Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Macitidwe a Atumwi

Macaputala

Za m'Bukuli

  • 1

    • Mawu opita kwa Teofilo (1-5)

    • Kucitila umboni mpaka kumalekezelo a dziko lapansi (6-8)

    • Yesu apita kumwamba (9-11)

    • Ophunzila asonkhana pamodzi mogwilizana (12-14)

    • Matiya asankhidwa kuti alowe m’malo Yudasi (15-26)

  • 2

    • Anthu alandila mzimu woyela pa Pentekosite (1-13)

    • Nkhani imene Petulo anakamba (14-36)

    • Khamu la anthu licitapo kanthu pa nkhani imene Petulo anakamba (37-41)

      • Anthu 3,000 abatizidwa (41)

    • Akhristu acitila zinthu pamodzi (42-47)

  • 3

    • Petulo acilitsa munthu wolemala wopemphapempha (1-10)

    • Nkhani imene Petulo anakamba pa Khonde la Zipilala la Solomo (11-26)

      • “Kubwezeletsa zinthu zonse” (21)

      • Mneneli ngati Mose (22)

  • 4

    • Petulo ndi Yohane amangidwa (1-4)

      • Amuna okhulupilila akwana 5,000 (4)

    • Aweluzidwa pamaso pa Khoti Yaikulu ya Ayuda (5-22)

      • “Ife sitingaleke kulankhula” (20)

    • Apemphela kuti akhale olimba mtima (23-31)

    • Ophunzila agawana zinthu (32-37)

  • 5

    • Hananiya ndi Safira (1-11)

    • Atumwi acita zizindikilo zambili (12-16)

    • Amangidwa kenako amasulidwa (17-21a)

    • Apelekedwanso ku Khoti Yaikulu ya Ayuda (21b-32)

      • ‘Kumvela Mulungu osati anthu’ (29)

    • Ulangizi wa Gamaliyeli (33-40)

    • Kulalikila kunyumba ndi nyumba (41, 42)

  • 6

    • Amuna 7 asankhidwa kuti atumikile (1-7)

    • Sitefano aimbidwa mlandu wonyoza Mulungu (8-15)

  • 7

    • Sitefano alankhula pamaso pa Khoti Yaikulu ya Ayuda (1-53)

      • Nthawi ya makolo akale (2-16)

      • Utsogoleli wa Mose; Aisiraeli alambila mafano (17-43)

      • Mulungu sakhala mu akacisi opangidwa ndi anthu (44-50)

    • Sitefano aponyedwa miyala (54-60)

  • 8

    • Saulo azunza ophunzila (1-3)

    • Utumiki wa Filipo ubala zipatso ku Samariya (4-13)

    • Petulo ndi Yohane atumidwa ku Samariya (14-17)

    • Simoni afuna kugula mzimu woyela (18-25)

    • Nduna ya ku Itiyopiya (26-40)

  • 9

    • Saulo ali pa ulendo wopita ku Damasiko (1-9)

    • Hananiya atumizidwa kuti akathandize Saulo (10-19a)

    • Saulo alalikila za Yesu ku Damasiko (19b-25)

    • Saulo apita ku Yerusalemu (26-31)

    • Petulo acilitsa Eneya (32-35)

    • Dorika wowolowa manja aukitsidwa (36-43)

  • 10

    • Masomphenya a Koneliyo (1-8)

    • Petulo aona masomphenya a nyama zoyeletsedwa (9-16)

    • Petulo apita kunyumba kwa Koneliyo (17-33)

    • Petulo alengeza uthenga wabwino kwa anthu a mitundu ina (34-43)

      • “Mulungu alibe tsankho” (34, 35)

    • Anthu a mitundu ina alandila mzimu woyela ndipo abatizidwa (44-48)

  • 11

    • Petulo apeleka lipoti kwa atumwi (1-18)

    • Baranaba ndi Saulo ku Antiokeya wa ku Siriya (19-26)

      • Ophunzila ayamba kuchedwa Akhristu (26)

    • Agabo alosela za njala (27-30)

  • 12

    • Yakobo aphedwa; Petulo aponyedwa m’ndende (1-5)

    • Petulo amasulidwa mozizwitsa (6-19)

    • Herode akanthidwa ndi mngelo (20-25)

  • 13

    • Baranaba ndi Saulo atumizidwa ngati amishonale (1-3)

    • Utumiki wa ku Kupuro (4-12)

    • Zimene Paulo anakamba ku Antiokeya wa ku Pisidiya  (13-41)

    • Ulosi wakuti ayambe kulalikila anthu a mitundu ina (42-52)

  • 14

    • Okhulupilila awonjezeka ku Ikoniyo ndipo ayamba kutsutsidwa (1-7)

    • Aonedwa monga milungu ku Lusitara (8-18)

    • Paulo apulumuka atamuponya miyala (19, 20)

    • Kulimbikitsa mipingo (21-23)

    • Abwelela ku Antiokeya wa ku Siriya (24-28)

  • 15

    • Atsutsana pa nkhani ya mdulidwe ku Antiokeya (1, 2)

    • Apeleka nkhaniyi ku Yerusalemu (3-5)

    • Akulu ndi atumwi akumana pamodzi (6-21)

    • Kalata yocokela ku bungwe lolamulila (22-29)

    • Mipingo ilimbikitsidwa ndi kalata (30-35)

    • Paulo ndi Baranaba apatukana (36-41)

  • 16

    • Paulo asankha Timoteyo (1-5)

    • Munthu wa ku Makedoniya aonekela m’masomphenya (6-10)

    • Lidiya akhala Mkhristu ku Filipi (11-15)

    • Paulo ndi Sila aponyedwa m’ndende (16-24)

    • Woyang’anila ndende ndi a m’banja lake abatizika (25-34)

    • Paulo apempha akuluakulu a zamalamulo kuti apepese (35-40)

  • 17

    • Paulo ndi Sila ku Tesalonika (1-9)

    • Paulo ndi Sila ku Bereya (10-15)

    • Paulo ku Atene (16-22a)

    • Zimene Paulo ananena ku bwalo la Areopagi  (22b-34)

  • 18

    • Utumiki wa Paulo ku Korinto (1-17)

    • Abwelela ku Antiokeya wa ku Siriya (18-22)

    • Paulo acoka n’kupita ku Galatiya ndi ku Filigiya (23)

    • Apolo wolankhula mwaluso athandizidwa (24-28)

  • 19

    • Paulo ku Efeso; ena abatizika kaciwili (1-7)

    • Nchito yophunzitsa ya Paulo (8-10)

    • Apeza cipambano ngakhale kuti ena anali kukhulupilila zamizimu (11-20)

    • Cipolowe ku Efeso (21-41)

  • 20

    • Paulo ku Makedoniya ndi ku Girisi (1-6)

    • Utiko aukitsidwa ku Torowa (7-12)

    • Acoka ku Torowa n’kupita ku Mileto (13-16)

    • Paulo akumana ndi akulu a ku Efeso (17-38)

      • Aphunzitsa kunyumba ndi nyumba (20)

      • “Kupatsa kumabweletsa cimwemwe cacikulu” (35)

  • 21

    • Ulendo wa ku Yerusalemu (1-14)

    • Afika ku Yerusalemu (15-19)

    • Paulo atsatila malangizo a akulu (20-26)

    • Cipolowe m’kacisi; Paulo agwidwa (27-36)

    • Paulo aloledwa kuti alankhule ndi khamu la anthu (37-40)

  • 22

    • Mawu a Paulo odziteteza pamaso pa khamu la anthu (1-21)

    • Paulo agwilitsa nchito unzika wake wokhala m’Roma (22-29)

    • Khoti Yaikulu ya Ayuda isonkhana (30)

  • 23

    • Paulo alankhula pamaso pa Khoti Yaikulu ya Ayuda (1-10)

    • Ambuye alimbikitsa Paulo (11)

    • Ciwembu cofuna kupha Paulo (12-22)

    • Paulo atumizidwa ku Kaisareya (23-35)

  • 24

    • Paulo aimbidwa milandu (1-9)

    • Paulo adziteteza pamaso pa Felike (10-21)

    • Mlandu wa Paulo uyedzekedwa kwa zaka ziwili (22-27)

  • 25

    • Paulo afotokoza mlandu wake pamaso pa Fesito (1-12)

      • “Ndikucita apilo kuti ndikaonekele kwa Kaisara!” (11)

    • Fesito afunsila nzelu kwa Mfumu Agiripa (13-22)

    • Paulo aonekela pamaso pa Agiripa (23-27)

  • 26

    • Paulo adziteteza pamaso pa Agiripa (1-11)

    • Paulo afotokoza mmene anakhalila Mkhristu (12-23)

    • Zimene Fesito ndi Agiripa anacita (24-32)

  • 27

    • Paulo ayamba ulendo wa panyanja wopita ku Roma (1-12)

    • Namondwe awomba ngalawa (13-38)

    • Ngalawa ipasuka (39-44)

  • 28

    • Gombe la ku Melita (1-6)

    • Atate ake Papuliyo acilitsidwa (7-10)

    • Ulendo wa ku Roma (11-16)

    • Paulo alankhula ndi Ayuda ku Roma (17-29)

    • Paulo alalikila molimba mtima kwa zaka ziwili (30, 31)