Maulaliki a Citsanzo
GALAMUKANI!
Funso: Kodi Baibo ni yocokeladi kwa Mulungu? Kapena ni buku lodzala na maganizo a anthu?
Lemba: 2 Tim. 3:16
Cogaŵila: Galamukani! ino ifotokoza maumboni atatu oonetsa kuti Baibo ni yocokeladi kwa Mulungu.
PHUNZITSANI COONADI
Funso: Kodi mphatso ya moyo tiyenela kuiona bwanji?
Lemba: Chiv. 4:11
Coonadi: Popeza moyo ni mphatso yocokela kwa Mulungu, timaulemekeza. Timayesetsa kupewa ngozi, ndipo sitingayese kupha munthu mwadala. Timalemekeza kwambili mphatso imeneyi ya moyo.
KODI COFUNIKA N’CIANI KUTI BANJA LIKHALE LAMTENDELE?
Funso: Onani funso limene lili pa kapepa aka kauthenga na mayankho amene alipo. Imwe muganiza bwanji?
Lemba: Luka 11:28
Cogaŵila: Kapepa kauthenga aka kafotokoza phindu limene mungapeze ngati mutsatila malangizo a m’Baibo pabanja lanu ndiponso cifukwa cake tiyenela kukhulupilila zimene Baibo imakamba.
KONZANI ULALIKI WANU
Funso:
Lemba:
Cogaŵila: