NYIMBO 94
Tikuthokoza Mulungu Potipatsa Mawu Ake
Tikuthokoza Mulungu Potipatsa Mawu Ake
-
1. Yehova Atate tikuthokoza
Chifukwa mwatipatsa mawu anu.
Munawauziradi.
Anatimasula.
Kuwala kwake kwatipatsa nzeru.
-
2. Mawu anu onse ndi a mphamvudi.
Amatithandiza kusankha bwino
Ndiponso zigamulo
Zanu n’zolondola.
Mfundo zanu zimatitsogolera.
-
3. Mawu anu amatikhudza mtima.
Aneneri ankakhulupirira,
Nafe tithandizeni
Tikhulupirire.
Tikuthokoza mwatipatsa mawu.
(Onaninso Sal. 19:9; 119:16, 162; 2 Tim. 3:16; Yak. 5:17; 2 Pet. 1:21.)