Aroma 15:1-33
15 Ife olimba tiyenera kunyamula zofooka za osalimba,+ osati kumadzikondweretsa tokha ayi.+
2 Aliyense wa ife azikondweretsa mnzake pa zinthu zabwino zomulimbikitsa.+
3 Pakuti ngakhale Khristu sanadzikondweretse yekha,+ koma anachita mmene Malemba amanenera kuti: “Mnyozo wa anthu amene anali kukutonzani wagwa pa ine.”+
4 Zinthu zonse zimene zinalembedwa+ kalekale zinalembedwa kuti zitilangize.+ Malembawa amatipatsa chiyembekezo+ chifukwa amatithandiza kupirira+ ndiponso amatilimbikitsa.+
5 Tsopano, Mulungu amene amatipatsa mphamvu kuti tithe kupirira ndiponso amene amatitonthoza, achititse nonsenu kukhala ndi maganizo+ amene Khristu Yesu anali nawo,
6 kuti nonse pamodzi,+ ndi pakamwa pamodzi, mulemekeze Mulungu, Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu.
7 Chotero landiranani,+ monga mmene Khristu anatilandirira,+ kuti ulemerero upite kwa Mulungu.
8 Kunena zoona,+ Khristu anakhaladi mtumiki+ kwa anthu odulidwa+ kuti atsimikizire kuti Mulungu ndi wokhulupirika. Komanso iye anasonyeza kuti malonjezo+ amene Mulunguyo anapatsa makolo awo ndi otsimikizirika,
9 kuti mitundu ina+ ipereke ulemerero kwa Mulungu chifukwa cha chifundo+ chake, monga mmene Malemba amanenera kuti: “N’chifukwa chake ndidzakuvomerezani poyera pakati pa mitundu. Ndipo ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.”+
10 Komanso Malemba amati: “Kondwerani, mitundu inu, pamodzi ndi anthu ake.”+
11 Ndiponso amati: “Tamandani Yehova, inu mitundu yonse ya anthu, ndipo anthu onse amutamande.”+
12 Komanso Yesaya anati: “Padzakhala muzu wa Jese,+ ndipo padzatuluka wina wodzalamulira mitundu.+ Mitundu idzayembekezera iye.”+
13 Mulungu amene amapereka chiyembekezo akudzazeni ndi chimwemwe chonse ndi mtendere wonse chifukwa cha kukhulupirira kwanu, kuti mukhale ndi chiyembekezo chachikulu mwa mphamvu ya mzimu woyera.+
14 Tsopano abale anga, ine ndine wotsimikiza mtima za inu kuti ndinu okonzeka kuchita zabwino, monga mmene mwakhalira odziwa zinthu zonse.+ Ndine wotsimikizanso mtima kuti mukhoza kulangizana.+
15 Komabe, ndakulemberani mfundo zina mosapita m’mbali kuti ndikukumbutseninso.+ Ndachita zimenezi chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu wandipatsa.+
16 Ndinapatsidwa kukoma mtima kumeneku kuti ndigwire ntchito yolengeza uthenga wabwino wa Mulungu monga wantchito wa Khristu Yesu, wotumikira anthu a mitundu ina.+ Cholinga changa pogwira ntchito yopatulikayi+ n’chakuti mitundu ina ya anthu iperekedwe+ kwa Mulungu ngati mphatso yovomerezeka+ imene yayeretsedwa ndi mzimu woyera.+
17 Chotero ndili ndi chifukwa chokhalira wokondwa mwa Khristu Yesu+ pa zinthu zokhudza Mulungu.+
18 Pakuti sindidzayesa m’pang’ono pomwe kulankhula kanthu ngakhale kamodzi kokha ngati sikanachokere m’zinthu zimene Khristu anachita mwa ine+ kuti mitundu ina ikhale yomvera.+ Anachita zimenezi pogwiritsa ntchito mawu anga+ ndi zochita zanga,
19 ndiponso pogwiritsa ntchito mphamvu yochita zizindikiro ndi zinthu zodabwitsa zolosera zam’tsogolo,+ mwa mphamvu ya mzimu woyera. Chotero ndalalikira mokwanira uthenga wabwino wonena za Khristu+ kuyambira ku Yerusalemu, kuzungulira+ mpaka ku Iluriko.
20 Ndithudi, pochita zimenezi ndinatsimikiza mtima kuti ndisalengeze uthenga wabwino kumene Khristu anatchulidwa kale, ndi cholinga chakuti ndisamange pamaziko+ a munthu wina,
21 koma ndichite monga mmene Malemba amanenera kuti: “Amene chilengezo chonena za iye sichinawapeze adzaona, ndipo amene sanamve adzazindikira.”+
22 Choncho, pa chifukwa chimenechinso ndinalephera kufika kwa inu.+
23 Koma tsopano popeza kulibenso gawo limene sindinafikeko m’madera amenewa, ndiponso popeza kuti kwa zaka zambiri ndakhala ndikulakalaka kufika kwanuko,+
24 ndili ndi chikhulupiriro kuti mulimonse mmene zingakhalire, pa ulendo wanga wa ku Sipaniya+ nthawi ina iliyonse, ndidzaonana nanu. Ndikadzacheza nanu mpaka kukhutira, mudzandiperekeza+ pa ulendo wangawo.
25 Koma tsopano ndatsala pang’ono kupita ku Yerusalemu kukatumikira oyera.+
26 Abale amene ali ku Makedoniya ndi ku Akaya+ akhala ali ofunitsitsa kupereka+ mphatso kwa oyera osauka a ku Yerusalemu.
27 Ndi zoona kuti achita zimenezo mwa kufuna kwawo, komabe iwo anali ndi ngongole kwa oyerawo. Pakuti ngati anthu a mitundu ina alandirako zinthu zauzimu+ kuchokera kwa oyerawo, ndiye kuti anthu a mitundu inawo ayeneranso kutumikira oyera amenewa mwa kuwapatsa zinthu zofunika pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku.+
28 Choncho ndikakamaliza zimenezi ndipo ndikakafika bwino ndi zopereka zimenezi+ kwa iwo, ndidzadzera kwanuko popita ku Sipaniya.+
29 Komanso, ndikudziwa kuti ndikadzafika kwanuko ndidzafika ndi dalitso lonse lochokera kwa Khristu.+
30 Chotero ndikukudandaulirani abale, kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu ndi mwa chikondi cha mzimu,+ kuti mulimbikire limodzi ndi ine popemphera kwa Mulungu za ineyo.+
31 Tilimbikire kupemphera kuti ndikalanditsidwe+ kwa anthu osakhulupirira a ku Yudeya, ndi kutinso utumiki wanga wa ku Yerusalemu+ ukakhale wolandirika kwa oyerawo,+
32 kuti ndikadzafika kwa inu ndi chisangalalo mwa kufuna kwa Mulungu, tidzalimbikitsidwe pamodzi.+
33 Mulungu amene amapatsa mtendere akhale ndi nonsenu.+ Ame.