Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Tengelani Khalidwe la Yehova la Cifundo

Tengelani Khalidwe la Yehova la Cifundo

“Yehova, Yehova, Mulungu wacifundo ndi wacisomo.” —EKS. 34:6.

NYIMBO: 142, 12

1. Kodi Yehova anadzidziŵikitsa bwanji kwa Mose? Nanga n’cifukwa ciani zimenezi n’zocititsa cidwi?

PANTHAWI ina, Mulungu anadzidziŵikitsa mwa kuchula dzina lake ndi makhalidwe ake kwa Mose. Makhalidwe oyamba amene anachula ni cifundo na cisomo. (Ŵelengani Ekisodo 34:5-7.) Yehova akanafuna akanayambila kuchula za mphamvu kapena nzelu zake. Koma panthawiyo, Mose anali kufuna kudziŵa ngati Mulungu anali wokonzeka kumuthandiza. N’cifukwa cake Yehova anayambila kuchula makhalidwe amene amaonetsa kuti iye ni wofunitsitsa kuthandiza atumiki ake. (Eks. 33:13) Ndithudi, n’zolimbikitsa kuona kuti Mulungu anayambila kuchula makhalidwe ocititsa cidwi amenewa akalibe kuchula makhalidwe ake ena. M’nkhani ino, tidzakambilana za khalidwe la cifundo, limene limatanthauza kukhudzika na mavuto a munthu wina ndi kufuna kumuthandiza.

2, 3. (a) N’ciani cionetsa kuti kusonyeza cifundo ni mbali ya cibadwa ca anthu? (b) N’cifukwa ciani kuphunzila zimene Baibo imakamba ponena za khalidwe la cifundo n’kofunika?

2 Ife anthu tinalengedwa m’cifanizilo ca Mulungu. Popeza Yehova ni Mulungu wacifundo, nafenso mwacibadwa timafunila anzathu zabwino. Ngakhale anthu amene sadziŵa Mulungu woona, nthawi zambili amacitila ena cifundo. (Gen. 1:27) M’Baibo muli zitsanzo zambili za anthu amene anaonetsa khalidwe la cifundo. Mwacitsanzo, kumbukilani nkhani ya mahule aŵili amene anali kulimbilana mwana pamaso pa Solomo. Pamene Solomo anawayesa mwa kulamula kuti mwanayo amudule pakati, mayi wake weni-weni anamvela cifundo. N’cifukwa cake analolela ngakhale kupeleka mwanayo kwa mzimayi winayo. (1 Maf. 3:23-27) Komanso kumbukilani za mwana wamkazi wa Farao, amene anapulumutsa Mose pamene anali wakhanda. Iye anadziŵa kuti mwana amene anapezayo anali wa Aheberi ndi kuti anafunika kuphedwa. Koma “anamumvela cisoni,” ndipo anaganiza zomulela monga mwana wake.—Eks. 2:5, 6.

3 N’cifukwa ciani kukambilana za khalidwe la cifundo n’kofunika? Cifukwa cakuti Baibo imatilangiza kuti tiyenela kutengela citsanzo ca Yehova. (Aef. 5:1) N’zoona kuti anthufe tinalengedwa kuti tizicitila ena cifundo. Koma cifukwa ca kupanda ungwilo kumene tinatengela kwa Adamu, timakonda kucita zinthu modzikonda. Nthawi zina, tingaone kuti n’zovuta kusankha kaya kuthandiza ena kapena kucita zinthu zodzipindulitsa. N’ciani cingatithandize kukhalabe acifundo ndi oganizila ena? Coyamba, tiyenela kupenda mmene Yehova waonetsela cifundo ndi mmene anthu enanso aonetsela khalidweli. Caciŵili, tiyenela kuganizila zimene tingacite kuti titengele citsanzo ca Mulungu ndiponso mapindu amene tingapeze ngati tacita zimenezi.

YEHOVA N’CITSANZO CABWINO KOPAMBANA PANKHANI YOONETSA CIFUNDO

4. (a) N’cifukwa ciani Yehova anatumiza angelo ku Sodomu? (b) Kodi nkhani ya Loti ndi ana ake itiphunzitsa ciani?

4 M’Baibo muli nkhani zambili zosonyeza mmene Yehova anaonetsela cifundo kwa anthu. Mwacitsanzo, ganizilani zimene Mulungu anacitila Loti. Munthu wolungama ameneyo anali ‘kuvutika mtima kwambili’ cifukwa ca khalidwe lotayilila la anthu a m’mizinda ya Sodomu ndi Gomora. M’pomveka kuti Mulungu anakonza zakuti awononge anthu aciwelewele amenewo. (2 Pet. 2:7, 8) Mulungu anatumiza angelo kuti akapulumutse Loti. Iwo analamula Loti pamodzi na banja lake kuti atuluke m’mizindayo. “Pamene iye anali kuzengeleza, [angelo], mwa cifundo ca Yehova pa iye, anagwila dzanja iyeyo, mkazi wake, ndi ana ake aakazi aŵiliwo, n’kuwatulutsa kukawasiya kunja kwa mzinda.” (Gen. 19:16) Citsanzo cimeneci cionetsa kuti Yehova amadziŵa bwino mavuto amene anthu ake okhulupilika amakumana nawo.—Yes. 63:7-9; Yak. 5:11; 2 Pet. 2:9.

5. Kodi Malemba monga 1 Yohane 3:17, angatithandize bwanji kukhala acifundo?

5 Inde, Yehova wakhala akuonetsa cifundo kwa anthu. Kuwonjezela pamenepo, waphunzitsa anthu ake kufunika koonetsa khalidwe limeneli. Ganizilani lamulo limene iye anapeleka kwa Aisiraeli lokamba za kulanda munthu covala monga cikole ca nkhongole. (Ŵelengani Ekisodo 22:26, 27.) Anthu ena ouma mtima anali kulanda munthu covala ngati ali naye nkhongole, n’kumusiya alibe ciliconse cakuti angafunde pogona. Koma Yehova anaphunzitsa anthu ake kuti sayenela kukhala ouma mtima mwanjila imeneyi. Anawaphunzitsa kuti afunika kukhala acifundo. Kodi mfundo ya m’lamulo limeneli itiphunzitsa ciani? Itiphunzitsa kuti sitiyenela kulekelela abale athu akuvutika ngati pali zimene tingacite kuti tiwathandize.—Akol. 3:12; Yak. 2:15, 16; ŵelengani 1 Yohane 3:17.

6. Kodi tiphunzilapo ciani pa zimene Yehova anacita pofuna kuthandiza Aisiraeli ocimwa kuti alape?

6 Yehova anamvela cifundo anthu ake Aisiraeli ngakhale pamene anali kum’cimwila. Baibo imati: “Yehova Mulungu wa makolo awo anapitiliza kuwatumizila macenjezo kudzela mwa amithenga ake. Anawatumiza mobwelezabweleza cifukwa ankamvela cisoni anthu akewo ndiponso malo ake okhala.” (2 Mbiri 36:15) Ifenso tifunika kucitila cifundo anthu oona mtima amene angathe kulapa macimo awo kuti Mulungu ayambe kuwakonda. Yehova safuna kuti munthu wina aliyense akawonongeke pa ciweluzo cimene cikubwela. (2 Petulo 3:9) Conco, Mulungu asanawononge anthu oipa, tiyeni tipitilize kulengeza uthenga wocenjeza anthu kuti ambili akapulumuke.

7, 8. N’ciani cinacititsa banja lina kukhulupilila kuti Yehova anawacitila cifundo?

7 Masiku ano, pali zinthu zambili zimene zakhala zikucitika zimene zionetsa kuti Mulungu ni wacifundo. Mwacitsanzo, ganizilani zimene zinacitikila wacicepele wina wa zaka 12, dzina lake Milan ndi a m’banja lake kuciyambi kwa zaka za m’ma 1990. Panthawiyo, m’dziko lawo la Bosnia munali nkhondo ya pakati pa mitundu yosiyana-siyana. Tsiku lina, Milan, mng’ono wake, makolo ake, ndi Mboni zina anali pa ulendo wa pa basi wocoka ku Bosnia kupita ku Serbia. Iwo anali kupita ku msonkhano wacigawo, ndipo makolo ake a Milan anali kuyembekezela kukabatizika kumeneko. Atafika paboda, asilikali anatulutsa Milan ndi onse a m’banja lake m’basimo cifukwa codana ndi mtundu wawo. Koma analola Mboni zinazo kupitiliza ulendo. Atawasunga kwa masiku aŵili, mkulu wa asilikali anatumila foni bwana wake na kum’funsa zimene angawacite abalewo. Popeza kuti msilikaliyo anali pafupi na pamene panali abalewo, iwo anamvela pamene bwana wakeyo anali kukamba kuti, “Mungowatulutsa panja n’kukawawombela mfuti!”

8 Pamene msilikaliyo anali kukambilana ndi ena, anthu aŵili osadziŵika kumene anacokela anafika pamene panali abalewo mwakacete-cete n’kuwauza kuti nawonso ni Mboni. Iwo anamva zimene zinacitikazo kwa abale amene anatsala m’basi ija. Anthuwo anauza Milan na mng’ono wake kuti akwele m’motoka yawo kuti adutse nawo paboda, cifukwa ziphaso za ana sanali kuzifuna. Kenako anauza makolo awo kuti ayende njila yozungulila boda kuti akakumane nawo kutsogolo. Milan anangokhala cete cifukwa ca mantha. Koma makolo ake anafunsa kuti, “Kodi muganiza kuti adzangotilekelela pamene tikucoka?” Ngakhale zinali conco, iwo anacoka bwino-bwino monga kuti asilikaliwo sanali kuwaona. Atafika kumbali ina ya boda, makolowo anakumananso ndi ana awo ndipo anapitiliza ulendo wawo wopita ku msonkhano. Iwo sanakayikile ngakhale pang’ono kuti Yehova anayankha mapemphelo awo. Malinga n’zimene Baibo imakamba, tidziŵa kuti si nthawi zonse pamene Yehova amateteza atumiki ake mwakuthupi. (Mac. 7:58-60) Ngakhale n’conco, Milan anafotokoza mmene anamvelela na zimene zinacitikazo. Iye anati: “N’naona monga kuti angelo anacititsa khungu asilikaliwo ndipo Yehova anatipulumutsa.”—Sal. 97:10.

9. Kodi Yesu anacita ciani ataona cikhamu ca anthu amene anali kumutsatila? (Onani pikica kuciyambi.)

9 Yesu nayenso n’citsanzo cabwino pankhani ya kuonetsa cifundo. Mwacitsanzo, nthawi ina atakumana ndi cikhamu ca anthu, anawamvela cifundo cifukwa “anali onyukanyuka ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa.” Kodi Yesu anacita ciani? “Anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambili.” (Mat. 9:36; ŵelengani Maliko 6:34.) Yesu anali wosiyana kwambili na Afarisi, amene sanali kufuna kuthandiza anthu wamba. (Mat. 12:9-14; 23:4; Yoh. 7:49) Nafenso tifunika kukhala na mtima ngati wa Yesu wofunitsitsa kuthandiza anthu amene ali na njala yauzimu.

10, 11. Kodi tiyenela kuonetsa cifundo nthawi zonse? Fotokozani.

10 Komabe, sikuti tifunika kuonetsa cifundo nthawi zonse. Cifundo cimene Mulungu anaonetsa m’zitsanzo za m’Baibo zimene takambilana m’mapalagilafu apitawa, cinali coyenelela. Mwacitsanzo, nthawi ina Mfumu Sauli anacita zimene anaganiza kuti ni cifundo, koma kunali kusamvela Mulungu. Iye analephela kupha mfumu Agagi, mdani wa anthu a Mulungu. Sanaphenso nkhosa zawo zonenepa bwino. Pa cifukwa cimeneci, Yehova anam’kana kuti asakhalenso mfumu ya Aisiraeli. (1 Sam. 15:3, 9, 15) Yehova ni Woweluza wacilungamo. Iye amadziŵa za mumtima mwa munthu. Amadziŵanso pamene munthu ayenela kucitilidwa cifundo kapena ai. (Maliro 2:17; Ezek. 5:11) Nthawi ikubwela pamene iye adzawononga onse amene safuna kumumvela. (2 Ates. 1:6-10) Panthawi imeneyo, iye sadzamvelanso cifundo anthu amene adzawaweluza kuti ni oipa. Koma adzawaononga pofuna kuonetsa cifundo cake kwa anthu olungama amene adzawapulumutsa.

11 Si udindo wathu kuweluza anthu kuti ni oyenela kuwonongedwa kapena kupulumutsidwa. Koma nchito yathu ni kuyesetsa kuthandiza anthu mmene tingathele. Nanga n’ciani cimene tingacite kuti tionetse kuti timawamvela cifundo anthu? Tiyeni tikambilane zinthu zingapo zimene tingacite.

MMENE TINGAONETSELE CIFUNDO

12. Kodi mungaonetse bwanji cifundo kwa anthu ena?

12 Muzithandiza anthu pa zocitika za tsiku na tsiku. Munthu aliyense amene amatsatila citsanzo ca Yesu amafunika kucitila cifundo anthu ena, kuphatikizapo abale ake auzimu. (Yoh. 13:34, 35; 1 Pet. 3:8) Tanthauzo limodzi la liu lakuti cifundo ni “kuvutikila pamodzi.” Munthu wacifundo amayesetsa kuthandiza anthu amene akuvutika, mwina mwa kuwathandiza kuthetsa vuto lawo. Tiyeni tiziyesetsa kufuna-funa mipata yothandizila ena. Mwacitsanzo, mungathandize wina wake mwa kudzipeleka kum’gwilila nchito zina zapakhomo, kapena kukam’gulila zinthu kumsika.—Mat. 7:12.

Onetsani cifundo kwa ena mwa kuwathandiza pamene afuna thandizo (Onani palagilafu 12)

13. Ni makhalidwe ati a anthu a Mulungu amene amaonekela ngako pakagwa masoka?

13 Muzigwilako nchito yothandiza anthu okhudzidwa na masoka. Anthu ambili akaona anthu ena akuvutika na masoka, amafuna kuwaonetsa cifundo. Anthu a Yehova amadziŵika kwambili kuti amadzipeleka kuthandiza anthu panthawi ya masoka. (1 Pet. 2:17) Mwacitsanzo, mlongo wina wa ku Japan anali kukhala m’dela limene linakhudzidwa kwambili ndi civomezi komanso cigumula ca madzi mu 2011. Iye anakamba kuti “analimbikitsidwa ndi kutonthozedwa kwambili” poona abale odzipeleka ocokela m’madela osiyana-siyana a ku Japan ndi a kumaiko ena. Abalewo anagwila mwakhama nchito yokonzanso Nyumba za Ufumu ndi za anthu zimene zinawonongeka. Iye analemba kuti: “Zimene zinacitikazo zinanithandiza kuzindikila kuti Yehova amatikonda. Zinanithandizanso kuona kuti Akhristu amakondanadi. Abale na alongo oculuka padziko lonse amatipemphelela.”

14. Kodi mungawathandize bwanji odwala na okalamba?

14 Muzithandiza odwala na okalamba. Tikaona anthu akuvutika na zotulukapo zoipa za chimo la Adamu, timawamvela cifundo ndipo timafuna kuwathandiza. Timalakalaka nthawi pamene matenda na ukalamba zidzasila. Conco, timapemphela kuti Ufumu wa Mulungu ubwele. Koma pali pano, timacita zonse zimene tingakwanitse kuti tithandize amene akukumana ndi mavuto amenewa. Ganizilani zimene munthu wina analemba zokhudza amayi ake acikulile, amene anali kudwala matenda a mu ubongo. Iye anakamba kuti tsiku lina amayi akewo anadziwonongela. Pamene anali kuyesa kudzikonza, anamva kugogoda pa citseko. Alendowo anali Mboni ziŵili zimene zinali kubwela kaŵili-kaŵili kunyumba kwawo. Alongowo anafunsa mayiyo ngati afuna thandizo. Iye anayankha kuti: “Zimenezi n’zocititsa manyazi ndithu, koma munithandize.” Alongowo anamuthandizadi. Kenako, anamupangila tiyi ndi kuyamba kuceza naye. Mwana wawo anayamikila ngako. Iye analemba kuti: “A Mboni inu mwanicititsa cidwi kwambili. Mumacitadi zimene mumaphunzitsa.” Nanga bwanji inu? Kodi mumaonetsa cifundo kwa odwala na okalamba mwa kuyesetsa kuwathandiza pa mavuto awo?—Afil. 2:3, 4.

15. Kodi nchito yolalikila imatipatsa mwayi wotani?

15 Muzithandiza anthu mwauzimu. Anthu ali na nkhawa ndipo akukumana ndi mavuto ambili. Izi zimatilimbikitsa kuwathandiza mwauzimu. Njila yabwino kwambili yocitila zimenezi ni kuwaphunzitsa za Mulungu ndi zimene Ufumu wake udzacitila anthu. Njila inanso ni kuwathandiza kuona ubwino wotsatila mfundo za Mulungu pa umoyo wawo. (Yes. 48:17, 18) Kugwila nchito yolalikila kumalemekeza Yehova komanso kumaonetsa kuti timamvela cifundo anthu. Kodi mungawonjezele zocita pa nchito imeneyi?—1 Tim. 2:3, 4.

MUDZAPINDULA NGATI MUCITILA ENA CIFUNDO

16. Kodi munthu amene amacitila ena cifundo amapindula bwanji?

16 Akatswili a zaumoyo amakamba kuti kucitila ena cifundo kungathandize munthu kukhala wathanzi, ndi kukhala na mabwenzi abwino. Ngati muthandiza ena pa mavuto awo, mudzakhala acimwemwe, opanda nkhawa kwambili, ndiponso simudzakhala osungulumwa. Ndithudi, ngati muonetsa ena cifundo, nanunso mudzapindula. (Aef. 4:31, 32) Akhristu amene amayesetsa kuthandiza ena amakhala na cikumbumtima coyela, podziŵa kuti akucita zinthu mogwilizana ndi mfundo za Mulungu. Ngati munthu ni wacifundo, amakhala kholo labwino, mkazi kapena mwamuna wabwino, ndiponso bwenzi labwino. Kaŵili-kaŵili anthu amene amakonda kucitila ena cifundo, nawonso amathandizidwa pamene afunikila thandizo.—Ŵelengani Mateyu 5:7; Luka 6:38.

17. Fotokozani cifukwa cake mufuna kukhala wacifundo.

17 N’zoona kuti munthu amapindula ngati acitila ena cifundo. Koma cimeneci siciyenela kukhala cifukwa cacikulu cokhalila wacifundo. Tifunika kucitila ena cifundo maka-maka cifukwa cofuna kutengela Yehova Mulungu ndi kum’lemekeza monga Gwelo la cikondi na cifundo. (Miy. 14:31) Iye n’citsanzo cabwino kwambili kwa ise pankhani imeneyi. Conco, tiyeni ticite zilizonse zimene tingathe kuti titengele citsanzo cake mwa kucitila ena cifundo. Tikatelo, tidzakhala pa ubwenzi wabwino na Akhristu anzathu komanso ndi anansi athu.—Agal. 6:10; 1 Yoh. 4:16.