Mavidiyo a M’zinenero Zambiri
A Mboni za Yehova amamasulira mabuku m’zinenero zambiri. Pofika mu November 2014, tinali titamasulira Baibulo m’zinenero 125 komanso mabuku ofotokoza Baibulo m’zinenero 742. Kuonjezera pamenepa, timamasuliranso mavidiyo. Mwachitsanzo, pofika mu January 2015, vidiyo yakuti Kodi pa Nyumbu ya Ufumu Pamachitika zotani? inali itamasuliridwa m’zinenero 398, ndipo vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? inamasuliridwa m’zinenero 569. N’chifukwa chiyani tinachita zimenezi nanga zinatheka bwanji?
Mu March 2014, Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova linauza maofesi a Mboni za Yehova padziko lonse kuti amasulire mavidiyo m’zinenero zambiri n’cholinga chofuna kuthandiza anthu kuphunzira Baibulo.
Kuti ntchito yomasulira vidiyo itheke pamafunika zinthu zingapo. Choyamba, ogwira ntchito yomasulira amafunika kumasulira kaye nkhaniyo. Kenako amapeza anthu amene amayankhula bwino chinenero chimene amasuliracho kuti awerenge mawu a m’vidiyomo. Zikatero, dipatimenti yojambula mavidiyo ndi zinthu zina zomvetsera, imajambula mawu ndi kuwakonza bwinobwino ndiponso kuika mawu oti azidzaoneka, ngati vidiyoyo ili ndi mawu oterowo. Pomaliza amaphatikiza mawu amene ajambulawo ndi zithunzi za m’vidiyomo kuti ikhale vidiyo ya m’chinenero chimene amasuliracho ndipo amaiika pa webusaiti.
Kuti zimenezi zitheke, nthambi zina zinali ndi situdiyo komanso anthu odziwa bwino ntchito imeneyi. Koma mwina tingadabwe kuti zinatheka bwanji kuti mavidiyowa apezekenso m’zinenero zimene zimayankhulidwa komanso kumasuliridwa kumadera omwe kulibe zipangizozi?
A Mboni amene amadziwa ntchitoyi ankatenga makina ojambulira oyenda nawo ndipo ankatumizidwa kumaderawa. Iwo ankakhala ndi kompyuta, zokuzila mawu ndiponso mapulogalamu a pa kompyuta othandiza kujambula mawu. Akatero ankapanga kasitudiyo m’malo ngati Nyumba ya Ufumu kapena m’nyumba ya munthu. A Mboni ena amene amadziwa chinenerocho ankawerenga zimene amasulirazo, kukocha anthu amene akufunika kujambulidwa mawu komanso kutsimikizira kuti zonse zili bwino. Odziwa ntchito yojambula mawu aja akamaliza ndiponso akaona kuti zili bwino, ankapita kudera lina.
Zimenezi zinathandiza kuti mavidiyo ajambulidwe m’zinenero zambiri kusiyana ndi kale lonse.
Anthu akuwakonda kwambiri mavidiyowa ndipo akusangalala. Izi zili choncho chifukwa chakuti mavidiyo athuwa anali oyamba kupezeka m’zinenero za anthu ambiri.
Vidiyo ina inajambulidwa m’chinenero cha Chipitjantjatjara chomwe chimalankhulidwa ndi anthu oposa 2,500. Vidiyoyi anakaijambulira ku Alice Springs komwe ndi kumpoto kwa dziko la Australia. Callan Thomas, yemwe anathandiza nawo pojambula vidiyoyi anati: “Anthu anasangalala kwambiri ndi mavidiyowa. Anthuwa anaikonda kwambiri vidiyoyi moti ankangoionerabe ndipo ankafuna kudziwa kumene angapeze mavidiyo ena. Kulibe mabuku ambiri a Chipitjantjatjara, choncho anthu amadabwa akamva kapena kuonera zinthu za m’chinenero chawochi.”
A Mboni ena awiri ku Cameroon, ankadutsa mumtsinje wina pabwato ndipo anaima pamudzi wotchedwa Pygmy. Iwo anacheza ndi mfumu ya mudziwo yomwe inkagwira ntchito ya uphunzitsi pasukulu ya m’mudzimo. A Mboniwo atazindikira kuti mfumuyo imalankhula Chibasa, anagwiritsa ntchito kachipangizo kamakono poyionetsa vidiyo ya chinenerochi yakuti, N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? Mfumuyo inasangalala kwambiri ndipo inapemphanso mabuku.
M’mudzi wina wa ku Indonesia, mtsogoleri wa chipembedzo china amatsutsa kwambiri a Mboni za Yehova ndipo anawotcha mabuku onse amene a Mboni anagawira anthu m’deralo. Ndipo anthu ena a m’mudziwu anaopseza kuti awotcha Nyumba ya Ufumu. Kenako apolisi anayi anapita kunyumba ya mayi wina wa Mboni kuti akamufunse mafunso pamodzi ndi banja lake. Iwo ankafuna kudziwa zimene zimachitika m’Nyumba ya Ufumu ndipo mayiyu anawaonetsa vidiyo ya m’Chiindoneziya yakuti Kodi pa Nyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani?
Pambuyo poonera vidiyoyi wapolisi mmodzi anati: “Pano ndazindikira kuti anthu sakudziwani bwinobwino ndipo sakumvetsani.” Wapolisi wina anafunsa kuti: “Kodi mungandigawire vidiyoyi kuti ndikasonyeze anzanga ena? Ndaona kuti vidiyoyi ikhoza kuthandiza anthu kukudziwani bwino.” Zimenezi zathandiza kuti apolisi asamadane ndi a Mboni ndipo amawateteza.
Ngati simunaonerepo mavidiyowa, dziwa kuti mukhoza kuwapeza m’chinenero chanu.