GAO 14
Kodi Mungaonetse Bwanji Kuti Ndinu Okhulupilika kwa Yehova?
Khalani kumbali ya Mulungu. 1 Petulo 5:6-9
Muzipewa miyambo yonse imene simagwilizana ndi Baibo. Kuti mucite zimenezi, muyenela kulimba mtima.
Musaziloŵa m’ndale; sizimacilikiza Yehova ndi Ufumu wake.
Mateyu 7:24, 25
Sankhani mwanzelu—mvetselani kwa Mulungu.Gwilizanani ndi Mboni za Yehova; zidzakuthandizani kuyandikila kwa Mulungu.
Pitilizani kuphunzila za Mulungu ndi kuyesa-yesa kumvela malamulo ake.
Cikhulupililo canu cikalimba, muyenela kudzipeleka kwa Yehova ndi kubatizika.—Mateyu 28:19.
Mvetselani kwa Mulungu. Ŵelengani Baibo, ndi kufunsa Mboni za Yehova kuti zikuthandizeni kuimvetsetsa. Ndipo seŵenzetsani zimene mukuphunzila. Mukacita zimenezi, mudzakhala ndi moyo wamuyaya.—Salimo 37:29.