UMOYO WATHU WACIKHIRISTU
Kukhala na Umoyo Wosafuna Zambili Kudzatithandiza Kutamanda Mulungu
Masiku ano, n’zosavuta kucolowanitsa moyo wathu na zinthu zambili. Zimafuna nthawi yozigula, kuzilipilila msonkho, kuzisamalila ndi kuziteteza. Yesu anali na umoyo wosafuna zambili. Anacita zimenezi n’colinga cakuti zinthu za kuthupi zisamucenjeneke pa utumiki wake.—Mat. 8:20.
Kodi mungacite ciani kuti mukhale na umoyo wosafuna zambili pofuna kucita zowonjezeleka mu utumiki? Kodi mungasinthe zina ndi zina kuti wina m’banja lanu akhale mpainiya? Ngati muli kale mu utumiki wa nthawi zonse, kodi mwayamba kulola zinthu zakuthupi kukucenjenekani? Kukhala ndi umoyo wosafuna zambili potumikila Yehova, kumakhala kokondweletsa ndipo kumafuna kukhala okhutila ndi zimene uli nazo —1 Tim. 6:7-9.
Lembani zimene mungacite kuti mukhale na umoyo wosafuna zambili: