Nyimbo 22
“Yehova Ndi M’busa Wanga”
(Salmo 23)
1. Yehova ndi M’busa wanga;
Kodi ndingaopenji?
Amasamala nkhosa zake,
Sadzaziiwaladi.
Andipititsa kumadzi
Kukanditsitsimula.
Anditsogolera poyenda
M’njira zachilungamo.
Anditsogolera poyenda
M’njira zachilungamo.
2. Poyenda mumdima ndekha,
Sindidzaopa kanthu.
M’busa wanga alitu nane
Kumandilimbikitsa.
Adzozatu mutu wanga,
Wadzaza chikho changa.
Chifundo chake chinditsate,
Ndikhale m’nyumba yake.
Chifundo chake chinditsate,
Ndikhale m’nyumba yake.
3. N’ngwachikonditu M’busayo!
Ndim’tamanda mokondwa.
Ndidzalalikira kwa ena
Za chikondi chakecho.
Ndidzamvera Mawu ake
Poyenda m’njira zake.
Mwayi wanga wom’tumikira
Ndiugwiritsa ntchito.
Mwayi wanga wom’tumikira
Ndiugwiritsa ntchito.
(Onaninso Sal. 28:9; 80:1.)