Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Acicepele—Cilimikani Polimbana ndi Mdyelekezi

Acicepele—Cilimikani Polimbana ndi Mdyelekezi

“Valani zida zonse zankhondo zocokela kwa Mulungu kuti musasunthike polimbana ndi zocita zacinyengo za Mdyelekezi.”—AEF. 6:11.

NYIMBO: 79, 140

1, 2. (a) N’ciani cimene cikuthandiza Akhristu acicepele kupambana pa nkhondo yolimbana na ziŵanda? (Onani pikica pamwambapa.) (b) Tidzakambilana ciani m’nkhani ino?

MTUMWI Paulo anayelekezela umoyo wathu wacikhristu na asilikali amene akumenyana moyandikana kwambili. Nkhondo imene tikumenya ni yauzimu osati yakuthupi. Ndipo adani athu Satana na ziŵanda, ni amphamvu. Iwo ni aciyambakale ndiponso ni akatswili pa nkhondoyi. Conco, tingaone kuti n’zosatheka kupambana pa nkhondoyi. Maka-maka Akhristu acicepele ndiwo amaoneka kukhala osatetezeka. Koma kodi iwo angapambane pa nkhondo yolimbana na angelo oipa? Inde, angapambane, ndipo akupambana kumene! Nanga n’ciani cimawathandiza? Iwo ‘akupitiliza kupeza mphamvu kucokela kwa Ambuye.’ Kuwonjezela pamenepo, amavala zovala zomenyela nkhondo. Molingana ndi asilikali ophunzitsidwa bwino, iwo ‘amavala zida zonse zankhondo zocokela kwa Mulungu.’—Ŵelengani Aefeso 6:10-12.

2 Pamene Paulo anali kufotokoza fanizo lake, mwina anali kuganizila zida zankhondo zimene asilikali aciroma anali kuvala. (Mac. 28:16) Tiyeni tikambilane cifukwa cake fanizolo n’lofunika. Pamene tikambilana, onani zimene acicepele ena anakamba za mavuto amene amakumana nawo povala cida ciliconse ca nkhondo yauzimu na mapindu amene amapeza.

Kodi Mwavala Zonse za Nkhondo Yauzimu?

LAMBA YA “COONADI”

3, 4. Kodi coonadi ca m’Baibo cili ngati lamba ya msilikali waciroma m’njila yotani?

3 Ŵelengani Aefeso 6:14. Lamba imene asilikali aciroma anali kuvala inali ya tunsimbi topyapyala, tumene tunali kuteteza ciuno cake. Lamba imeneyo inali kuthandiza kuti msilikaliyo asamamvele kulema kwambili akavala codzitetezela pacifuwa. Malambawo anali kukhalanso na tuzitsulo tolimba tokoloŵekapo lupanga na mpeni. Msilikali akamanga bwino lamba yake, anali kumenya nkhondo molimba mtima podziŵa kuti ni wotetezeka.

4 Mofananamo, coonadi cimene timaphunzila m’Mau a Mulungu cimatiteteza ku ziphunzitso zabodza zimene zikhoza kutiwononga mwauzimu. (Yoh. 8:31, 32; 1 Yoh. 4:1) Ngati timacikonda kwambili coonadi, zimakhala zosavuta kunyamula “codzitetezela pacifuwa,” kutanthauza kutsatila miyezo yolungama ya Mulungu mu umoyo wathu. (Sal. 111:7, 8; 1 Yoh. 5:3) Kuwonjezela apo, kumvetsetsa bwino mfundo za coonadi ca Mau a Mulungu, kudzatithandiza kukhala wokonzeka kuteteza molimba mtima coonadi kwa otsutsa.—1 Pet. 3:15.

5. N’cifukwa ciani tifunika kukamba zoona nthawi zonse?

5 Ngati timamvetsetsa coonadi ca m’Baibo, zimakhala ngati kuti tacimanga kwambili m’ciuno mwathu. Ndipo izi zimatilimbikitsa kucita zinthu mogwilizana ndi coonadico na kukamba zoona nthawi zonse. N’cifukwa ciani timapewa kukamba bodza? Cifukwa cakuti bodza ni cimodzi mwa zida zamphamvu zimene Satana amaseŵenzetsa. Bodza imawononga onse aŵili, wonamayo komanso wonamizidwa. (Yoh. 8:44) Conco, olo kuti ndise opanda ungwilo, tifunika kuyesetsa kupewa kunama. (Aef. 4:25) Koma nthawi zina, kucita zimenezi kungakhale kovuta. Abigail, mtsikana wa zaka 18, anati: “Nthawi zina, kukamba zoona kungaoneke monga kosathandiza, maka-maka ngati zioneka kuti kunama kungakupulumutse ku mavuto.” Nanga n’cifukwa ciani iye amayesetsa kukamba zoona nthawi zonse? Abigail anati: “Kukamba zoona kumanithandiza kukhala na cikumbumtima coyela pamaso pa Yehova. Ndipo makolo anga na anzanga amanidalila.” Nayenso Victoria wa zaka 23 anati: “Ngati ukamba zoona na kuikila kumbuyo zimene umakhulupilila, ena angayambe kukuvutitsa. Koma nthawi zonse kucita zimenezi kumatipindulitsa kwambili. Kumatithandiza kukhala wolimba mtima na kuyandikila kwambili Yehova, ndipo anthu amene amatikonda amayamba kutilemekeza.” Inde, tifunika kumanga zolimba lamba ya ‘coonadi m’ciuno mwathu’ nthawi zonse.

Lamba wa coonadi (Onani palagilafu 3-5)

“CODZITETEZELA PACIFUWA CACILUNGAMO”

6, 7. N’cifukwa ciani Baibo imayelekezela cilungamo na codzitetezela pacifuwa?

6 Mtundu wina wa codzitetezela pa cifuwa cimene asilikali aciroma anali kuvala m’nthawi ya atumwi, cinali kukhala na tunsimbi topyapyala toikidwa mosanjikiza. Tunsimbi tumeneto anali kutupinda kuti tuzikwana bwino pa thupi la msilikali, ndipo anali kutumanga na nthambo za cikumba. Pamimba pa msilikaliyo, pacifuwa cake, na pamapewa, monse munali kukhala tunsimbi topyapyala tomangiwa na nthambo za cikumba. Covalaco cinali kupangitsa kuti iye asamakhale womasuka kweni-kweni poyenda, ndipo nthawi na nthawi anali kufunikila kumaona ngati tunsimbito tukali togwila bwino. Ngakhale zinali conco covalaco cinali kumuteteza ku lupanga kapena mivi ya adani kuti isavulaze mtima wake kapena ziwalo zina zofunika kwambili za thupi.

7 Ndithudi! Ici n’cizindikilo coyenelela kwambili coonetsa mmene miyezo yolungama ya Yehova imatetezela mtima wathu wophiphilitsa. (Miy. 4:23) Msilikali sangasinthanitse codzitetezela pacifuwa copangiwa na citsulo colimba n’kutenga cina copangiwa na citsulo cosalimba. Na ise n’cimodzi-modzi. Sitifunika kusinthanitsa miyezo yolungama ya Yehova na miyezo yathu. Sitiyenela kudalila nzelu zathu cifukwa sizingatithandize kukhala otetezeka. (Miy. 3:5, 6) M’malomwake, mofanana ndi msilikali amene anali kuonetsetsa kuti tunsimbi twa codzitetezela pa cifuwa n’togwila bwino, tifunika kuonetsetsa kuti mfundo za Yehova ni zozikika mozama mu mtima mwathu.

8. Kodi kumamatila ku miyezo ya Yehova kuli na mapindu anji?

8 Kodi nthawi zina mumaona kuti miyezo yolungama ya Yehova ni yolemetsa kapena yovuta? Daniel, wa zaka 21, anati: “Ana asukulu anzanga na matica anali kuniseka cifukwa cakuti nimakonkha miyezo ya m’Baibo. Cifukwa ca zimenezi, n’nayamba kudzikayikila na kuvutika maganizo.” N’ciani cinam’limbikitsa Daniel kuti asafooke? Iye anati: “M’kupita kwa nthawi, n’naona mapindu amene amabwela cifukwa cotsatila miyezo ya Yehova. Anzanga ena anayamba kuseŵenzetsa amkolabongo, ndipo ena analeka sukulu. Cinali comvetsa cisoni kuona mavuto amene anakumana nawo. Ndithudi! Yehova amatiteteza.” Madison, wa zaka 15, anati “Cimanivuta kutsatila miyezo ya Yehova kuti n’satengele zimene anzanga amaona kuti ndiye zabwino kapena zokondweletsa.” Kodi Madison amacita ciani kuti asagonje? Iye anati: “Nimayesetsa kukumbukila kuti ndine Mboni ya Yehova na kuti ciyeso ni njila imene Satana amaseŵenzetsa pofuna kunigonjetsa. Nikapambana ciyeso, nimamvela bwino ngako.”

Codzitetezela pacifuwa cacilungamo (Onani palagilafu 6-8)

“MAPAZI ANU MUTAWAVEKA NSAPATO ZOKONZEKELA UTHENGA WABWINO WAMTENDELE”

9-11. (a) Kodi nsapato zophiphilitsa zimene Akhristu amavala n’ciani? (b) N’ciani cingatithandize kuti tizilalikila momasuka uthenga wabwino?

9 Ŵelengani Aefeso 6:15. Msilikali waciroma ngati sanavale nsapato, ndiye kuti sanali wokonzeka kumenya nkhondo. Nsapato zake zokhala ngati masandasi zinali na nthambo zambili zacikumba zomangidwa bwino pamodzi kuti akazivala zizigwila bwino mapazi ake. Cifukwa ca mmene anali kuzipangila, nsapatozo zinali kukhala zolimba ndi zosavuta kuyenda nazo.

10 Nsapato zimene asilikali aciroma anali kuvala zinali zopita nazo ku nkhondo. Koma nsapato zophiphilitsa zimene Akhristu amavala, zimawathandiza polalikila uthenga wa mtendele. (Yes. 52:7; Aroma 10:15) Ngakhale n’conco, Mkhristu amafunika kulimba mtima kuti alalikile pamene mpata wapezeka. Mnyamata wina wa zaka 20, dzina lake Bo, anati: “N’nali kuyopa kulalikila anzanga a m’kilasi. N’nali kucita manyazi. Koma niona kuti panalibe cifukwa cocitila manyazi. Lomba, nimakondwela kulalikila anzanga.”

11 Acicepele ambili aona kuti ngati akonzekela bwino ulaliki, zimakhala zosavuta kulalikila uthenga wabwino kwa ena. Kodi mungakonzekele bwanji? Julia, wa zaka 16, anati: “Nimakhala na zofalitsa m’cola canga ca ku sukulu. Komanso, nimayesetsa kumvetsela zimene anzanga amakamba kuti nidziŵe maganizo awo na zikhulupililo zawo. Mwa ici, nimakwanitsa kudziŵa zimene zingawathandize. Nikakhala wokonzeka, nimakwanitsa kukamba nawo mfundo zimene zingawapindulitse.” Makenzie, wa zaka 23, anati: “Ngati anzako umacita nawo zinthu mokoma mtima na kuwamvetsela mwaubwenzi, umadziŵa zovuta zimene akukumana nazo. Ine nimaonetsetsa kuti naŵelenga nkhani na zofalitsa zonse zokhudza acicepele. Mwa ici, nimatha kuwaonetsa mfundo za m’Baibo kapena zofalitsa za pa jw.org zimene zingawathandize.” Malinga n’zimene acicepelewa anafotokoza, pamene mwakonzekela bwino ulaliki m’pamenenso “nsapato” zanu zophiphilitsa zimakhala zogwila bwino ku mapazi anu.

Mapazi ovekedwa nsapato zokonzekela uthenga wabwino (Onani palagilafu 9-11)

“CISHANGO CACIKULU CACIKHULUPILILO”

12, 13. Kodi ina mwa “mivi yoyaka moto” ya Satana ni iti?

12 Ŵelengani Aefeso 6:16. “Cishango cacikulu” cimene msilikali waciroma anali kunyamula cinali ca makona 4, ndipo cinali cacitali bwino, moti cinali kumuteteza kucokela m’mapewa mpaka m’mawondo. Cishango cimeneci cinali kumuteteza ku zida zina na mivi imene adani anali kuponya.

13 Mivi ina “yoyaka moto” imene Satana angakuponyeleni ndiyo kufalitsa mabodza akuti Yehova sakuonani monga ofunika ndiponso sakukondani. Ida wa zaka 19, wakhala akuvutika na maganizo odziona monga wosafunika. Iye anati: “Nthawi zambili, nimaona ngati kuti Yehova ali nane patali ndipo safuna kukhala Mnzanga.” Kodi Ida amacita ciani polimbana na vuto imeneyi? Iye anati: “Misonkhano imalimbitsa kwambili cikhulupililo canga. Kale, n’nali kungopezeka pa misonkhano koma osayankhapo, poganiza kuti palibe aliyense amene angamvetsele zokamba zanga. Koma lomba nimakonzekela misonkhano na kuyesetsa kuyankhapo, kaŵili kapena katatu. Zimanivuta, koma nimamvela bwino kwambili nikayankhapo. Komanso, abale na alongo amanilimbikitsa maningi. Conco, nthawi zonse pamene nicoka ku misonkhano, nimakhala wotsimikiza kuti Yehova amanikonda.”

14. Ni mfundo yofunika iti imene tiphunzilapo pa citsanzo ca Ida?

14 Citsanzo ca Ida citiphunzitsa mfundo inayake yofunika kwambili. Cishango ceni-ceni cimene msilikali anganyamule, saizi yake siimasintha, koma cishango cathu cacikhulupililo cingakule kapena kucepa. Zimadalila pa zimene timacita. (Mat. 14:31; 2 Ates. 1:3) Conco, kukulitsa cikhulupililo cathu n’kofunika ngako.

Cishango cacikulu cacikhulupililo (Onani palagilafu 12-14)

“CISOTI COLIMBA CACIPULUMUTSO”

15, 16. Kodi ciyembekezo cili monga cisote ca msilikali m’lingalilo lanji?

15 Ŵelengani Aefeso 6:17. Cisoti cimene msilikali waciroma anali kuvala cinali kuteteza mutu wake, khosi, na nkhope yake ku zida za adani. Visote vina vinali kukhala na cogwilila kotelo kuti nthawi zina msilikali anali kucinyamula kumanja.

16 Monga mmene cisote cimatetezela mutu na ubongo wa msilikali, “ciyembekezo cacipulumutso” cimateteza maganizo athu, na kutithandiza kuti tiziganiza bwino. (1 Ates. 5:8; Miy. 3:21) Ciyembekezo cimatithandiza kuikabe maganizo athu pa malonjezo a Mulungu. Cimatithandizanso kuona mavuto moyenelela. (Sal. 27:1, 14; Mac. 24:15) Koma kuti ‘cisote’ cathu cimeneci cititeteze bwino, tifunika kucivala osati kucinyamula kumanja.

17, 18. (a) Kodi Satana angatipangitse bwanji kuvula cisoti cathu? (b) Tingaonetse bwanji kuti sitinapusitsike na cinyengo ca Satana?

17 Kodi Satana angatipangitse bwanji kuvula cisote cathu? Ganizilani zimene iye anacita kwa Yesu. Satana anali kudziŵa kuti Yesu anali na ciyembekezo cokakhala mfumu yolamulila mtundu wa anthu. Koma Yesu anafunika kuyembekezela mpaka pa nthawi yoikika ya Yehova. Ndipo akalibe kukhala mfumu, iye anafunika kukumana na mavuto na kuphedwa. Koma Satana anapatsa Yesu mwayi wakuti angakhale mfumu mwamsanga nthawi ya Yehova isanakwane. Iye anauza Yesu kuti akamulambila kamodzi kokha cabe, adzakhala mfumu pa nthawi imeneyo. (Luka 4:5-7) Mofananamo, Satana amadziŵa kuti Yehova analonjeza kuti adzatipatsa zinthu zambili zabwino m’dziko latsopano. Koma tifunika kuziyembekezela, ndipo pali pano tikhoza kukumana na mavuto ambili. Conco, Satana amatiyesa mwa kutipatsa mwayi wakuti tikhale na zinthu zambili zakuthupi pa nthawi ino. Iye amafuna kuti tizifuna-funa zinthu zakuthupi coyamba, pofuna kudzipezela umoyo wabwino. Satana amafuna kuti tiziika zinthu za Ufumu pa malo aciŵili mu umoyo wathu.—Mat. 6:31-33.

18 Akhristu ambili acicepele sanapusitsike na cinyengo ca Satana cimeneci. Mmodzi wa iwo ni mlongo Kiana, wa zaka 20. Iye anati: “Nidziŵa kuti ni Ufumu wa Mulungu cabe umene udzacotsapo mavuto athu onse.” Kodi ciyembekezo cake colimba cimakhudza bwanji maganizo na zocita zake? Iye anakamba kuti: “Ciyembekezo ca Paladaiso cimanithandiza kuika zolinga zakuthupi pa malo oyenelela. Nimapewa kuseŵenzetsa maluso anga pofuna cabe kudzipindulitsa kapena kupeza nchito yapamwamba. M’malomwake, nimaseŵenzetsa nthawi na mphamvu zanga pokwanilitsa zolinga zauzimu.”

Cisoti colimba cacipulumutso (Onani palagilafu 15-18)

“LUPANGA LA MZIMU,” LIMENE NI MAU A MULUNGU

19, 20. Kodi tingakulitse bwanji luso la mmene timaseŵenzetsela Mau a Mulungu?

19 M’nthawi imene Paulo anali kulemba kalata yopita kwa Aefeso, lupanga limene asilikali aciroma anali kuseŵenzetsa linali lalitali masentimita 50. Ndipo linali kupangidwa m’njila yakuti lizigwilitsidwa nchito pa nkhondo yomenyana moyandikana. Cifukwa cimodzi cimene asilikali aciroma anali kucitila bwino pa nkhondo, n’cakuti tsiku lililonse anali kuyeseza mmene angaseŵenzetsele malupanga awo.

20 Paulo anakamba kuti Mau a Mulungu amene Yehova watipatsa ali monga lupanga. Komabe, tifunika kuphunzila mmene tingaseŵenzetsele mwaluso lupanga limeneli poikila kumbuyo zikhulupililo zathu, kapena powongolela maganizo athu. (2 Akor. 10:4, 5; 2 Tim. 2:15) Kodi tingakulitse bwanji luso la mmene timaseŵenzetsela Mau a Mulungu? Sebastian, wa zaka 21, anati: “Pamene niŵelenga Baibo, nimalemba vesi imodzi m’caputa iliyonse, na kuika pamodzi mavesi anga a pamtima. Izi zathandiza kuti maganizo anga akhale ogwilizana kwambili na maganizo a Yehova.” Komanso Daniel, amene tamuchula kuciyambi, anati: “Poŵelenga Baibo, nimasankha mavesi amene niona kuti adzakhala othandiza kwa anthu amene nimakumana nawo mu ulaliki. Naona kuti anthu amamvetsela kwambili akazindikila kuti umaikonda Baibo komanso umayesetsa kuwathandiza.”

Lupanga la mzimu (Onani palagilafu 19-20)

21. N’cifukwa ciani sitifunika kumuyopa Satana na ziŵanda?

21 Monga mmene taonela kwa acicepele amene tawagwila mau m’nkhani ino, palibe cifukwa comuyopela Satana na ziŵanda zake. Iwo ni amphamvu, koma sikuti ni osagonjetseka. Kuwonjezela apo, sadzakhala na moyo kwamuyaya. Posacedwa, mu Ulamulilo wa Khristu wa Zaka 1,000, iwo adzaponyedwa ku phompho, kumene sadzakhalanso na mphamvu zocita ciliconse. Pambuyo pake, adzawonongedwa. (Chiv. 20:1-3, 7-10) Mdani wathu timam’dziŵa bwino. Timawadziŵanso bwino macenjela ake. Ndipo mwa thandizo la Yehova, tingathe kucilimika polimbana naye!