Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

August 31–September 6

EKSODO 21-22

August 31–September 6

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

  • Muzionetsa kuti Mumaona Moyo Mmene Yehova Amauonela”: (10 min.)

    • Eks. 21:20—Yehova amaletsa kupha munthu (it-1 271)

    • Eks. 21:22, 23—Yehova amaona moyo wa mwana wosabadwa kukhala wamtengo wapatali (lvs 95 ¶16)

    • Eks. 21:28, 29—Yehova amafuna kuti tizitsatila malangizo acitetezo (w10 4/15 29 ¶4)

  • Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (10 min.)

    • Eks. 21:5, 6—Malinga na mavesiwa, kodi tikadzipatulila kwa Yehova timapindula motani? (w10 1/15 4 ¶4-5)

    • Eks. 21:14—Kodi mfundo ya palembali tingaifotokoze motani? (it-1 1143)

    • Pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?

  • Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Eks. 21:1-21 (th phunzilo 5)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

  • Nyimbo 60

  • Muziona Moyo Mmene Mulungu Amauonela: (10 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyoyi. Ndiyeno funsani omvetsela: Kodi pa nthawi imene mayi ali na pakati pangabuke zovuta zotani? Kodi lemba la Ekisodo 21:22, 23 ili na mfundo yanji pankhani ya kucotsa mimba? N’cifukwa ciani cikhulupililo na kulimba mtima n’zofunika kuti tipange cosankha cokondweletsa Yehova? Kodi ciyembekezo ca ciukililo cimatitonthoza bwanji?

  • Mmene Kudzipatulila Kumatipindulitsila: (5 min.) Nkhani yozikidwa mu Nsanja Yolonda ya January 15, 2010, peji 4, mapalagilafu 4-7. Limbikitsani ophunzila Baibo kuti apite patsogolo kuti akadzipatulile na kubatizika.

  • Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 130

  • Mawu Othela (3 min. olo kucepelapo)

  • Nyimbo 15 na Pemphelo