2 Timoteyo 4:1-22
4 Pamaso pa Mulungu ndi pa Khristu Yesu, amene anaikidwiratu kudzaweruza+ amoyo ndi akufa,+ akadzaonekera+ bwinobwino ndiponso akadzabwera mu ufumu wake,+ ndikukulamula mwamphamvu kuti,
2 lalikira mawu.+ Lalikira modzipereka, m’nthawi yabwino+ ndi m’nthawi yovuta.+ Dzudzula,+ tsutsa, dandaulira. Chita zimenezi ndi luso la kuphunzitsa ndiponso moleza mtima kwambiri.+
3 Pakuti idzafika nthawi imene anthu sadzafunanso chiphunzitso cholondola,+ koma mogwirizana ndi zilakolako zawo, adzadzipezera aphunzitsi kuti amve zowakomera m’khutu.+
4 Iwo adzasiya kumvetsera choonadi, n’kutembenukira ku nkhani zonama.+
5 Koma iwe ukhalebe woganiza bwino+ pa zinthu zonse, imva zowawa,+ gwira ntchito ya mlaliki,*+ ndipo ukwaniritse mbali zonse za utumiki wako.+
6 Pakuti ine ndayamba kale kukhuthulidwa ngati nsembe yachakumwa,+ ndipo nthawi yakuti ndimasuke+ yatsala pang’ono kukwana.
7 Ndamenya nkhondo yabwino.+ Ndathamanga panjirayo mpaka pa mapeto pake.+ Ndasunga chikhulupiriro.+
8 Kuyambira panopa mpaka m’tsogolo, andisungira chisoti chachifumu chachilungamo.+ Ambuye, woweruza wolungama,+ adzandipatsa mphotoyo+ m’tsikulo.+ Sadzapatsa ine ndekha ayi, komanso onse amene akhala akuyembekezera kuti iye adzaonekere.
9 Uchite chilichonse chotheka kuti ubwere kwa ine posachedwa.+
10 Pakuti Dema+ wandisiya chifukwa chokonda zinthu za m’nthawi* ino,+ ndipo wapita ku Tesalonika. Keresike wapita ku Galatiya,+ ndipo Tito wapita ku Dalimatiya.
11 Luka yekha ndiye amene ali ndi ine. Pobwera utengenso Maliko, pakuti iye ndi wofunika kwa ine chifukwa amandithandiza+ pa utumiki wanga.
12 Koma Tukiko+ ndamutuma ku Efeso.
13 Unditengerekonso chovala champhepo chimene ndinachisiya ku Torowa+ kwa Karipo ndi mipukutu, makamaka yazikopa ija.
14 Alekizanda,+ wosula zinthu zamkuwa uja, anandichitira zoipa zambiri. Yehova adzamubwezera malinga ndi ntchito zake,+
15 ndipo iwenso uchenjere naye, chifukwa anatsutsa mawu athu mwamphamvu.
16 Pamene ndinali kudziteteza koyamba pa mlandu wanga, palibe amene anakhala kumbali yanga. Onse anandisiya ndekha.+ Ngakhale zinali choncho, usakhale mlandu kwa iwo.+
17 Koma Ambuye anaima pafupi ndi ine+ ndi kundipatsa mphamvu,+ kuti kudzera mwa ine, ntchito yolalikira ichitidwe mokwanira, ndi kuti mitundu yonse ya anthu imve uthengawo.+ Ndiponso ndinapulumutsidwa m’kamwa mwa mkango.+
18 Ambuye adzandipulumutsa ku choipa chilichonse+ ndipo adzandisungira ufumu wake wakumwamba.+ Iye apatsidwe ulemerero mpaka muyaya. Ame.
19 Undiperekere moni kwa Purisika+ ndi Akula, ndi banja la Onesiforo.+
20 Erasito+ anatsalira ku Korinto,+ koma Terofimo+ ndinamusiya akudwala ku Mileto.+
21 Uchite chilichonse chotheka kuti ufike kuno nyengo yachisanu isanayambe.
Ebulo, Pude, Lino ndiponso Kalaudiya ndi abale onse, akupereka moni.
22 Ambuye akhale nawe chifukwa cha mzimu umene umaonetsa.+ Kukoma mtima kwake kwakukulu kukhale nanu.