Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga
Pamene Satana anauza Hava kuti sadzafa akadya cipatso ca mtengo wodziŵitsa cabwino na coipa, kodi anali kuyambitsa ciphunzitso cofala masiku ano cakuti munthu ali na mzimu wosafa?
Mwacionekele iyai. Mdyelekezi sanauze Hava kuti akadya cipatso ca mtengo umene Mulungu anawaletsa, thupi lake lidzafa koma mzimu wake udzapitiliza kukhala na moyo kwinakwake. Polankhula kudzela mwa njoka, Satana anauza Hava kuti akadya cipatso ca mtengowo, “sadzafa ayi.” Apa, Satana anatanthauza kuti Hava adzapitiliza kukhala na moyo wosangalala pano padziko lapansi, popanda kudalila Mulungu.—Gen. 2:17; 3:3-5.
Ngati ciphunzitso cabodza cakuti anthu ali na mzimu umene sumafa sicinayambile m’munda wa Edeni, kodi cinayamba liti? Sitidziŵa bwino-bwino. Zimene tidziŵa n’zakuti, anthu onse ocilikiza kulambila konama anawonongedwa pa Cigumula ca Nowa. Panalibe munthu wokhulupilila ciphunzitso conama amene anapulumuka. Nowa na banja lake ndiwo wokha anapulumuka Cigumula, ndipo anali olambila oona.
Motelo, ciphunzitso cakuti munthu ali na mzimu umene sumafa ciyenela kuti cinayamba pambuyo pa Cigumula. Pamene Mulungu anasokoneza cilankhulo pa Babele, anthu anamwazikana na kufalikila “padziko lonse lapansi.” Ndipo mosakaikila, kulikonse kumene iwo anapita, anapitiliza kukhulupilila kuti anthu ali na mzimu umene sumafa. (Gen. 11:8, 9) Olo kuti sitidziŵa bwino-bwino nthawi imene ciphunzitso conama cimeneci cinayamba, sitikaikila kuti “tate wake wa bodza,” Satana Mdyelekezi, ndiye anayambitsa ciphunzitsoci, ndipo anakondwela kuona kuti cikufalikila pa dziko lonse.—Yoh. 8:44.