1 Atesalonika 4:1-18

4  Pomalizira abale, tinakulangizani za mmene muyenera kuyendera+ ndi mmene muyenera kukondweretsera Mulungu, ndipo mukuchitadi zimenezo. Tsopano tikufuna kukudandaulirani ndi kukupemphani m’dzina la Ambuye Yesu kuti mupitirize kuchita zimenezi mowonjezereka.+  Pakuti mukudziwa malamulo+ amene tinakupatsani mwa ulamuliro wa Ambuye Yesu.  Mulungu akufuna kuti mukhale oyera+ mwa kupewa dama.*+  Akufunanso kuti aliyense wa inu akhale woyera mwa kudziwa kulamulira thupi lake+ m’njira yoyera+ kuti mukhale olemekezeka pamaso pa Mulungu,  osati mwa chilakolako chosalamulirika cha kugonana,+ ngati chimene anthu a mitundu ina+ osadziwa Mulungu+ ali nacho.  Koma akufuna kuti pasapezeke wina wopweteka m’bale wake kapena womuphwanyira ufulu wake pa nkhani imeneyi,+ chifukwa Yehova adzalanga anthu onse ochita zimenezi,+ monga mmene tinakuuzirani kale ndi kukufotokozerani momveka bwino.+  Pakuti Mulungu sanatiitane mwa kulekerera zodetsa, koma kuti tikhale oyera.+  Choncho munthu wonyalanyaza+ chiphunzitso chimenechi sakunyalanyaza munthu, koma Mulungu+ amene amaika mzimu wake woyera+ mwa inu.  Koma za kukonda abale,+ n’zosafunika kuti tizichita kukulemberani pakuti inu nomwe, Mulungu amakuphunzitsani+ kukondana.+ 10  Ndipo inu mukuchitadi zimenezi kwa abale onse ku Makedoniya konse. Koma tikukudandaulirani abale kuti mupitirize kutero mowonjezereka. 11  Ndiponso muyesetse kukhala mwamtendere,+ kusalowerera mu nkhani za eni,+ ndi kugwira ntchito ndi manja anu+ monga mmene tinakulamulirani. 12  Mutero kuti muziyenda moyenerera+ pamaso pa anthu akunja*+ ndiponso kuti mukhale osasowa kanthu.+ 13  Komanso abale, sitikufuna kuti mukhale osadziwa za amene akugona+ mu imfa, kuti musachite chisoni mofanana ndi mmene onse opanda chiyembekezo+ amachitira. 14  Pakuti ngati timakhulupirira kuti Yesu anafa ndi kuukanso,+ ndiye kuti amenenso agona mu imfa kudzera mwa Yesu, Mulungu adzawasonkhanitsa kuti akhale naye limodzi.+ 15  Pakuti tikukuuzani izi mogwirizana ndi mawu a Yehova+ kuti, ife amoyofe amene tidzakhalapo pa nthawi ya kukhalapo* kwa Ambuye,+ sitidzakhala patsogolo pa amene agona mu imfa. 16  Chifukwa Ambuye mwini adzatsika kumwamba,+ ndi mfuu yolamula ya mawu a mkulu wa angelo,+ ndi lipenga+ la Mulungu. Ndipo amene anafa mwa Khristu adzauka choyamba.+ 17  Pambuyo pake ife amoyo otsalafe, limodzi ndi iwowo,+ tidzatengedwa+ m’mitambo+ kukakumana+ ndi Ambuye m’mlengalenga, ndipo tizikakhala ndi Ambuye nthawi zonse.+ 18  Choncho, muzilimbikitsana ndi mawu amenewa.

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 7.
Amenewa ndi anthu amene sali mumpingo wachikhristu.
Onani Zakumapeto 8.