Alalikila khomo na khomo ku Italy

UMOYO NA UTUMIKI WATHU–KABUKU KA MISONKHANO July 2017

Maulaliki a Citsanzo

Maulaliki a citsanzo oseŵenzetsa pogaŵila Nsanja ya Mlonda ndi pophunzitsa coonadi pa nkhani ya mavuto. Seŵenzetsani maulaliki a citsanzo pokonza ulaliki wanu.

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

Kodi Muli na Mtima wa Mnofu?

Kodi mtima umakhudzidwa bwanji popanga zosankha pa nkhani ya zosangalatsa, mavalidwe, na kudzikonza? Kodi kukhala na mtima wa mnofu kumatanthauza ciani?

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

Kodi Mumasunga Malonjezo Anu?

Tiphunzilapo ciani pa zimene zinatulukapo pamene Mfumu Zedekiya anaphwanya malonjezo ake?

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

Kodi Yehova Akatikhululukila Macimo, Amawakumbukilanso?

Ni zitsanzo za m’Baibo ziti zoonetsa umboni wakuti Yehova amakhululukila? Kodi mmene anacitila zinthu na Davide, Manase, na Petulo kutithandiza bwanji kukhulupilila kuti amatikhululukiladi?

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kodi Mumadziimbabe Mlandu?

Kungakhale kovuta kuleka kudziimba mlandu pa zolakwa zimene Yehova anatikhululukila kale. N’ciani cingatithandize?

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

Ufumuwo ni wa Uyo Ali Woyenelela Mwalamulo

Kodi ulosi wa Ezekieli wokhudza mfumu yoyenelela mwa lamulo unakwanilitsika bwanji pa Yesu? Kodi tiphunzilapo ciani za Yehova?

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Tizionetsa Ulemu Tikafika pa Khomo la Munthu

Tikaimilila pa khomo la munthu, ena amationela pa windo kapena kumvetsela ali kumbuyo kwa citseko. Tingaonetse bwanji ulemu tikafika pakhomo la munthu?

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU

Ulosi wa Kuwonongedwa kwa Mzinda wa Turo Umalimbitsa Cidalilo m’Mau a Yehova

Mbali zonse za Ulosi wa Ezekieli wokhudza kuwonongedwa kwa Turo zinakwanilitsika.