za thupi, ngati mzimu wa Mulungu ukukhaladi mwa inu.+ Ngati wina alibe mzimu wa Khristu,+ ameneyu si wa Khristu. 10  Koma ngati Khristu ali wogwirizana ndi inu,+ ngakhale kuti thupi ndi lakufa chifukwa cha uchimo, mzimu ndiwo moyo+ chifukwa cha chilungamo. 11  Chotero, mzimu wa amene anaukitsa Yesu kwa akufa ukakhala mwa inu, iye amene anaukitsa Khristu Yesu kwa akufa+ adzachititsanso matupi anu otha kufawo kukhala ndi moyo+ mwa mzimu wake umene ukukhala mwa inu. 12  Choncho abale, tili ndi ngongole, osati kwa thupi kuti tizikhala motsatira zofuna za thupi.+ 13  Pakuti ngati mukukhala motsatira zofuna za thupi, ndiye kuti mosakayikira mudzafa.+ Koma mukapha zochita za thupi+ mwa mzimu, mudzakhala ndi moyo. 14  Onse amene akutsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu, amenewa ndiwo ana a Mulungu.+ 15  Popeza simunalandire mzimu wa ukapolo woyambitsanso mantha,+ koma munalandira mzimu+ wakuti mukhale ana,+ umene timafuula nawo kuti: “Abba,*+ Atate!” 16  Pakuti mzimuwo+ umachitira umboni+ limodzi ndi mzimu wathu+ kuti ndife ana a Mulungu.+ 17  Chotero, ngati tili ana, tilinso olandira cholowa: Olandira cholowa a Mulungu, komanso olandira cholowa anzake+ a Khristu, malinga ngati tivutika+ naye limodzi kuti tikalandire ulemerero limodzi ndi iye.+ 18  Ndiye chifukwa chake ndikuona kuti masautso+ amene tili nawo tsopano si kanthu powayerekeza ndi ulemerero+ umene udzaonekere kudzera mwa ife. 19  Pakuti chilengedwe+ chikudikira mwachidwi+ nthawi imene ulemelero wa ana a Mulungu udzaonekere.+ 20  Popeza chilengedwe chinaperekedwa ku mkhalidwe wopanda pake,+ osati mwa kufuna kwake koma kudzera mwa iye amene anachipereka, pa maziko a chiyembekezo+ 21  chakuti chilengedwecho+ chidzamasulidwa+ ku ukapolo wa kuvunda n’kukhala ndi ufulu waulemerero wa ana a Mulungu. 22  Pakuti tikudziwa kuti chilengedwe chonse chikubuula limodzi ndi kumva zowawa mpaka pano. 23  Si zokhazo ayi, komanso ifeyo amene tili ndi zipatso zoyambirira+ zomwe ndi mzimu, tikubuula+ mumtima mwathu pamene tikudikira ndi mtima wonse kuti titengedwe kukhala ana a Mulungu,+ kumasulidwa ndi dipo* kuti tituluke m’matupi athu. 24  Pakuti tinapulumutsidwa tili ndi chiyembekezo chimenechi,+ koma chimene chikuyembekezedwa chikaoneka sichikhalanso choyembekezedwa, chifukwa munthu akaona chinthu chimene anali kuchiyembekezera, kodi amachiyembekezanso? 25  Koma ngati tikuyembekezera+ chimene sitikuchiona,+ timachidikirabe mopirira.+ 26  Mofanana ndi zimenezi, mzimu+ umatithandiza pa zofooka zathu.+ Pakuti chimene tiyenera kupempherera monga mmene tiyenera kupemphera sitikuchidziwa,+ koma mzimu+ umachonderera m’malo mwathu ndi madandaulo amene sitinathe kuwafotokoza. 27  Koma iye amene amasanthula mitima+ amadziwa zimene mzimu ukutanthauza,+ chifukwa umachonderera m’malo mwa oyera mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.+ 28  Tikudziwa tsopano kuti Mulungu amagwirizanitsa zochita zake zonse+ pofuna kupindulitsa amene amakonda Mulungu, anthu oitanidwa mogwirizana ndi cholinga chake.+ 29  Amatero chifukwa amene anawadziwa choyamba+ anawasankhiratu+ kuti adzakhale ofanana+ ndi Mwana wake,+ kuti iye akhale woyamba kubadwa+ pakati pa abale ake ambiri.+ 30  Ndiponso, amene anawasankhiratu+ ndi amenenso anawaitana,+ ndipo amene anawaitanawo ndi amenenso anawayesa olungama.+ Kenako amene anawayesa olungama ndi amenenso anawapatsa ulemerero.+ 31  Ndiye tinene kuti chiyani pa zinthu zimenezi? Ngati Mulungu ali kumbali yathu, ndani adzatsutsana nafe?+ 32  Iye amene sanaumire ngakhale Mwana wake+ koma anamupereka m’malo mwa ife tonse,+ angalephere bwanji kutipatsanso mokoma mtima zinthu zina zonse pamodzi ndi Mwana wakeyo?+ 33  Ndani adzasumira mlandu anthu a Mulungu ochita kusankhidwa?+ Mulungu ndiye amawayesa olungama.+ 34  Ndani adzawatsutsa? Khristu Yesu ndiye amene anafa, zoonadi, amenetu anaukitsidwa kwa akufa. Iye ali kudzanja lamanja+ la Mulungu, ndipo amatilankhulira mochonderera kwa Mulunguyo.+ 35  Ndani adzatilekanitsa ndi chikondi cha Khristu?+ Chisautso kodi, kapena zowawa, chizunzo, njala, usiwa, zoopsa, kapena lupanga?+ 36  Monga mmene Malemba amanenera kuti: “Chifukwa cha inu, tikuphedwa nthawi zonse. Takhala ngati nkhosa zokaphedwa.”+ 37  Koma tikugonjetsa zinthu zonsezi+ kudzera mwa iye amene anatikonda. 38  Pakuti ndatsimikiza mtima kuti imfa, moyo,+ angelo,+ maboma,+ zinthu zimene zilipo, zinthu zimene zikubwera m’tsogolo, mphamvu,+ 39  msinkhu, kuzama, kapena cholengedwa china chilichonse, sichidzatha kutilekanitsa ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.+

Mawu a M'munsi

Mawu achiaramu otanthauza “ababa,” kapena, “Bambo anga!”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.