Aroma 10:1-21
10 Ndithu abale, chimene ndikufunitsitsa mumtima mwanga ndiponso pembedzero langa kwa Mulungu ndi lakuti Aisiraeli apulumutsidwe.+
2 Pakuti ndikuwachitira umboni kuti ndi odzipereka+ potumikira Mulungu, koma samudziwa molondola.+
3 Ndipo posadziwa chilungamo cha Mulungu,+ iwo sanagonjere chilungamocho+ koma anayesetsa kukhazikitsa chawochawo.+
4 Pakuti Khristu ndiye kutha kwa Chilamulo,+ kuti aliyense wokhulupirira akhale wolungama.+
5 Pajatu Mose analemba kuti munthu wochita chilungamo cha m’Chilamulo adzakhala ndi moyo chifukwa cha chilungamo chimenecho.+
6 Koma za chilungamo chimene chimabwera chifukwa cha chikhulupiriro, Malemba amati: “Mumtima mwako usanene kuti,+ ‘Kodi ndani adzakwera kumwamba?’+ kuti akatsitse Khristu.+
7 Kapena, ‘Kodi ndani adzatsikira kuphompho?’+ kuti akaukitse Khristu kwa akufa.”+
8 Koma kodi Lemba limati chiyani? Limati: “Mawu a chilamulowo ali pafupi ndi iwe, ali m’kamwa mwako ndi mumtima mwako,”+ amenewa ndi “mawu”+ a chikhulupiriro, amene tikulalikira.+
9 Pakuti ngati ukulengeza kwa anthu ‘mawu amene ali m’kamwa mwakowo,’+ akuti Yesu ndiye Ambuye,+ ndipo mumtima mwako ukukhulupirira kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa,+ udzapulumuka.+
10 Munthu amakhala ndi chikhulupiriro mumtima mwake+ kuti akhale wolungama, koma ndi pakamwa pake amalengeza poyera+ chikhulupiriro chake kuti apulumuke.
11 Paja Lemba limati: “Palibe wokhulupirira iye,+ amene adzakhumudwe.”+
12 Palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi Mgiriki,+ popeza kwa onsewo Ambuye ndi mmodzi, amene amapereka mowolowa manja+ kwa onse oitana pa dzina lake.
13 Pakuti “aliyense amene adzaitana pa dzina la Yehova* adzapulumuka.”+
14 Komabe, kodi angaitane bwanji munthu amene samukhulupirira?+ Angakhulupirire bwanji munthu amene sanamvepo za iye? Angamve bwanji za iye popanda wina kulalikira?+
15 Ndipo angalalikire bwanji ngati sanatumidwe?+ Zili monga muja Malemba amanenera kuti: “Mapazi a anthu olengeza uthenga wabwino wa zinthu zabwino, ndi okongola kwabasi!”+
16 Ngakhale zili choncho, si onse amene analabadira uthenga wabwino.+ Pakuti Yesaya anati: “Yehova, kodi ndani wakhulupirira zimene anamva kwa ife?”+
17 Chotero munthu amakhala ndi chikhulupiriro chifukwa cha zimene wamva.+ Ndipo zimene wamvazo zimachokera m’mawu onena za Khristu.+
18 Koma ndifunsebe kuti, Kodi kumva sanamve? Pajatu “liwu lawo linamveka padziko lonse lapansi,+ ndipo mawu awo anamveka kumalekezero a dziko lapansi kumene kuli anthu.”+
19 Komabe ndifunse kuti, Kodi si zoona kuti Aisiraeli anadziwa?+ Choyamba Mose anati: “Ndidzakuchititsani nsanje kudzera mwa anthu omwe si mtundu. Ndidzaputa mkwiyo wanu woopsa kudzera mwa mtundu wopusa.”+
20 Koma Yesaya analankhula molimba mtima kwambiri kuti: “Anthu amene anandipeza ndi amene sanali kundifunafuna.+ Ndinaonekera kwa anthu amene sanafunse za ine kuti andipeze.”+
21 Koma za Aisiraeli iye anati: “Ndatambasula manja anga tsiku lonse kwa anthu osamva+ komanso otsutsa.”+
Mawu a M'munsi
^ Onani Zakumapeto 2.