Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 145

Mulungu Watilonjeza Paradaiso

Mulungu Watilonjeza Paradaiso

(Luka 23:43)

  1. 1. M’lungu wathu watilonjeza

    Madalitso posachedwa.

    Adzachotsa uchimo, imfa,

    Misozi ndi zopweteka.

    (KOLASI)

    Ndiye tidikirirebe

    Ndipo tikhulupirire.

    Khristu adzakwaniritsa

    Chifuniro cha Mulungu.

  2. 2. Cholinga cha Mulungu n’choti

    Adzaukitse akufa.

    ‘Udzakhala m’Paradaiso,’

    N’zomwe Yesu ananena.

    (KOLASI)

    Ndiye tidikirirebe

    Ndipo tikhulupirire.

    Khristu adzakwaniritsa

    Chifuniro cha Mulungu.

  3. 3. Tidzakhala m’Paradaiso,

    Yesu ndiye Mfumu yathu.

    Tithokoze Atate wathu

    Kuchokera mumtimamu.

    (KOLASI)

    Ndiye tidikirirebe

    Ndipo tikhulupirire.

    Khristu adzakwaniritsa

    Chifuniro cha Mulungu.