1 Mbiri 28:1-21

28  Davide anasonkhanitsa akalonga onse+ a Isiraeli ku Yerusalemu. Akalongawo+ anali a mafuko ndi a magulu otumikira mfumu, atsogoleri a magulu a anthu 1,000,+ atsogoleri a magulu a anthu 100,+ ndiponso atsogoleri oyang’anira katundu yense+ ndi ziweto+ za mfumu ndi za ana ake.+ Panalinso nduna za panyumba ya mfumu+ ndi amuna amphamvu,+ ngakhale mwamuna aliyense wamphamvu ndi wolimba mtima.  Kenako Davide mfumu anaimirira ndipo anati: “Ndimvereni inu abale anga ndi anthu anga. Ineyo ndinafunitsitsa mumtima mwanga+ kumanga nyumba yoti likasa la pangano la Yehova lizikhalamo, ndiponso yoti ikhale monga chopondapo mapazi+ cha Mulungu wathu, ndipo ndinakonzekera kuimanga.+  Koma Mulungu woonayo anandiuza kuti; ‘Iwe sumanga nyumba ya dzina langa,+ chifukwa wamenya nkhondo zambiri, ndiponso wakhetsa magazi ambiri.’+  Komabe, m’nyumba yonse ya bambo anga+ Yehova Mulungu wa Isiraeli anasankha ineyo kuti ndikhale mfumu+ ya Isiraeli mpaka kalekale, popeza anasankha Yuda kuti akhale mtsogoleri.+ M’nyumba ya Yuda anasankhamo nyumba ya bambo anga.+ Pa ana a bambo anga+ anavomereza ineyo+ kuti ndikhale mfumu ya Isiraeli yense.  Ndipo pa ana anga onse (pakuti Yehova wandipatsa ana ambiri)+ anasankha mwana wanga Solomo+ kuti akhale pampando wachifumu+ wa ufumu wa Yehova, kuti alamulire Isiraeli.  “Kuwonjezera pamenepo, anandiuza kuti: ‘Mwana wako Solomo ndiye adzamanga nyumba yanga+ ndiponso mabwalo anga, chifukwa ndam’sankha kuti akhale mwana wanga+ ndipo ine ndidzakhala atate wake.+  Akamatsatira malamulo anga+ ndi zigamulo zanga+ ndi mtima wonse ngati mmene akuchitira lero, ine ndidzakhazikitsa ufumu wake+ ndipo sudzagwedezeka mpaka kalekale.’  Tsopano mwaima pamaso pa Aisiraeli onse, amene ndi mpingo wa Yehova,+ ndiponso Mulungu wathu akumva zimenezi.+ Choncho samalani ndi kutsatira malamulo onse a Yehova Mulungu wanu, kuti dziko labwinoli+ likhale lanu ndi kuti mudzasiyire ana anu obwera pambuyo panu monga cholowa chawo mpaka kalekale.  “Ndipo iwe Solomo mwana wanga, dziwa+ Mulungu wa bambo wako, um’tumikire+ ndi mtima wathunthu+ ndi moyo wosangalala,+ chifukwa Yehova amasanthula mitima yonse+ ndipo amazindikira maganizo a munthu ndi zolinga zake zonse.+ Ukam’funafuna, adzalola kuti um’peze,+ koma ukam’siya+ adzakutaya kosatha.+ 10  Tsopano taona, Yehova wakusankha kuti umange nyumba yopatulika yoti azikhalamo. Limba mtima ndipo gwira ntchitoyi.”+ 11  Atatero, Davide anapatsa Solomo mwana wake mapulani akamangidwe+ ka khonde+ ndi nyumba zake, zipinda zake zosungiramo katundu,+ zipinda zake zakudenga,*+ zipinda zake zamkati zosalowa kuwala kwambiri, ndi nyumba yokhalamo chivundikiro chophimba machimo.+ 12  Panalinso mapulani a kamangidwe ka zonse zimene anauzidwa kudzera mwa mzimu+ zokhudza mabwalo+ a nyumba ya Yehova, zipinda zonse zodyeramo+ kuzungulira kachisi, chuma cha nyumba ya Mulungu woona, ndi chuma cha zinthu zimene anaziyeretsa kukhala zopatulika.+ 13  Anam’patsanso malangizo okhudza magulu+ a ansembe ndi a Alevi, ntchito yonse yokhudza utumiki wa panyumba ya Yehova, ndiponso malangizo okhudza ziwiya zonse za utumiki wa panyumba ya Yehova. 14  Anayezeratu golide, golide wa ziwiya zonse+ za ntchito zosiyanasiyana, ndi siliva wa ziwiya zonse zasiliva za ntchito zosiyanasiyana. 15  Anayezanso kulemera kwa zoikapo nyale+ zagolide ndi nyale zake zagolide, malinga ndi kulemera kwa zoikapo nyale zosiyanasiyana ndi nyale zake, komanso kulemera kwa zoikapo nyale zasiliva malinga ndi kulemera kwa choikapo nyale ndi nyale zake mogwirizana ndi ntchito zosiyanasiyana za zoikapo nyalezo. 16  Anayeza golide malinga ndi kulemera kwa matebulo osiyanasiyana oikapo mkate wosanjikiza,+ ndipo anayezanso siliva wa matebulo asiliva. 17  Anayezanso mafoloko, mbale zolowa,+ mitsuko, zinthu zonse zagolide woyenga bwino ndi mbale zing’onozing’ono zagolide zolowa,+ malinga ndi kulemera kwa mbale zing’onozing’ono zosiyanasiyana zolowa, komanso mbale zing’onozing’ono zasiliva zolowa, malinga ndi kulemera kwa mbale zing’onozing’ono zosiyanasiyana zolowa. 18  Anayezanso golide woyengedwa bwino wa guwa lansembe la zofukiza+ malinga ndi kulemera kwake, ndiponso golide wa chifaniziro cha galeta,+ kutanthauza akerubi+ agolide otambasula mapiko awo kuphimba likasa la pangano la Yehova. 19  “Zonsezi zalembedwa+ chifukwa chakuti dzanja la Yehova linali pa ine, ndipo anandithandiza kumvetsa mbali zake zonse za mapulani a kamangidwe kake.”+ 20  Kenako Davide anauza Solomo mwana wake kuti: “Limba mtima,+ ugwire ntchitoyi mwamphamvu. Usaope+ kapena kuchita mantha+ chifukwa Yehova Mulungu, Mulungu wanga, ali ndi iwe.+ Sadzakutaya+ kapena kukusiya, kufikira ntchito yonse yokhudza utumiki wa nyumba ya Yehova itatha. 21  Tsopano ndikukupatsa magulu a ansembe+ ndi a Alevi+ ogwira ntchito zonse za panyumba ya Mulungu woona. Pa ntchito yonseyi, uli ndi amisiri odzipereka+ odziwa ntchito zosiyanasiyana,+ ndi akalonga,+ ndiponso anthu onse. Onsewa ndi okonzeka kuchita monga mwa mawu ako.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “zakutsindwi.”