Tingathe Kupewa Ciwelewele
“Yeletsani manja anu, . . . ndipo yeletsani mitima yanu.”—YAK. 4:8.
1. Kodi anthu ambili amaliona bwanji khalidwe laciwelewele?
ANTHU ambili masiku ano amakonda kucita zaciwelewele. Mwacitsanzo, anthu ambili amaona kuti si kulakwa kugonana ndi mwamuna kapena mkazi mnzao kapena kugonana ndi munthu wina amene si mwamuna kapena mkazi wao. Mafilimu, mabuku, nyimbo, ndi zinthu zina zotsatsa malonda zimalimbikitsa khalidwe laciwelewele. (Sal. 12:8) Khalidweli lafala kwambili cakuti mungadzifunse kuti, ‘Kodi n’zothekadi kukhala wodziletsa?’ Koma tifuna kukutsimikizilani kuti n’zotheka Akristu oona kupewa ciwelewele mwa kuthandizidwa ndi Yehova.—Ŵelengani 1 Atesalonika 4:3-5.
2, 3. (a) N’cifukwa ciani kulimbana ndi zilakolako zoipa n’kofunika kwambili? (b) Tikambilana ciani m’nkhani ino?
2 Kuti tikondweletse Yehova, tiyenela kupewa ciliconse cimene amadana naco. Koma cifukwa cakuti ndife opanda ungwilo, tingakopeke ndi ciwelewele, monga mmene nsomba zimakopekela ndi nyambo. Tikayamba kuganizila zaciwelewele, tiyenela kucotsa maganizo oipawo mwamsanga. Popanda kucita zimenezo, cilakolako ca ciwelewele cingakhale Yakobo 1:14, 15.
camphamvu kwambili moti mpata ukapezeka, tingacite chimo. Izi n’zimene Baibulo limanena kuti: “Cilakolako cikatenga pakati, cimabala chimo.”—Ŵelengani3 Tiyenela kukumbukila kuti cilakolako coipa cingapangitse kuti ticite chimo. Koma ngati timayesetsa kulimbana ndi zilakolako zoipa, tidzapewa ciwelewele ndi mavuto amene amatsatilapo cifukwa ca khalidweli. (Agal. 5:16) Tsopano tikambilana zinthu zitatu zimene zingatithandize kulimbana ndi zilakolako zoipa. Zinthu zimenezi ndi ubwenzi wathu ndi Yehova, malangizo a m’Baibulo, ndi thandizo la Akristu anzathu.
“YANDIKILANI MULUNGU”
4. N’cifukwa ciani tifunika kuyandikila Yehova?
4 Baibulo limalangiza anthu amene amafuna ‘kuyandikila Mulungu’ kuti: “Yeletsani manja anu, . . . ndipo yeletsani mitima yanu.” (Yak. 4:8) Ngati timakonda kwambili Yehova, timayesetsa kumukondweletsa mwa zocita ndi zoganiza zathu. Timayesetsa kukhala ‘oyela mumtima mwathu’ mwa kuganizila zinthu zoyela, khalidwe labwino, ndi zinthu zotamandika. (Sal. 24:3, 4; 51:6; Afil. 4:8) Yehova amadziŵa kuti ndife opanda ungwilo ndipo nthawi zambili timakonda kulakalaka zoipa. Komabe, iye amakhumudwa ngati timalekelela maganizo oipa kuzika mizu m’mitima mwathu m’malo mowacotsa. (Gen. 6:5, 6) Kuganizila mfundo imeneyi kuyenela kutilimbikitsa kupewa maganizo oipa.
5, 6. Kodi pemphelo lingatithandize bwanji kulimbana ndi zilakolako zoipa?
5 Tiyenela kupemphela kwa Yehova kuti atithandize kucotsa maganizo oipa. Kucita zimenezi kumaonetsa kuti timamudalila kwambili. Tikamayandikila Yehova m’pemphelo, nayenso amatiyandikila. Iye amatipatsa mzimu woyela moolowa manja, umene umatithandiza kukaniza maganizo oipa kuti tikhalebe oyela. Conco, tiyenela kuuza Mulungu m’pemphelo kuti timafunitsitsa kusinkhasinkha zinthu zimene zimamukondweletsa. (Sal. 19:14) Kodi timamupempha modzicepetsa kuti atifufuze ndi kuona ngati tili ndi zilakolako zoipa zimene ‘zingaticititse kuyenda m’njila yoipa’ ndi kucita chimo? (Sal. 139:23, 24) Kodi timamupempha nthawi zonse kuti atithandize kukhalabe okhulupilika pamene takumana ndi ciyeso?—Mat. 6:13.
6 Tikalibe kuphunzila za Yehova, mwina tinali kucita zinthu zimene iye amadana nazo, ndipo mwina tikali kulimbana ndi zilakolako zoipa. Yehova angatithandize kusintha ndi kuyamba kumutumikila m’njila imene amavomeleza. Mwacitsanzo, Mfumu Davide atacita cigololo ndi Batiseba, anapempha Yehova kuti: “Lengani mtima wolungama mkati mwanga, ndipo ikani maganizo atsopano ndi okhazikika mwa ine.” (Sal. 51:10, 12) Conco, ngati tikali kulimbana ndi zilakolako zoipa, Yehova angatithandize kukhala ndi mtima wofunitsitsa kumvela malamulo ake ndi kucita zinthu zoyenela. Iye angatithandizenso kulamulila maganizo athu opanda ungwilo.—Sal. 119:133.
“MUZICITA ZIMENE MAU AMANENA”
7. Kodi Mau a Mulungu angatithandize bwanji kupewa maganizo oipa?
7 Nthawi zina Yehova amayankha mapemphelo athu kudzela m’Mau ake, Baibulo. Nzelu zopezeka m’Mau a Mulungu ‘coyamba, ndi zoyela.’ (Yak. 3:17) Kuŵelenga Baibulo tsiku lililonse ndi kusinkhasinkha kungatithandize kupewa maganizo oipa. (Sal. 19:7, 11; 119:9, 11) Komanso m’Baibulo muli malangizo ndi zitsanzo zambili zimene zingatithandize kupewa zilakolako zoipa.
8, 9. (a) N’ciani cinacititsa mnyamata wina kuti afike pocita ciwelewele? (b) Ndi zinthu ziti zimene tiyenela kupewa malinga ndi cenjezo la pa Miyambo 7?
8 Pa Miyambo 5:8 pamati: “Njila yako ikhale kutali ndi [mkazi waciwelewele]. Usayandikile pakhomo la nyumba yake.” Pa Miyambo caputala 7 pali citsanzo cosonyeza kuopsa konyalanyaza malangizo amenewa. Palembali pamafotokoza za mnyamata wina amene anapita kukayenda madzulo mumseu pafupi ndi nyumba ya mkazi waciwelewele. Kenako kunayamba kuda. Mnyamatayo atafika pamphambano ya msewuwo, mkaziyo anamuyandikila, ndipo anali atavala zovala za uhule. Iye anagwila mnyamatayo n’kumupsompsona. Mau okopa a mkaziyo anadzutsa cilakolako coipa mwa mnyamatayo ndipo analephela kudziletsa. Iwo anacita ciwelewele. N’zodziŵikilatu kuti mnyamatayo sanapite kumeneko kuti akacite ciwelewele. Koma anali wosadziŵa zinthu ndi wopanda nzelu. Ngakhale zinali conco, iye anakumana ndi mavuto aakulu cifukwa ca zocita zake. Iye akanadziŵa zoopsa zimene adzakumana nazo, sakanayenda pafupi ndi nyumba ya mkaziyo.—Miy. 7:6-27.
9 Kodi nafenso nthawi zina timalephela
kuganiza bwino mwa kucita zinthu zimene zingadzutse cilakolako coipa? Mwacitsanzo, madzulo, pa machanelo ambili a TV pamakhala mapulogalamu oipa. Conco, kungakhale kupanda nzelu kumasinthasintha machanelo kuti tione mapulogalamu amene alipo. Komanso si bwino kupita pa Mawebusaiti kapena pa malo ocezela pa Intaneti osadziŵika bwino amene angationetse zinthu zaciwelewele ndi zamalisece. Zimene tingaone pa malo amenewo zingatipangitse kukhala ndi zilakolako zoipa, ndipo pamapeto pake tingacimwile Yehova.10. N’cifukwa ciani kukopana n’koopsa? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhaniyi.)
10 Baibulo limatithandizanso kupewa ciwelewele mwa kutiuza mmene tifunika kucitila zinthu ndi anthu amene si amuna kapena akazi anzathu. (Ŵelengani 1 Timoteyo 5:2.) Mau a Mulungu amaletselatu khalidwe la kukopana. Anthu ena amaganiza kuti kugwedeza thupi kapena ziwalo zina za thupi pofuna kukopa ena, kucita magesica okopa, ndi kuyang’ana kokopa kulibe vuto cifukwa anthu sagwilana. Koma kukopana, kapena kulola kuti wina atikope, kungayambitse maganizo oipa amene angatipangitse kucita ciwelewele. Zimenezi zakhala zikucitika, ndipo ifenso zingaticitikile.
11. Kodi Yosefe anatipatsa citsanzo cotani?
11 Yosefe anacita zinthu mwanzelu pamene mkazi wa mbuye wake, Potifara anayesa kumukopa. Yosefe sanagonje pamene mkaziyo anali kumunyengelela. Tsiku ndi tsiku mkaziyo anali kumupempha kuti akhale pambali pake. (Gen. 39:7, 8, 10) Malinga ndi katswili wina wa Baibulo, m’mau ena mkazi wa Potifara anali kunena kuti: “‘Tiye ticezeko tili aŵiliŵili.’ Colinga cake cinali cakuti [Yosefe] agone naye.” Komabe, Yosefe sanalole zofuna za mkaziyo kapena kulola kuti azimukopa. Kucita zimenezo kunathandiza kuti cilakolako coipa cisazike mizu mumtima mwake. Pamene mkaziyo anamukakamiza kuti agone naye, Yosefe anakana mosazengeleza. Iye “anangovula [malaya ake] n’kuwasiya m’manja mwa mkaziyo n’kuthawila panja.”—Gen. 39:12.
12. Timadziŵa bwanji kuti zimene timaona zingakhudze mtima wathu?
12 Yesu anaticenjeza kuti zimene timayang’ana zingakhudze mtima wathu ndi kudzutsa cilakolako ca kugonana. Iye anati: “Aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka, wacita naye kale cigololo mumtima mwake.” (Mat. 5:28) Kumbukilani zimene zinacitikila Mfumu Davide. Pamene anali padenga la nyumba yake, iye “anaona mkazi akusamba.” (2 Sam. 11:2) M’malo moyang’ana kumbali, iye anapitiliza kuyang’anitsitsa mkaziyo. Zimenezo zinapangitsa kuti ayambe kulakalaka mkazi wa mwiniyo, ndipo pamapeto pake anacita naye cigololo.
13. N’cifukwa ciani tifunika ‘kucita pangano ndi maso athu’? Nanga tingacite bwanji zimenezi?
13 Kuti tilimbane ndi zilakolako zoipa, tifunika ‘kucita pangano ndi maso athu’ ngati mmene anacitila Yobu. (Yobu 31:1, 7, 9) Tifunika kuyesetsa kulamulila maso athu kuti tisayang’anitsitse munthu wina mosayenela. Zimenezi zikuphatikizapo kupewa kuyang’ana zithunzi zodzutsa cilakolako, kaya ndi pa kompyuta, pa zikwangwani, pa magazini, kapena pena paliponse.
14. N’ciani cimene tiyenela kucita kuti tikhalebe oyela?
14 Pa zimene takambilanazi, ngati pali zinthu zina zimene mufunika kusintha kuti mupewe zilakolako zoipa, Yakobo 1:21-25.
muyenela kucita zimenezo mwamsanga. Muyenela kumvela ndi mtima wonse malangizo a m’Baibulo amene angakuthandizeni kupewa chimo ndi kukhalabe oyela.—Ŵelengani“AITANE AKULU”
15. Ngati tikuvutika kuthetsa cilakolako coipa, n’cifukwa ciani tifunika kupempha thandizo?
15 Ngati tikuvutika kuthetsa cilakolako coipa, tiyenela kupempha thandizo kwa Akristu anzathu. N’zoona kuti kuuza ena nkhani zotelo n’kovuta. Koma kucita zimenezo n’kofunika kwambili. Kupempha thandizo kwa Mkristu wokhwima mwauzimu kungatithandize kuti tisalekelele zilakolako zoipa kukula mumtima mwathu. (Miy. 18:1; Aheb. 3:12, 13) Mkristu wokhwima mwauzimu angatithandizenso kudziŵa zinthu zoipa zimene tiyenela kusintha pa umoyo wathu kuti tikhalebe m’cikondi ca Yehova.
16, 17. (a) Kodi akulu angathandize bwanji Akristu amene akuvutika kuthetsa zilakolako zoipa? Pelekani citsanzo. (b) N’cifukwa ciani anthu amene amapenyelela zamalisece afunika kupempha thandizo mwamsanga?
16 Akulu mumpingo ndi amene ali oyenelela kwambili kutipatsa thandizo. (Ŵelengani Yakobo 5:13-15.) Mwacitsanzo, mnyamata wina wa ku Brazil anavutika kwa zaka zambili kuti athetse cilakolako coipa. Iye anati: “Ndinali kudziŵa kuti maganizo anga anali onyansa pamaso pa Yehova, koma ndinali kucita mantha kwambili kuuza ena za vuto langa.” Mwamwai, mkulu wina wa mumpingo mwake anamufikila ndi kumulimbikitsa kupempha thandizo. Pokumbukila zimene zinacitika, mnyamatayo anati: “Ndinacita cidwi kwambili ndi kukoma mtima kwa akuluwo. Iwo anacita nane zinthu mokoma mtima kwambili kuposa mmene ndinali kuganizila, ndiponso anali kumvetsela mosamala pamene ndinali kuwauza mavuto anga. Anagwilitsila nchito Baibulo ponditsimikizila kuti Yehova amandikonda, ndipo anapemphela nane. Zimenezo zinandithandiza kuti ndimvetsele ndi kugwilitsila nchito malangizo a m’Baibulo amene anandipatsa.” Patapita zaka, iye anapita patsogolo mwa kuuzimu, ndipo anati: “Tsopano ndaona kuti kupempha thandizo kwa ena n’kofunika kwambili m’malo moyesa kuthetsa nekha vuto.”
17 Kupempha thandizo n’kofunika kwambili ngati tikulimbana ndi zilakolako zoipa cifukwa copenyelela zamalisece. Kulephela kupeza thandizo mwamsanga kungacititse zilakolako zoipa kukula ndi kufika pobala chimo. Izi zingakhumudwitse abale athu ndiponso kunyozetsa dzina la Yehova. Cifukwa cofunitsitsa kukondweletsa Yehova ndi kukhalabe mumpingo wacikristu, atumiki ambili a Mulungu amagwilitsila nchito malangizo acikondi amene apatsidwa.—Yak. 1:15; Sal. 141:5; Aheb. 12:5, 6.
YESETSANI KUPEWA CIWELEWELE
18. Kodi mukufunitsitsa kucita ciani?
18 Pamene makhalidwe akuipilaipila m’dziko la Satanali, Yehova amakondwela kwambili kuona atumiki ake odzipeleka akuyesetsa kupewa maganizo oipa ndi kutsatila mfundo zake za makhalidwe abwino. Motelo, tiyeni tonse tiyesetse kukhalabe pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ndi kumvela malangizo amene iye amapeleka kudzela m’Mau ake ndi mumpingo wacikristu. Kupewa ciwelewele kumatithandiza kukhala ndi mtendele wa m’maganizo ndi kukhala osangalala. (Sal. 119:5, 6) Mtsogolo, Satana akadzaonongedwa, tidzakhala ndi moyo wosatha m’dziko latsopano lopanda makhalidwe oipa.