Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 46

Tikukuthokozani Yehova

Tikukuthokozani Yehova

(1 Atesalonika 5:​18)

  1. 1. Tikukuthokozanitu Yehova.

    Mumatipatsa kuwala kwanu.

    Tikuthokoza mwayi wa pemphero

    Kuti tinene mavuto athu.

  2. 2. Tikuthokoza potumiza Yesu

    Amene anagonjetsa dziko.

    Tikuthokozanso potithandiza

    Kukwanitsa malonjezo athu.

  3. 3. Tikuthokoza chifukwa cha mwayi

    Wolalikira za dzina lanu.

    Tikuthokoza kuti posachedwa

    Mavuto onsewa adzathadi.