Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 51

Kodi Mungamukondweletse Bwanji Yehova na Malankhulidwe Anu?

Kodi Mungamukondweletse Bwanji Yehova na Malankhulidwe Anu?

Yehova potilenga anatipatsa mphatso yapadela kwambili—luso la kulankhula. Kodi zimamukhudza iye mmene timagwilitsila nchito mphatso imeneyi? Inde zimamukhudzadi! (Ŵelengani Yakobo 1:26.) Conco, kodi luso la kulankhula tingaligwilitse nchito motani kuti tizikondweletsa Yehova?

1. Kodi mphatso ya kulankhula tiyenela kuigwilitsa nchito motani?

Baibo imakamba kuti “pitilizani kutonthozana ndi kulimbikitsana.” (1 Atesalonika 5:11) Kodi mungaganizileko anthu ena ofunikila cilimbikitso? Kodi tingathandize bwanji kuti akhale olimbikitsika? Auzeni kuti mumawaganizila kwambili. Achulileni mbali zimene mumawayamikila. Kodi mungaganizileko lemba limene mungalimbikitse nalo munthu wina amene mumam’dziŵa? Malemba alipo ambili amene mungasankhepo. Kumbukilaninso kuti, njila imene mukukambila zinthu ingakhumudwitse munthu kwambili, mofanana na mawu enieniwo. Conco, yesetsani nthawi zonse kumalankhula mokoma mtima komanso modekha.—Miyambo 15:1.

2. Kodi tiyenela kupewa malankhulidwe otani?

Baibo imakamba kuti: “Mawu alionse owola asatuluke pakamwa panu.” (Ŵelengani Aefeso 4:29.) Izi zikutanthauza kuti sitiyenela kukamba mawu otukwana, ankhanza kapena acipongwe, amene angakhumudwitse munthu. Tiyenelanso kupewa mijedo yovulaza komanso misece.—Ŵelengani Miyambo 16:28.

3. Kodi n’ciyani cingatithandize kumalankhula m’njila yolimbikitsana?

Kambili zinthu zimene timakambapo, zimaonetsa zimene zili mumtima mwathu na m’maganizo mwathu. (Luka 6:45) Conco, tiyenela kudzizoloŵeza kumaganizila zinthu zolungama, zoyela, zacikondi, komanso zoyamikilika. (Afilipi 4:8) Kuti maganizo athu azikhazikika pa zinthu zimenezi, tiyenela kusankha mwanzelu zosangalatsa komanso mabwenzi. (Miyambo 13:20) Cinanso cingatithandize ni kuyamba taganiza tisanalankhule. Ganizilani mmene mawu anu angakhudzile anthu ena. Baibo imakamba kuti: “Pali munthu amene amalankhula mosaganizila ndi mawu olasa ngati lupanga, koma lilime la anthu anzelu limacilitsa.”Miyambo 12:18.

KUMBANI MOZAMILAPO

Phunzilani kulankhula m’njila yokondweletsa Yehova, komanso yolimbikitsa anthu ena.

4. Khalani odziletsa pa malankhulidwe anu

Nthawi zina, timakamba zinthu zimene timamva nazo kuipa pambuyo pake. (Yakobo 3:2) Ŵelengani Agalatiya 5:22, 23, na kukambilana mafunso aya:

  • Pa makhalidwe ali pa lembali, ni makhalidwe ati angakuthandizeni kukhala wodziletsa pa kalankhulidwe kanu? Ndipo makhalidwe amenewa angakuthandizeni bwanji?

Ŵelengani 1 Akorinto 15:33, na kukambilana funso ili:

  • Kodi mabwenzi amene mumasankha, komanso zosangalatsa, zingakhudze bwanji malankhulidwe anu?

Ŵelengani Mlaliki 3:1, 7, na kukambilana funso ili:

  • Kodi ni panthawi iti pamene mungacite mwanzelu kukhala cete, kapena kuyembekeza nthawi yabwino kuti mukambe zinazake?

5. Muzikamba zabwino za ena

Kodi tingapewe bwanji kunyoza anthu ena kapena kuwakambila zoipa? Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso otsatila.

  • Mu vidiyo imeneyi, n’cifukwa ciyani m’baleyu anaona kuti ayenela kusintha mmene anali kulankhulila za anthu ena?

  • Kodi anacita ciyani kuti asinthe?

Ŵelengani Mlaliki 7:16, na kukambilana funso ili:

  • Kodi tiyenela kukumbukila ciyani tisanakambe zoipa za munthu wina?

Ŵelengani Mlaliki 7:21, 22, na kukambilana funso ili:

  • Kodi lemba limeneli lingakuthandizeni bwanji kusakwiya mopitilila malile, pamene munthu wina wakukambilani zoipa?

6. Khalani wokoma mtima polankhula kwa a m’banja mwanu

Yehova amafuna kuti m’banja mwathu tizikambilana mokoma mtima komanso mwacikondi. Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso aya.

  • Cingakuthandizeni n’ciyani kumalankhula mokoma mtima kwa a m’banja mwanu?

Ŵelengani Aefeso 4:31, 32, na kukambilana funso ili:

  • Kodi ni malankhulidwe otani amene amamangiliza banja?

Yehova anaonetsa mmene amamukondela Mwana wake, Yesu. Ŵelengani Mateyu 17:5, na kukambilana funso ili:

  • Kodi mungatengele bwanji citsanzo ca Yehova polankhula kwa a m’banja mwanu?

Yesani kupeza mipata yolimbikitsa anthu ena

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Nimakamba za kukhosi kwanga. Ngati ena sakondwela nazo, ilo si vuto langa.”

  • Kodi inunso mukuvomeleza zimenezi? Cifukwa ciyani?

CIDULE CAKE

Mawu ali na mphamvu kwambili. Tiyenela kuganiza mosamala zimene tifuna kukamba, pozikambila, komanso mozikambila.

Mafunso Obweleza

  • Kodi malankhulidwe anu mungathandize nawo anthu ena m’njila ziti?

  • Ni malankhulidwe otani amene muyenela kupewa?

  • N’ciyani cingatithandize kuti malankhulidwe athu azikhala okoma mtima, komanso omangiliza nthawi zonse?

Colinga

FUFUZANI

N’ciyani cingatithandize kukhala na makambidwe abwino?

Khalani Ndi Lilime la Anthu Anzeru (8:04)

Onani cingakuthandizeni kupewa mawu onyoza kapena otukwana.

“Kodi Kutukwana N’koipadi? (Nkhani ya pawebusaiti)

Onani mmene mungapewele msampha wa mijedo yovulaza.

Ningacite Ciani Kuti Nileke Mijedo? (2:36)

Onani mmene Yehova anathandizila munthu wina amene anali na vuto la kutukwana.

“Ndinayamba Kuganizira Kwambiri za Moyo Wanga” (Nsanja ya Olonda, August 1, 2013)