JANUARY 21, 2014
RUSSIA
Akuluakulu a Boma la Russia Akupempha Chilolezo cha Khoti kuti Aletse Webusaiti Yotchuka Yophunzitsa Baibulo
ST. PETERSBURG, Russia—Pa August 7, 2013, khoti la Tsentralniy District mumzinda wa Tver, womwe uli pa mtunda wa makilomita 100 kuchokera mumzinda wa Moscow, linagamula kuti webusaiti yophunzitsa Baibulo ya jw.org iletsedwe m’dziko lonse la Russia.
Anthu ambiri amagwiritsira ntchito webusaitiyi, kuphatikizapo akatswiri ena ofufuza zinthu. Ngakhale zili chonchi, akuluakulu a boma la Russia komanso akhoti anagwirizana zoti iletsedwe. Khoti linapereka chigamulo popanda kudziwitsa kapena kumva maganizo a eni webusaitiyi omwe ndi a Watchtower Bible and Tract Society of New York. A Mboni za Yehova akuchita apilo chigamulochi kukhoti lina la Tver Regional. Khotili lidzaonanso chigamulo cha khoti loyamba pa January 22, 2014.
Ngati khoti la Tver Regional Court likane apilo ya a Mboni, ndiye kuti webusaitiyi sidzapezekanso kwa a Mboni za Yehova 160,000 a m’dziko la Russia. A Mboniwa amakonda kugwiritsa ntchito webusaitiyi pa zochita zawo zauzimu komanso pophunzira Baibulo monga banja. Malinga ndi chigamulo cha khoti loyamba, zikuonetseratu kuti wina aliyense akadzapezeka akulimbikitsa anthu kugwiritsa ntchito webusaitiyi, adzaimbidwa mlandu. Zimenezi zidzakhudzanso anthu 142 miliyoni okhala m’dziko la Russia kuti asamagwiritse ntchito webusaiti ya jw.org pofufuza mfundo za m’Baibulo. Pofotokoza zokhudza webusaitiyi, pulofesa wina dzina lake, Yekaterina Elbakyan yemwe amaphunzitsa maphunziro a zachipembedzo pa sukulu yina yotchedwa Academy of Labor and Social Relations mumzinda wa Moscow anati: “Webusaiti ya jw.org ndi mphatso kwa aliyense amene akuchita kafukufuku wa za zipembedzo. Ndi yothandiza kwambiri kuti munthu umvetse zinthu zosiyanasiyana. Nkhani zokhudza zinthu zauzimu ndiponso makhalidwe abwino zimafotokozedwa m’njira yosavuta kumva. Ukamagwiritsa ntchito webusaitiyi zimangokhala ngati ukulandiridwa ndi manja awiri m’nyumba ya a Mboni za Yehova.”
Bambo Grigory Martynov omwe ndi mneneri wa Mboni za Yehova m’dziko la Russia, anati: “Webusaiti ya jw.org, ndi yothandiza kwambiri m’dziko lino pofufuza nkhani zokhudza Baibulo ndipo silowerera ndale ngakhale pang’ono kapena kutsatsa malonda. Tikukhulupirira kuti khoti la Tver Regional Court lionetsetsa kuti webusaiti yophunzitsa imeneyi ipitirizabe kuthandiza anthu onse a ku Russia.”
Bambo J. R. Brown omwe ndi mneneri wa Mboni za Yehova kulikulu lawo lapadziko lonse ku New York anati: “Webusaiti ya jw.org ndi yothandiza kwambiri pofufuza nkhani komanso ndi malo amene mabanja padziko lonse angapezepo malangizo othandiza kwabasi. Anthu pafupifupi 900,000 amafufuza zinthu zowathandiza pa webusaitiyi tsiku lililonse m’zinenero 600. Kuletsa webusaitiyi ndi kulakwa kwenikweni.”
Kuchokera m’mayiko ena:
Lankhulani ndi: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000
Russia: Grigory Martynov, tel. +7 812 702 2691