2 Akorinto 1:1-24
1 Ine Paulo, mtumwi+ wa Khristu Yesu mwa kufuna kwa Mulungu, ndikulembera mpingo wa Mulungu wa ku Korinto, pamodzi ndi oyera onse+ amene ali mu Akaya+ monse, ndili limodzi ndi Timoteyo+ m’bale wathu, kuti:
2 Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere, zochokera kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu, zikhale nanu.+
3 Atamandike Mulungu ndi Atate+ wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Tate wachifundo chachikulu+ ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse,+
4 amenenso amatitonthoza m’masautso athu onse,+ kuti tithe kutonthoza+ amene ali m’masautso amtundu uliwonse, chifukwa nafenso tatonthozedwa ndi Mulungu.+
5 Popeza tikukumana ndi masautso ambiri chifukwa cha Khristu,+ tikutonthozedwanso kwambiri kudzera mwa Khristu.+
6 Tsopano ngati tili m’masautso, cholinga chake ndi choti inuyo mutonthozedwe ndi kupulumutsidwa.+ Ngati tikutonthozedwa, cholinga chake ndi choti inuyo mutonthozedwe kuti mupirire masautso amene ifenso tikukumana nawo.+
7 Chotero chiyembekezo chathu mwa inu sichikugwedera, podziwa kuti mukukumana ndi masautso ofanana ndi amene ifeyo tikukumana nawo, inunso mudzatonthozedwa ngati ifeyo.+
8 Abale, sitikufuna kuti mukhale osadziwa za masautso amene tinakumana nawo m’chigawo cha Asia,+ pamene tinali pa vuto lalikulu lotiposa mphamvu, moti tinalibenso chiyembekezo choti tikhala ndi moyo.+
9 Ngakhalenso m’mitima mwathu, tinali kumva ngati talandira chiweruzo cha imfa. Zinatero kuti tisakhale ndi chikhulupiriro mwa ife tokha,+ koma mwa Mulungu amene amaukitsa akufa.+
10 Iye anatipulumutsadi ku chinthu choopsa, ndicho imfa, ndipo adzatipulumutsabe.+ Tikukhulupirira kuti iye apitiriza kutipulumutsa.+
11 Inunso mungathandizepo mwa kutiperekera mapembedzero anu,+ kuti pakhale anthu ambiri otiperekera mapemphero oyamikira+ zinthu zimene tapatsidwa mokoma mtima, chifukwa cha mapemphero a anthu ambiri.+
12 Ifeyo tili ndi chifukwa chodzitamandira chakuti m’dzikoli, makamaka pakati pa inuyo, tachita zinthu zoyera ndiponso moona mtima mogwirizana ndi zimene Mulungu amaphunzitsa. Tachita zimenezi osati modalira nzeru+ za m’dzikoli koma modalira kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, ndipo chikumbumtima chathu chikuchitiranso umboni zimenezi.+
13 Pakuti zimene takulemberanizi si zina ayi, koma zimene mukuzidziwa bwino ndiponso zimene mukuzivomereza. Ndili ndi chikhulupiriro choti mupitiriza kuvomereza zinthu zimenezi mpaka pa mapeto.+
14 Inuyo mwavomereza kale, ngakhale kuti m’pang’ono pokha, kuti ifeyo ndife chifukwa choti mudzitamandire,+ ngati mmene inuyonso mudzakhalire chifukwa choti ifeyo tidzadzitamandire m’tsiku la Ambuye wathu Yesu.+
15 Choncho, popeza ndine wotsimikiza za zimenezi, ndinali ndi cholinga chofika kwa inu poyamba,+ kuti mudzakhale ndi mwayi wachiwiri+ wosangalala.
16 Kuti ndikadzacheza nanu pang’ono ndidzapite ku Makedoniya,+ ndipo ndikadzachoka ku Makedoniya ndidzabwerenso kwa inu+ kuti mudzandiperekeze+ popita ku Yudeya.
17 Tsopano pamene ndinali ndi cholinga chimenechi, kodi ndinali kulingalira mwachibwana?+ Kapena kodi zimene ndimaganiza kuti ndichite, ndimaziganiza ndi zolinga zadyera,+ kuti ndikati “Inde, inde” nthawi yomweyo ndisinthe ndinene kuti “Ayi, ayi”?+
18 Koma Mulungu ndi wodalirika kuti mawu athu kwa inu asakhale Inde kenako Ayi.
19 Pakuti Mwana wa Mulungu,+ Khristu Yesu, amene analalikidwa pakati panu kudzera mwa ineyo, Silivano, ndi Timoteyo,+ sanakhale Inde kenako Ayi, koma mwa iye, Inde wakhalabe Inde.+
20 Ndiponso malonjezo a Mulungu, kaya akhale ochuluka chotani,+ akhala Inde kudzera mwa iye.+ Choteronso kudzera mwa iye, “Ame”+ amanenedwa kwa Mulungu kuti Mulungu alandire ulemerero kudzera mwa ife.
21 Koma amene amatitsimikizira kuti inuyo ndi ife tili a Khristu, amenenso anatidzoza,+ ndiye Mulungu.
22 Iye watiikanso chidindo+ chake chotitsimikizira ndipo watipatsa m’mitima mwathu chikole+ cha madalitso am’tsogolo, ndicho mzimu.+
23 Mulungu akhale mboni+ pa moyo wanga kuti chifukwa chimene sindinabwererebe ku Korintoko n’chakuti sindinafune kuti ndidzawonjezere chisoni chanu.+
24 Sikuti ndife olamulira+ chikhulupiriro chanu, koma ndife antchito anzanu+ kuti mukhale ndi chimwemwe, pakuti ndinu okhazikika+ chifukwa cha chikhulupiriro chanu.+